bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 9
Zechariah 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 10 →
1
Mau a Chauta akudzudzula dziko la Hadaraki, ndiponso mzinda wa Damasiko. Paja mizinda yonse ya ku Aramu njake ya Chauta, chimodzimodzi ngati mafuko onse a Aisraele.
2
Ndi wa Chautanso mzinda wa Hamati, umene ukuchitana malire ndi maikowo, chimodzimodzinso Tiro ndi Sidoni ngakhale ndi anzeru kwambiri.
3
Tiro adadzimangira linga. Adaunjika siliva ngati dothi, adakundika golide ngati chifwilimbwiti cham'miseu.
4
Koma taimani, Chauta adzamlanda chuma chonsechi, adzachitaya m'nyanja, iyeyo adzapserera ndi moto.
5
Mzinda wa Asikeloni nawonso udzaziwona zimenezo, nkuchita mantha. Gaza adzakhwinyata ndi mantha, Ekeroninso chimodzimodzi, chifukwa zimene ankayembekeza zidzasokonezeka. Mfumu ya ku Gaza idzachotsedwa, ku Asikeloni kudzakhala kopanda anthu.
6
Ku Asidodi kudzakhala anthu achimsakaniza. Chauta akuti, “Ndidzathetsa kunyada kwa Filistiya.
7
Anthu ake sadzadyanso nyama yamagazi, kapena nyama yoletsedwa iliyonse. Otsala onse adzakhala anthu anga, adzasanduka ngati fuko la ku Yuda. Nawonso Aekeroni adzakhala ngati Ayebusi.
8
Pamenepo Ine ndidzakhala mlonda wa dziko langalo, kuti wina asamadutsepo kapena kuloŵamo. Palibe adani amene adzaŵapambane, pakuti zimenezi ndikuzisamala Ine ndemwe.”
9
Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni. Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu. Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu. Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu, bulu wake kamwana tsono.
10
Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efuremu ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu. Uta wankhondo adzauthyola. Mfumu yanu idzachititsa mtendere pakati pa mitundu yonse ya anthu. Adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, ndiponso kuchokera ku Mtsinje wa Yufurate mpaka ku mathero a dziko lapansi.
11
Chauta akuti, “Tsono kunena za inu, chifukwa cha chipangano changa ndi inu, chimene nsembe zamagazi zidachitsimikiza, ndidzaŵatulutsa m'dzenje lopanda madzi anthu anu amene ali ngati akapolo.
12
Bwererani ku linga lanu lolimba, inu akapolo amene tsopano muli ndi chikhulupiriro. Lero ndi tsiku limene ndikulengeza kuti ndidzakubwezerani zabwino moŵirikiza.
13
“Ndidzakoka Yuda ngati uta wanga, Efuremu adzakhala ngati muvi wake. Ndidzatenga ana ako, iwe Ziyoni, kuti alimbane ndi ana ako, iwe Grisi; ndidzakugwira ngati lupanga la wankhondo wamphamvu.”
14
Tsono Chauta adzaonekera anthu ake, ndipo mivi yake adzaiponya ngati zing'aning'ani. Ambuye Chauta adzaliza lipenga, ndipo adzayenda m'kamvulumvulu wochokera kumwera.
15
Chauta Wamphamvuzonse adzakhala chishango chao. Iwowo adzapambana ndi kugonjetsa adani ao poponya miyala chabe. Adzamwa magazi ao nkumafuula ngati okhuta vinyo. Magaziwo adzachita kuyenderera ngati magazi a nsembe, othira ndi mkhate pa guwa popembedza.
16
Tsiku limenelo Chauta, Mulungu wao, adzaŵapulumutsa, pakuti anthu akewo ali ngati nkhosa. M'dziko laolo anthuwo adzakhala onyezimira ngati miyala ya mtengo wapatali ya pa chisoti chaufumu.
17
Dzikolo lidzakhaladi lokongola kwambiri. Tirigu adzalimbitsa anyamata, ndipo vinyo watsopano adzakometsa anamwali.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14