bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 11
2 Chronicles 11
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 12 →
1
Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehobowamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisraele kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu.
2
Koma mau a Yehova anadza kwa Semaya munthu wa Mulunguyo, ndi kuti,
3
Lankhula ndi Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda ndi Benjamini, ndi kuti,
4
Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense kunyumba yake; pakuti chinthu ichi chifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobowamu.
5
Ndipo Rehobowamu anakhala m'Yerusalemu, namanga midzi yolimbikiramo m'Yuda.
6
Anamangadi Betelehemu, ndi Etamu, ndi Tekowa,
7
ndi Betezuri, ndi Soko, ndi Adulamu,
8
ndi Gati, ndi Maresa, ndi Zifi,
9
ndi Adoraimu, ndi Lakisi, ndi Azeka,
10
ndi Zora, ndi Ayaloni, ndi Hebroni; ndiyo midzi yamalinga ya m'Yuda ndi Benjamini.
11
Ndipo analimbitsa malingawo, naikamo atsogoleri, ndi chakudya chosungikiratu, ndi mafuta, ndi vinyo.
12
Ndi m'midzi iliyonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa chilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ake.
13
Ndipo ansembe ndi Alevi okhala m'Israele lonse anadziphatikiza kwa iye, ochokera m'malire ao onse.
14
Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko aoao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobowamu ndi ana ake anawataya, kuti asachitire Yehova ntchito ya nsembe;
15
nadziikira ansembe a misanje, ndi a ziwanda, ndi a anaang'ombe adawapanga.
16
Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m'mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.
17
Momwemo analimbikitsa ufumu wa Yuda, nalimbikitsa Rehobowamu, mwana wa Solomoni zaka zitatu; pakuti anayenda m'njira ya Davide ndi Solomoni zaka zitatu.
18
Ndipo Rehobowamu anadzitengera mkazi Mahalati, mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide, ndi wa Abihaili mwana wamkazi wa Eliyabu mwana wa Yese;
19
ndipo anambalira ana, Yeusi, ndi Semariya, ndi Zahamu.
20
Ndi pambuyo pake anatenga Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu; ndipo anambalira Abiya, ndi Atai, ndi Ziza, ndi Selomiti.
21
Ndipo Rehobowamu anakonda Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu koposa akazi ake onse, ndi akazi ake ang'ono (pakuti adatenga akazi khumi mphambu asanu ndi atatu, ndi akazi aang'ono makumi asanu ndi limodzi, nabala ana amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu, ndi ana akazi makumi asanu ndi limodzi).
22
Ndipo Rehobowamu anaika Abiya mwana wa Maaka akhale wamkulu, kalonga mwa abale ake; ndiko kuti adzamlonga ufumu.
23
Ndipo anachita mwanzeru, nabalalitsa ana ake amuna onse m'maiko onse a Yuda ndi Benjamini, kumidzi yonse yamalinga; nawapatsa chakudya chochuluka, nawafunira akazi ochuluka.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36