bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 8
2 Chronicles 8
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 9 →
1
Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni anamanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba yakeyake,
2
Solomoni anamanga midzi imene Huramu adampatsa, nakhalitsamo ana a Israele.
3
Ndipo Solomoni anamuka ku Hamatizoba, naugonjetsa.
4
Ndipo anamanga Tadimori m'chipululu, ndi midzi yonse yosungiramo chuma, imene anaimanga m'Hamati.
5
Anamanganso Betehoroni wa kumtunda, ndi Betehoroni wa kunsi, midzi ya malinga yokhala nao malinga, zitseko, ndi mipiringidzo;
6
ndi Baalati, ndi midzi yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi midzi yonse ya magaleta ake, ndi midzi ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa m'Yerusalemu, ndi m'Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.
7
Ndipo anthu onse otsala mwa Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, osati Aisraele,
8
mwa ana ao otsala m'dziko pambuyo pao, amene ana a Israele sanawathe, mwa iwowa Solomoni anawachititsa thangata mpaka lero lino.
9
Koma mwa ana a Israele Solomoni sanawayese akapolo omgwirira ntchito; koma iwowa anali anthu a nkhondo, akazembe ake akulu, ndi akulu a magaleta ake, ndi apakavalo ake.
10
Amenewa anali akulu a akapitao a mfumu Solomoni, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu akulamulira anthu.
11
Ndipo Solomoni anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mudzi wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.
12
Pamenepo Solomoni anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe la Yehova, limene adalimanga pakhomo pachipinda cholowera,
13
monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m'chaka, pa zikondwerero za Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa zikondwerero za Masabata, ndi pa zikondwerero za Misasa.
14
Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.
15
Ndipo sanapatuke pa lamulo la mfumu la kwa ansembe ndi Alevi, kunena za kanthu kalikonse, kapena za chumachi.
16
Momwemo ntchito yonse ya Solomoni inakonzekeratu tsiku lakuika maziko a nyumba ya Yehova, mpaka anaitsiriza.
17
Pamenepo Solomoni anamuka ku Eziyoni-Gebere, ndi ku Eloti m'mphepete mwa nyanja, m'dziko la Edomu.
18
Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amalinyero ake, ndi anyamata akudziwa za m'nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomoni ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golide, nabwera nao kwa Solomoni mfumu.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36