bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 31
2 Chronicles 31
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 32 →
1
Chitatha ichi chonse tsono, Aisraele onse opezekako anatuluka kunka kumidzi ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe m'Yuda monse, ndi m'Benjamini, m'Efuremunso, ndi m'Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israele anabwerera, yense kudziko lake ndi kumidzi yao.
2
Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wake, ndi ansembe ndi Alevi, achite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, kuzipata za chigono cha Ambuye.
3
Naikanso gawo la mfumu lotapa pa chuma chake la nsembe zopsereza, ndilo la nsembe zopsereza za m'mawa ndi madzulo, ndi la nsembe zopsereza za masabata, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika, monga mulembedwa m'chilamulo cha Yehova.
4
Anauzanso anthu okhala m'Yerusalemu apereke gawo la ansembe ndi Alevi, kuti iwowa alimbike m'chilamulo cha Yehova.
5
Ndipo pobuka mau aja, ana a Israele anapereka mochuluka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uchi, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mochuluka.
6
Ndi ana a Israele ndi Yuda okhala m'midzi ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng'ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyulumiyulu.
7
Mwezi wachitatu anayamba kuika miyalo ya miyuluyi, naitsiriza mwezi wachisanu ndi chiwiri.
8
Ndipo pamene Hezekiya ndi akulu ake anadza, naona miyuluyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ake Aisraele.
9
Pamenepo Hezekiya anafunsana ndi ansembe ndi Alevi za miyuluyi.
10
Ndipo Azariya wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki anamyankha, nati, Chiyambire anthu anabwera nazo zopereka kunyumba ya Yehova, tadya, takhuta, ndipo zitatsalira zambiri; pakuti Yehova anadalitsa anthu ake; ndipo siuku kuchuluka kwa chotsala.
11
Pamenepo Hezekiya anawauza akonze zipinda m'nyumba ya Yehova; nazikonza.
12
Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkulu woyang'anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng'ono wake ndiye wotsatana naye.
13
Ndi Yehiyele, ndi Azaziya, ndi Nahati, ndi Asahele, ndi Yerimoti, ndi Yozabadi, ndi Eliyele, ndi Isimakiya, ndi Mahati, ndi Benaya, ndiwo akapitao omvera Konaniya ndi Simei mng'ono wake, oikidwa ndi Hezekiya mfumu ndi Azariya mkulu wa kunyumba ya Mulungu.
14
Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri.
15
Ndi omvera iye ndiwo Edeni, ndi Miniyamini, ndi Yesuwa, ndi Semaya, Amariya ndi Sekaniya, m'midzi ya ansembe, kugawira abale ao m'zigawo zao mokhulupirika, akulu monga ang'ono;
16
pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa aliyense amene adalowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa ntchito yake pa tsiku lake, kukachita za utumiki wao m'udikiro wao monga mwa zigawo zao;
17
ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu m'udikiro mwao, monga mwa zigawo zao;
18
ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ana ao ang'ono onse, akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi, mwa msonkhano wonse; pakuti m'kukhulupirika kwao anadzipatula akhale opatulika;
19
panalinso amuna mwa ana a Aroni ansembe, okhala m'minda ya kubusa kwa midzi yao, m'mudzi uliwonse, otchulidwa maina ao, agawire amuna onse mwa ansembe, ndi onse mwa Alevi, oyesedwa mwa chibadwidwe magawo ao.
20
Momwemo anachita Hezekiya mwa Yuda lonse nachita chokoma, ndi choyenera, ndi chokhulupirika, pamaso pa Yehova Mulungu wake.
21
Ndipo m'ntchito iliyonse anaiyamba m'utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi m'chilamulo, ndi m'mauzo, kufuna Mulungu wake, anachita ndi mtima wake wonse, nalemerera nayo.
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36