bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 35
2 Chronicles 35
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 36 →
1
Pamenepo Yosiya anachitira Yehova Paska m'Yerusalemu, naphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi woyamba.
2
Ndipo anaika ansembe pa udikiro wao, nawalimbikitsa achite utumiki wa nyumba ya Yehova.
3
Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisraele onse, ndiwo opatulikira Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ake Israele.
4
Ndipo mudzikonzere monga mwa nyumba za makolo anu, m'zigawo zanu, monga umo adalembera Davide mfumu ya Israele, ndi umo adalembera Solomoni mwana wake.
5
Ndipo muimirire m'malo opatulika, monga mwa magawidwe a nyumba za makolo za abale anu ana a anthu, akhale nalo onse gawo la nyumba ya makolo ya Alevi.
6
Ndipo muphere Paska, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kuchita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.
7
Ndipo Yosiya anapatsa ana a anthu zoweta, anaankhosa ndi a mbuzi zikhale zonsezo za nsembe za Paska kwa aliyense anali komweko; zinafikira zikwi makumi atatu, ndi ng'ombe zikwi zitatu, ndizo zotapa pa chuma cha mfumu.
8
Ndi akulu ake anapatsa nsembe yaufulu kwa anthu, kwa ansembe, ndi kwa Alevi. Hilikiya ndi Zekariya ndi Yehiyele, atsogoleri a m'nyumba ya Mulungu, anapatsa ansembe zoweta zazing'ono zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi, ndi ng'ombe mazana atatu, zikhale nsembe za Paska.
9
Konaniyanso, ndi Semaya, ndi Netanele, abale ake, ndi Hasabiya, ndi Yeiyele, ndi Yozabadi, akulu a Alevi, anapatsa Alevi zoweta zazing'ono zikwi zisanu, ndi ng'ombe mazana asanu, zikhale nsembe za Paska.
10
Momwemo anakonzera kutumikiraku, naima ansembe pokhala pao, ndi Alevi m'zigawo zao, monga umo adawauzira mfumu.
11
Pamenepo anaphera Paska; ndi ansembe anawaza mwazi adaulandira m'manja mwa Alevi amene anasenda nsembezo.
12
Ndipo anachotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo.
13
Ndipo anaotcha Paska pamoto, monga mwa chiweruzo; koma zopatulikazo anaziphika m'miphika, ndi m'mitsuko, ndi m'ziwaya; nazipereka msanga kwa ana onse a anthu.
14
Ndi pambuyo pake anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; chifukwa chake Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni.
15
Ndi oimbira, ana a Asafu, anali pokhala pao, monga adalamulira Davide, ndi Asafu, ndi Hemani, ndi Yedutuni mlauli wa mfumu; ndi olindirira anali pa zipata zonse, analibe kuleka utumiki wao; pakuti abale ao Alevi anawakonzera.
16
Momwemo kutumikira konse kwa Yehova kunakonzeka tsiku lomwelo, kuchita Paska, ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la nsembe la Yehova, monga analamulira mfumu Yosiya.
17
Ndipo ana a Israele okhalako anachita Paska nthawi yomweyo, ndi chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri.
18
Panalibe Paska wochitika m'Israele wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samuele mneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israele anachita Paska wotere, ngati ameneyu anachita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisraele opezekako, ndi okhala m'Yerusalemu.
19
Yosiya atakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri anachita Paska amene.
20
Chitatha ichi chonse, Yosiya atakonza nyumbayi, Neko mfumu ya Aejipito anakwera kuyambana ku Karikemisi ku Yufurate; ndipo Yosiya anamtulukira kuyambana naye.
21
Koma Neko anatuma mithenga kwa iye, ndi kuti, Ndili ndi chiyani ndi inu, mfumu ya Yuda? Sindinafika kuyambana ndi inu lero, koma ndi nyumba imene ndili nayo nkhondo; ndipo Mulungu anati ndifulumire; lekani kuvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuonongeni.
22
Koma Yosiya sanatembenuke nkhope yake kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ochokera m'kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m'chigwa cha Megido.
23
Ndipo oponya anayang'anitsa mivi pa mfumu Yosiya, niti mfumu kwa anyamata ake, Ndichotseni ndalasidwa ndithu.
24
Pamenepo anyamata ake anamtulutsa m'galeta, namuika m'galeta wachiwiri anali naye, nabwerera naye ku Yerusalemu; nafa iye naikidwa m'manda a makolo ake. Ayuda onse ndi Yerusalemu nalira Yosiya.
25
Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba m'Israele; taonani, zilembedwa m'Nyimbo za Maliro.
26
Machitidwe ena tsono a Yosiya, ndi ntchito zake zokoma, monga mulembedwa m'chilamulo cha Yehova,
27
ndi zochita iye, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda.
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 36 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36