bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 14
Zechariah 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
1
Onani, tsiku likubwera, la Chauta, pamene zinthu zomwe adani ako adakulanda, azidzagaŵana iwe uli pomwepo.
2
Chauta adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu. Adzaulanda mzindawo ndi kuphwasula nyumba zonse, ndipo akazi am'menemo adzaŵachita chigololo. Theka la anthu a mu mzindawo lidzatengedwa ukapolo, koma ena onse otsala mumzindamo sadzachotsedwa.
3
Pambuyo pake Chauta adzabwera kudzamenyana ndi adani amenewo, monga m'mene amachitira pa tsiku la nkhondo.
4
Tsiku limenelo adzaimirira pa phiri la Olivi loyang'anana ndi Yerusalemu chakuvuma, ndipo phirilo lidzagaŵika paŵiri ndi chigwa chachikulu choyenda kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Theka la phiri lidzasunthira chakumpoto, theka lina chakumwera.
5
Inu mudzapulumuka podzera m'chigwa chimenecho cha pakati pa mapiri. Mudzathaŵa monga m'mene mudaathaŵira nthaŵi ija ya chivomezi pa nthaŵi ya Uziya mfumu ya ku Yuda. Kenaka Chauta, Mulungu wanu, adzabwera pamodzi ndi oyera ake onse.
6
Tsiku limenelo sikudzatentha, sikudzazizira ndipo sikudzachita chisanu chambee.
7
Lidzakhala tsiku la kuŵala kokhakokha, osakhala usana, osakhala usiku, chifukwa ndi madzulo omwe kuzidzaŵalabe. Tsiku limene zidzachitike zimenezi ndi Chauta yekha akulidziŵa.
8
Tsiku limenelo madzi a moyo adzatuluka ku Yerusalemu. Theka la madziwo lidzathira m'nyanja yakuvuma, theka lina lidzathira m'nyanja yakuzambwe. Zimenezi zidzachitika pa nthaŵi yachilimwe ndi yachisanu yomwe.
9
Tsono Chauta adzakhala mfumu ya dziko lonse lapansi. Tsiku limenelo Chauta yekha anthu onse adzampembedza, adzamdziŵa ndi dzina lake limodzi lokhalo.
10
Dziko lonse adzalisalaza kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu. Koma Yerusalemu adzakwezedwa pamalo pakepo, kuyambira ku chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene kunali chipata chakale mpaka ku chipata chapangodya, ndiponso kuchokera ku Nsanja ya Hananele mpaka ku malo opondera mphesa za mfumu.
11
Anthu adzakhala ku Yerusalemu mwamtendere, poti sadzaopsezedwanso ndi chiwonongeko kumeneko.
12
Pambuyo pake Chauta adzalanga ndi mliri adani onse amene ankamenyana nkhondo ndi Yerusalemu. Matenda ake adzakhala motere: matupi ao adzaola eni ake akuyendabe, maso ao adzaola ali chikhalire m'malo mwake, ndipo malilime ao adzaola m'kamwa mwao.
13
Pa tsiku limenelo Chauta adzasokoneza anthu ndi mantha aakulu, mpaka aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndipo adzayamba kumenyana okhaokha.
14
Nawonso anthu a ku Yuda adzachita nkhondo ku Yerusalemu. Ndipo chuma cha anthu a mitundu yozungulira adzachisonkhanitsa pamodzi. Chuma chake ndi golide ndi siliva wambiri ndiponso zovala zochuluka.
15
Mliri uja udzaphanso akavalo, ngamira ndi abulu a mitundu yonse, ndiponso nyama zonse zokhala ku zithando zankhondo.
16
Zitatha zimenezi anthu onse otsala mwa adani amene ankamenyana ndi Yerusalemu, azidzabwera chaka ndi chaka kudzapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, ndiponso kudzachita chikondwerero chamisasa.
17
Ngati mabanja ena pa dziko lapansi sadzapita ku Yerusalemu kukapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, mvula sidzaŵagwera.
18
Ngati anthu a ku Ejipito sadzapita kukaonekera kumeneko, adzalandiranso chilango chonga chomwe Chauta adzalange nacho mtundu wina uliwonse wa anthu osapita kukachita chikondwerero chamisasa.
19
Chimenechi ndicho chidzakhale chilango cha Aejipito ndiponso cha mtundu uliwonse wa anthu amene sadzachita nao chikondwerero chamisasacho.
20
Pa tsiku limenelo pa mabelu ovala akavalo ankhondo padzalembedwa mau akuti, “Woperekedwa kwa Chauta.” Ndipo mbiya za ku Nyumba ya Chauta nazonso zidzakhala zoyera ngati mbale zakuguwa.
21
Mbiya iliyonse ya ku Yerusalemu ndi ku Yuda idzakhala yoperekedwa kwa Chauta Wamphamvuzonse. Onse opereka nsembe ku Yerusalemu adzagwiritsa ntchito mbiyazo pophika nyama za nsembe. Nthaŵi imeneyo ikadzafika, sipadzaonekanso wamalonda aliyense m'Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14