bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 24
2 Chronicles 24
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 25 →
1
Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la make ndiye Zibiya wa ku Beereseba.
2
Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe.
3
Ndipo Yehoyada anamtengera akazi awiri, nabala ana aamuna ndi aakazi.
4
Ndipo pambuyo pake mumtima mwa Yowasi munali chofuna kukonzanso nyumba ya Yehova.
5
Nasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, nanena nao, Mutuluke kunka kumidzi ya Yuda, ndi kusonkhanitsa kwa Aisraele onse ndalama zakukonzetsa nyumba ya Mulungu wanu chaka ndi chaka; ndipo inu fulumirani nayo ntchitoyi. Koma Alevi sanafulumire nayo.
6
Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkulu wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kuchokera m'Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israele, ukhale wa chihema cha umboni?
7
Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola chitseko cha nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwa Baala.
8
Nilamulira mfumu, ndipo anapanga bokosi, naliika kunja kuchipata cha nyumba ya Yehova.
9
Nalalikira mwa Yuda ndi Yerusalemu, abwere nao kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu anauikira Aisraele m'chipululu.
10
Ndipo akalonga onse ndi anthu onse anakondwera, nabwera nazo, naponya m'bokosi mpaka atatha.
11
Ndipo kunali, pamene amabwera nalo bokosi alipenye mfumu, mwa manja a Alevi, nakapenya kuti ndalama zinachulukamo, amadza mlembi wa mfumu, ndi kapitao wa wansembe wamkulu, nakhuthula za m'bokosi, nalisenza ndi kubwera nalo kumalo kwake. Anatero tsiku ndi tsiku, nasonkhanitsa ndalama zochuluka.
12
Ndipo mfumu ndi Yehoyada anazipereka kwa iwo akugwira ntchito ya utumiki ya nyumba ya Yehova, nalembera amisiri omanga ndi miyala, ndi osema mitengo, akonzenso nyumba ya Yehova; ndiponso akuchita ndi chitsulo ndi mkuwa alimbitse nyumba ya Yehova.
13
Momwemo anachita ogwira ntchito, nikula ntchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ake, nailimbitsa.
14
Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golide ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.
15
Koma Yehoyada anakalamba, nachuluka masiku, namwalira iye; ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi atatu pamene anamwalira.
16
Ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anachita zabwino m'Israele, ndi kwa Mulungu, ndi kunyumba yake.
17
Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera.
18
Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, chifukwa cha kupalamula kwao kumene.
19
Koma Iye anawatumira aneneri kuwabwezeranso kwa Yehova, ndiwo anawachitira umboni; koma sanawamvere.
20
Ndipo mzimu wa Mulungu unavala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.
21
Koma anampangira chiwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m'bwalo la nyumba ya Yehova.
22
Motero mfumu Yowasi sanakumbukire zokoma anamchitirazi Yehoyada atate wake, koma anapha mwana wake; ndiye pomwalira anati, Yehova achipenye, nachifunse.
23
Ndipo kunachitika, podzanso nyengoyi khamu la nkhondo la Aaramu linamkwerera, nafika iwo ku Yuda ndi Yerusalemu, naononga mwa anthu akalonga onse a anthu, natumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko.
24
Pakuti khamu la nkhondo la Aaramu linadza la anthu owerengeka; ndipo Yehova anapereka khamu lalikulu m'dzanja lao; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Motero anachitira Yowasi zomlanga.
25
Ndipo atamchokera (popeza anamsiya wodwala nthenda zazikulu), anyamata ake anamchitira chiwembu, chifukwa cha mwazi wa ana a Yehoyada wansembe, namupha pakama pake, namwalira iye; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma osamuika m'manda a mafumu.
26
Omchitira chiwembu ndi awa: Zabadi, mwana wa Simeati wamkazi Mwamoni; ndi Yehozabadi, mwana wa Simiriti wamkazi Mmowabu.
27
Za ana ake tsono, ndi katundu wamkulu anamsenza, ndi kumanganso kwa nyumba ya Mulungu, taonani, zilembedwa m'buku lomasulira la mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36