bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Chronicles 5
2 Chronicles 5
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 6 →
1
Momwemo zidatha ntchito zonse Solomoni adazichitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni anabwera nazo zopatulika zija za atate wake Davide; naziika siliva, ndi golide, ndi zipangizo zonse m'chuma cha nyumba ya Mulungu.
2
Pamenepo Solomoni anasonkhanitsira akuluakulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, ndi akalonga a nyumba za makolo a ana a Israele, ku Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova kumudzi wa Davide ndiwo Ziyoni.
3
Ndipo amuna onse a Israele anasonkhana kwa mfumu kumadyerero anachitikawo, m'mwezi wachisanu ndi chiwiri.
4
Nadza akuluakulu onse a Israele, nanyamula likasalo Alevi.
5
Ndipo anakwera nalo likasa, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika zinali m'chihemamo; izizo ansembe Alevi anakwera nazo.
6
Ndi mfumu Solomoni ndi khamu lonse la Israele losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kuchuluka kwake.
7
Ndipo ansembe analowa nalo likasa la chipangano la Yehova kumalo kwake m'chipinda chamkati mwa Kachisi, m'malo opatulika kwambiri, pansi pa mapiko a akerubi.
8
Pakuti akerubi anafunyulula mapiko ao pa malo a likasa, ndi akerubi anaphimba likasa ndi mphiko zake pamwamba pake.
9
Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa chakuno cha chipinda chamkati, koma sizinaoneka kubwalo; ndipo zili komweko mpaka lero lino.
10
Munalibe kanthu kena m'likasa, koma magome awiri Mose anawaika m'mwemo ku Horebu, muja Yehova anachita chipangano ndi ana a Israele potuluka iwo m'Ejipito.
11
Ndipo ansembe anatuluka m'malo opatulika, pakuti ansembe onse anali komwe adadzipatula, osasunga magawidwe ao;
12
Alevi omwe akuimba, onsewo ndiwo Asafu, Hemani, Yedutuni, ndi ana ao, ndi abale ao ovala bafuta, ali nazo nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, anaima kum'mawa kwa guwa la nsembe, ndi pamodzi nao ansembe zana limodzi mphambu makumi awiri akuomba malipenga.
13
Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;
14
ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36