bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 15
2 Chronicles 15
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 16 →
1
Pamenepo mzimu wa Mulungu unagwera Azariya mwana wa Odedi,
2
ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.
3
Masiku ambiri tsono Israele anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo;
4
koma pamene anatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele m'kusautsidwa kwao, ndi kumfuna, anampeza.
5
Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakutuluka, kapena kwa iye wakulowa, koma mavuto aakulu anagwera onse okhala m'maikomo.
6
Ndipo anapasulidwa, mtundu wa anthu kupasula unzake, ndi mudzi kupasula mudzi; pakuti Mulungu anawavuta ndi masautso ali onse.
7
Koma limbikani inu, manja anu asalende; pakuti ku ntchito yanu kuli mphotho.
8
Ndipo pakumva Asa mau awa, ndi chinenero cha Odedi mneneriyo, analimbika mtima, nachotsa zonyansazo m'dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m'midzi adailanda ku mapiri a Efuremu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pachipinda cholowera cha nyumba ya Yehova.
9
Namemeza onse a m'Yuda ndi m'Benjamini, ndi iwo akukhala nao ochokera ku Efuremu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ochuluka ochokera ku Israele, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wake anali naye.
10
Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu mwezi wachitatu, Asa atakhala mfumu zaka khumi ndi zinai.
11
Naphera Yehova nsembe tsiku lija za zofunkha adabwera nazo, ng'ombe mazana asanu ndi awiri, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri.
12
Nalowa chipangano chakufuna Yehova Mulungu wa makolo ao ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse;
13
ndi kuti yense wosafuna Yehova Mulungu wa Israele aphedwe, ngakhale wamng'ono kapena wamkulu, wamwamuna kapena wamkazi.
14
Ndipo analumbira kwa Yehova ndi mau akulu, ndi kufuula ndi mphalasa ndi malipenga.
15
Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi chifuno chao chonse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.
16
Maaka yemwe, mai wake wa Asa, mfumu, namchotsa uyu asakhalenso mai wa ufumu, popeza anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fanizolo, naliphwanyaphwanya, nalitenthera ku mtsinje wa Kidroni.
17
Chinkana misanje siinachotsedwa m'Israele, mtima wa Asa unali wangwiro masiku ake onse.
18
Ndipo analowa nazo zopatulika za atate wake, ndi zopatulika zakezake, kunyumba ya Mulungu; ndizo siliva, ndi golide, ndi zipangizo.
19
Ndipo panalibenso nkhondo mpaka Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zinai.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36