bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 4
2 Chronicles 4
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 5 →
1
Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono khumi.
2
Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wake mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizunguniza.
3
Ndi pansi pake panali mafaniziro a ng'ombe zakulizinga, khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pake. Ng'ombe zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.
4
Linasanjikika pa ng'ombe khumi ndi ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, ndi zitatu zinapenya kumadzulo, ndi zitatu zinapenya kumwera, ndi zitatu zinapenya kum'mawa; ndi thawale linasanjikika pamwamba pao, ndi nkholo zao zinayang'anana.
5
Ndi kuchindikira kwake kunanga chikhato, ndi mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati luwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi zitatu.
6
Anapanganso mbiya zaphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo.
7
Ndipo anapanga zoikapo nyali khumi zagolide, monga mwa ziweruzo chake; naziika m'Kachisi, zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere.
8
Anapanganso magome khumi, nawaika m'Kachisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolide.
9
Anamanganso bwalo la ansembe, ndi bwalo lalikulu, ndi zitseko za kubwalo, nakuta zitseko zake ndi mkuwa.
10
Ndipo anaika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum'mawa chakumwera.
11
Ndipo Huramu anapanga miphika, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake. Natsiriza Huramu ntchito adaichitira mfumu Solomoni m'nyumba ya Mulungu:
12
nsanamira ziwiri, ndi zikhozo, ndi mitu iwiri inali pamwamba pa nsanamirazo, ndi maukonde awiri akukuta zikho ziwiri za mitu ili pamwamba pa nsanamirazo,
13
ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwa; mizere iwiri ya makangaza ya ukonde uliwonse, akukuta zikho ziwiri za mitu, inali pa nsanamirazo.
14
Anapanganso maphaka, napanga mbiya zaphwamphwa khumi pamwamba pa maphaka;
15
thawale limodzi ndi ng'ombe khumi ndi ziwiri pansi pake.
16
Miphika yomwe, ndi zoolera, ndi mitungo, ndi zipangizo zake zonse, Huramuabi anazipangira mfumu Solomoni, kuzipangira nyumba ya Yehova, za mkuwa wonyezimira.
17
Mfumuyi inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zereda.
18
Ndipo Solomoni anazipanga zipangizo izi zonse zochulukadi, pakuti kulemera kwake kwa mkuwa sikunayeseka.
19
Solomoni anapanganso zipangizo zonse zinali m'nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolide lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera;
20
ndi zoikapo nyali ndi nyali zake za golide woona, zakuunikira monga mwa chilangizo chake chakuno cha chipinda chamkati;
21
ndi maluwa, ndi nyali, ndi mbano zagolide, ndiwo golide wangwiro;
22
ndi zozimira nyali, ndi mbale zowazira, ndi zipande, ndi mbale za zofukiza za golide woona; ndi kunena za polowera m'nyumba, zitseko zake za m'katimo za malo opatulika kwambiri, ndi zitseko za nyumbayi, ndiyo Kachisi, zinali zagolide.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36