bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 10
2 Chronicles 10
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 11 →
1
Ndipo Rehobowamu anamuka ku Sekemu; pakuti Aisraele onse adadza ku Sekemu kumlonga ufumu.
2
Ndipo kunali, atamva Yerobowamu mwana wa Nebati (popeza anali m'Ejipito kumene adathawira, kuthawa Solomoni mfumu), Yerobowamu anabwera kuchoka ku Ejipito.
3
Ndipo anatuma munthu kukamuitana, nadza Yerobowamu ndi Aisraele onse, nalankhula ndi Rehobowamu, ndi kuti,
4
Atate wanu analemeretsa goli lathu; inu tsono pepuzaniko ntchito yolemetsa ya atate wanu, ndi goli lake lolemera anatisenzetsali, ndipo tidzakutumikirani.
5
Ndipo ananena nao, Mubwerenso atapita masiku atatu. Nachoka anthu.
6
Ndipo Rehobowamu mfumu anafunsana ndi akuluakulu, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake akali ndi moyo, nati, Mundipangire bwanji, kuti ndiwabwezere mau anthu awa?
7
Ndipo ananena naye, kuti, Mukawachitira chokoma anthu awa, ndi kuwakonda, ndi kulankhula nao mau okoma, adzakhala anyamata anu kosatha.
8
Koma analeka uphungu wa akulu akuluwa adampangirawo, nakafunsana ndi anyamata anakula naye pamodzi, oimirira pamaso pake.
9
Nati nao, Mundipangire bwanji inu, kuti tibwezere mau anthu awa ananena nanewo, ndi kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenzetsa ife?
10
Ndipo anyamatawo adakula naye pamodzi ananena naye, ndi kuti, Muzitero nao anthu awa adalankhula nanu, ndi kuti, Atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire ilo; muzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'chuuno mwa atate wanga.
11
Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
12
Tsono Yerobowamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu tsiku lachitatu, monga mfumu idanena, ndi kuti Bweraninso kwa ine tsiku lachitatu.
13
Ndipo mfumu inawayankha mokalipa, popeza mfumu Rehobowamu analeka uphungu wa akuluakulu,
14
nalankhula nao monga umo anampangira achinyamata, ndi kuti, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
15
Momwemo mfumu siinamvera anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ake, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati.
16
Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu sinawamvera anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu, Aisraele inu; yang'anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisraele onse anamuka ku mahema ao.
17
Koma za ana a Israele okhala m'midzi ya Yuda, Rehobowamu anakhalabe mfumu yao.
18
Pamenepo Rehobowamu mfumu inatuma Hadoramu woyang'anira thangata; koma ana a Israele anamponya miyala, nafa. Ndipo Rehobowamu mfumu anafulumira kukwera pa galeta wake kuthawira ku Yerusalemu.
19
Motero Israele anapandukana nayo nyumba ya Davide mpaka lero lino.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36