bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 34
2 Chronicles 34
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 35 →
1
Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi atatu mphambu chimodzi.
2
Nachita zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira za Davide kholo lake, osapatuka kudzanja lamanja kapena kulamanzere.
3
Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake; ndipo atakhala zaka khumi ndi chimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzichotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga.
4
Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pake; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe.
5
Napsereza mafupa a ansembe pa maguwa a nsembe ao, nayeretsa Yuda ndi Yerusalemu.
6
Nateronso m'midzi ya Manase, ndi Efuremu, ndi Simeoni, mpaka Nafutali, m'mabwinja mwao mozungulira.
7
Nagumula maguwa a nsembe, naperapera zifanizo ndi mafano osema, nalikha mafano a dzuwa onse m'dziko lonse la Israele, nabwerera kunka ku Yerusalemu.
8
Atakhala mfumu tsono zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri, atayeretsa dziko ndi nyumbayi, anatuma Safani mwana wa Azaliya, ndi Maaseiya kazembe wa mudzi, ndi Yowa mwana wa Yehowahazi wolemba mbiri, akonze nyumba ya Yehova Mulungu wake.
9
Ndipo anadza kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, napereka ndalama adabwera nazo kunyumba ya Mulungu, zimene Alevi osunga pakhomo adasonkhanitsa kuzilandira kudzanja la Manase ndi Efuremu, ndi kwa otsala onse a Israele, ndi kwa Yuda yense, ndi Benjamini, ndi kwa okhala m'Yerusalemu.
10
Ndipo anazipereka m'dzanja la antchito oikidwa ayang'anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa antchito akuchita m'nyumba ya Yehova kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi;
11
anazipereka kwa amisiri a mitengo ndi omanga nyumba, agule miyala yosema, ndi mitengo ya mitanda yam'mwamba ndi yammunsi ya nyumbazi, adaziononga mafumu a Yuda.
12
Ndipo amunawo anachita ntchitoyi mokhulupirika; ndi oikidwa awayang'anire ndiwo Yahati ndi Obadiya, Alevi, a ana a Merari; ndi Zekariya ndi Mesulamu, a ana a Akohati, kuifulumiza; ndi Alevi ena aliyense waluso la zoimbira.
13
Anayang'aniranso osenza akatundu, nafulumiza onse akugwira ntchito ya utumiki uliwonse; ndi mwa Alevi munali alembi, ndi akapitao, ndi odikira.
14
Ndipo pakutulutsa ndalama zimene adalowa nazo kunyumba ya Yehova, Hilikiya wansembe anapeza buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.
15
Ndipo Hilikiya anayankha nati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m'nyumba ya Yehova. Hilikiya napereka buku kwa Safani.
16
Ndi Safani anamuka nalo buku kwa mfumu, nabwezeranso mau kwa mfumu, ndi kuti, Zonse mudazipereka kwa anyamata anu alikuzichita.
17
Nakhuthula ndalama zinapezeka m'nyumba ya Yehova, nazipereka m'manja a akapitao ndi m'manja a antchito.
18
Ndipo Safani mlembi anauza mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe anandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.
19
Ndipo kunali, atamva mfumu mau a chilamulo, anang'amba zovala zake.
20
Mfumu niuza Hilikiya, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Abidoni mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,
21
Mukani, mundifunsire kwa Yehova, ine ndi otsala m'Israele ndi Yuda, za mau a m'buku lopezekalo; pakuti ukali wa Yehova atitsanulirawu ndi waukulu; popeza makolo athu sanasunge mau a Yehova kuchita monga mwa zonse zolembedwa m'bukumu.
22
Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulida mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira wosunga zovala, amene anakhala m'Yerusalemu m'dera lachiwiri, nanena naye mwakuti.
23
Ndipo iye ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine,
24
Atero Yehova, Taonani, ndifikitsira malo ano ndi anthu okhala m'mwemo choipa, ndicho matemberero onse olembedwa m'buku adaliwerenga pamaso pa mfumu ya Yuda;
25
chifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika.
26
Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero kwa iye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kunena za mau udawamva,
27
popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ake otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzichepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zovala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.
28
Taona, ndidzakusonkhanitsa kumakolo ako, nudzaikidwa kumanda kwako mumtendere, ndi maso ako sadzapenya zoipa zonse ndidzafikitsira malo ano ndi okhala m'mwemo. Ndipo anambwezera mfumu mau.
29
Pamenepo mfumu inatumiza anthu, nisonkhanitsa akuluakulu onse a Yuda ndi Yerusalemu.
30
Nikwera mfumu kunyumba ya Yehova ndi amuna onse a m'Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu, ndi ansembe ndi Alevi, ndi anthu onse akulu ndi ang'ono; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.
31
Ndipo mfumu inaimirira pokhala pake, nichita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda chotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, kuchita mau a chipangano olembedwa m'bukumu.
32
Naimiritsapo onse okhala m'Yerusalemu ndi m'Benjamini. Ndipo okhala m'Yerusalemu anachita monga mwa chipangano cha Mulungu, Mulungu wa makolo ao.
33
Yosiya nachotsa zonyansa zonse m'maiko onse okhala a ana a Israele, natumikiritsa onse opezeka m'Israele, inde kutumikira Yehova Mulungu wao. Masiku ake onse iwo sanapatuke kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo ao.
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36