bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 21
2 Chronicles 21
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 22 →
1
Ndipo Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide; ndi Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
2
Ndipo anali nao abale ake, ana a Yehosafati, Azariya, ndi Yehiyele, ndi Zekariya, ndi Azariya, ndi Mikaele, ndi Sefatiya, onsewa ndiwo ana a Yehosafati mfumu ya Israele.
3
Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikulu, zasiliva, ndi zagolide, ndi za mtengo wake, pamodzi ndi midzi yamalinga m'Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wake woyamba.
4
Atauka tsono Yehoramu m'ufumu wa atate wake, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ake onse, ndi akalonga ena omwe a Israele.
5
Yehoramu anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nachita ufumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu.
6
Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, umo mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wake; ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova.
7
Koma Yehova sanafune kuononga nyumba ya Davide chifukwa cha pangano adalichita ndi Davide, ndi monga adalonjeza kumpatsa iye ndi ana ake nyali nthawi zonse.
8
Masiku ake Aedomu anapanduka kuchoka m'dzanja la Yuda, nadziponyera okha mfumu.
9
Ndipo Yehoramu anaoloka, ndi akazembe ake, ndi magaleta ake onse pamodzi naye, nauka usiku, nakantha Aedomu omzinga ndi akapitao a magaleta.
10
Chinkana anatero, Aedomu anapanduka kupulumuka m'dzanja la Yuda mpaka lero lino; nthawi yomweyo anapanduka Alibina kupulumuka m'dzanja lake; chifukwa adasiya Yehova Mulungu wa makolo ake.
11
Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nachititsa okhala m'Yerusalemu chigololo, nakankhirako Ayuda.
12
Ndipo anamdzera kalata wofuma kwa Eliya mneneri, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Davide atate wanu, Popeza simunayenda m'njira za Yehosafati atate wanu, kapena m'njira za Asa mfumu ya Yuda,
13
koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israele, ndi kuchititsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu chigololo, monga umo anachitira chigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;
14
taonani, Yehova adzakantha anthu anu, ndi ana anu, ndi akazi anu, ndi chuma chanu chonse, makanthidwe akulu;
15
ndipo mudzadwala kwakukulu nthenda yamatumbo, mpaka matumbo anu adzatuluka chifukwa cha nthendayi tsiku ndi tsiku.
16
Ndipo Yehova anautsira Yehoramu mzimu wa Afilisti, ndi wa Aarabu okhala pambali pa Akusi;
17
ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda chuma chonse chinapezeka m'nyumba ya mfumu, ndi ana ake omwe, ndi akazi ake, osamsiyira mwana, koma Yehowahazi yekha mwana wake wamng'ono.
18
Ndi pambuyo pake pa izi zonse Yehova anamdwalitsa m'matumbo ake ndi nthenda yosachira nayo.
19
Ndipo kunali, itapita nthawi, pakutha pake pa zaka ziwiri, anatuluka matumbo ake mwa nthenda yake namwalira nazo nthenda zoipa. Ndipo anthu ake sanampserezere zonunkhira, monga umo anapserezera makolo ake.
20
Anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu, namuka wopanda wina womlakalaka; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma si m'manda a mafumu ai.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36