bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 13
2 Chronicles 13
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 14 →
1
Ndipo chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yerobowamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda.
2
Anakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zitatu; ndi dzina la make ndiye Mikaya mwana wamkazi wa Uriyele wa ku Gibea. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.
3
Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobowamu atandandalitsa nkhondo yake ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.
4
Ndipo Abiya anaimirira pa phiri la Zemaraimu, ndilo ku mapiri a Efuremu, nati, Mundimvere Yerobowamu ndi Aisraele onse;
5
simudziwa kodi kuti Yehova Mulungu wa Israele anapereka chiperekere ufumu wa Israele kwa Davide, kwa iye ndi ana ake, ndi pangano lamchere?
6
Koma Yerobowamu mwana wa Nebati mnyamata wa Solomoni mwana wa Davide anauka, napandukana ndi mbuye wake.
7
Ndipo anamsonkhanira amuna achabe, anthu opanda pake, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehobowamu mwana wa Solomoni, muja Rehobowamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwalaka.
8
Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu anaang'ombe agolide adawapanga Yerobowamu akhale milungu yanu.
9
Simunapirikitsa kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amachita anthu a m'maiko ena? Kuti aliyense wakudza kudzipatulira ndi mwanawang'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu.
10
Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiya Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m'ntchito mwao,
11
nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikapo nyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.
12
Ndipo taonani, Mulungu ali nafe, wotitsogolera ndi ansembe ake, ndi malipenga oliza nao chokweza, kukulizirani inu chokweza. Ana a Israele inu, musalimbane naye Yehova Mulungu wa makolo anu; pakuti simudzapindula nako.
13
Koma Yerobowamu anazunguliritsa owalalira, awadzere kumbuyo; momwemo iwowa anali kumaso kwa Yuda, ndi owalalira anali kumbuyo kwao.
14
Ndipo pocheuka Yuda, taonani, nkhondo inayambana nao kumaso ndi kumbuyo; nafuulira iwo kwa Yehova, ndi ansembe analiza malipenga.
15
Pamenepo amuna a Yuda anafuula chokweza; ndipo pofuula amuna a Yuda, kunachitika kuti Mulungu anakantha Yerobowamu ndi Aisraele onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.
16
Ndipo ana a Israele anathawa pamaso pa Yuda, nawapereka Mulungu m'dzanja lao.
17
Ndipo Abiya ndi anthu ake anawakantha makanthidwe akulu; nagwa, nafa amuna osankhika zikwi mazana asanu a Israele.
18
Momwemo anachepetsedwa ana a Israele nthawi ija, nalakika ana a Yuda; popeza anatama Yehova Mulungu wa makolo ao.
19
Ndipo Abiya analondola Yerobowamu, namlanda midzi yake, Betele ndi milaga yake, ndi Yesana ndi milaga yake, ndi Efuroni ndi milaga yake.
20
Ndi Yerobowamu sanaonenso mphamvu m'masiku a Abiya, namkantha Yehova, nafa iye.
21
Koma Abiya anakula mphamvu, nadzitengera akazi khumi ndi anai, nabala ana amuna makumi awiri mphambu awiri, ndi ana akazi khumi mphamvu asanu ndi mmodzi.
22
Machitidwe ena tsono a Abiya, ndi mayendedwe ake, ndi mau ake, alembedwa m'buku lomasulira la mneneri Ido.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36