bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 11
2 Kings 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 12 →
1
Ataliya, mai wake wa Ahaziya, ataona kuti mwana wake wafa, adanyamuka nakaononga onse a pa banja laufumu.
2
Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, adatenga Yowasi, mwana wa Ahaziya. Adachita momuba, kumchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene ankati aŵaphewo. Adamuika m'chipinda china chogona cha m'Nyumba ya Chauta pamodzi ndi mlezi wake. Motero adamubisa mwanayo, kubisira Ataliya, kotero kuti sadaphedwe.
3
Mwanayo adakhala ndi mlezi wake zaka zisanu ndi chimodzi akubisala m'Nyumba ya Chauta, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.
4
Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri, wansembe Yehoyada adatumiza mau kukaitana atsogoleri a asilikali olonda mfumu ndipo a alonda a nyumba yaufumu. Adabwera nawo kwa Yehoyada ku Nyumba ya Chauta. Tsono adapangana nawo chipangano ndipo adaŵalumbiritsa m'Nyumba ya Chauta. Kenaka adaŵaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja,
5
naŵalamula kuti, “Zimene mudzachite ndi izi: Inu a m'chigaŵo chija choyamba, amene mukudzatumikira pa Sabata, mugaŵikane patatu: gulu limodzi lidzalonde ku nyumba ya mfumu;
6
gulu lachiŵiri lidzalonde pa Chipata cha Suri, gulu lachitatu lidzalonde pa chipata cha kumbuyo kwa asilikali, azilonda pa zipata zoloŵera ku Nyumba ya Chauta.
7
Tsono enawo a m'zigawo ziŵiri zija odzaŵeruka ntchito pa Sabata, iwo adzalonde ku Nyumba ya Chauta, kuti aziteteza mfumu.
8
Mudzazungulire mfumuyo, aliyense atatenga zida m'manja. Wina aliyense amene at ayandikire pafupi, aphedwe. Muzikhala nayo mfumu kulikonse kumene iziyenda.”
9
Atsogoleriwo adachitadi zonse monga m'mene wansembe Yehoyada adaŵalamulira. Aliyense adabwera ndi anthu ake amene ankadzayamba ntchito yao pa Sabata, pamodzinso ndi anthu amene ankasiya ntchito yao kulonda pa Sabata. Onsewo adafika kwa Yehoyada wansembe uja.
10
Wansembeyo adapatsa atsogoleri aja mikondo ndi zishango, zimene zidaali za mfumu Davide. Zimenezi zinkasungidwa m'Nyumba ya Chauta.
11
Tsono adandanditsa asilikaliwo kuti aziteteza mfumu, aliyense ali ndi zida m'manja mwake, kuzungulira guwalo ndiponso Nyumbayo.
12
Kenaka adaŵatulutsira mwana wa mfumu, namuveka chisoti chaufumu, nkumupatsa buku la malamulo, ndipo adamdzoza namlonga ufumu. Anthu adamuwombera m'manja nkunena mofuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali.”
13
Tsono mfumukazi Ataliya, atamva phokoso la asilikali ndi la anthu, adapita ku Nyumba ya Chauta.
14
Atayang'ana, adaona mfumu itaima pa nsanja yake potsata mwambo wachifumu, atsogoleri ndi anthu oimba malipenga ali pafupi ndi mfumuyo. Anthu onse am'deralo ankakondwa, namaimba malipenga. Pamenepo Ataliyayo adang'amba zovala zake, ndipo mofuula adati, “Akundiwukira! Akundiwukira!”
15
Tsono wansembe Yehoyada adalamula atsogoleri a gulu lankhondo aja kuti, “Mtulutseni ameneyu pakati pa mizere mwandandayo. Ndipo aliyense amene amtsate, mumuphe ndi lupanga.” Wansembeyo adaanenadi kuti, “Musamphere m'Nyumba ya Chauta ai.”
16
Choncho anthuwo adamgwira Ataliya uja, ndipo atafika naye ku nyumba ya mfumu, pakhomo lotchedwa la Akavalo, adamuphera pamenepo.
17
Tsono Yehoyada adachititsa chipangano pakati pa Chauta ndi mfumu pamodzi ndi anthu ake, kuti iwowo akhale anthu akeake a Chauta. Anthuwo adachitanso chipangano ndi mfumu,
18
Choncho anthu onse a m'dzikomo adapita ku nyumba ya Baala nakaigwetsa. Maguwa ake ndi mafano ake adaŵaphwanyaphwanya. Kenako adapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo. Tsono wansembe Yehoyada adaika alonda ku Nyumba ya Chauta.
19
Pambuyo pake iyeyo adandanditsa atsogoleri a ankhondo, asilikali olonda mfumu, alonda a nyumba ya mfumu, ndi anthu onse a m'dzikomo. Onsewo adaperekeza mfumu kuchokera ku Nyumba ya Chauta, nadzera ku chipata cha alonda mpaka kukafika ku nyumba ya mfumu. Pomwepo Yowasi adakhala pa mpando waufumu.
20
Motero anthu am'dzikomo adakondwa. Ndipo mumzindamo mudakhala bata, Ataliya ataphedwa ku nyumba ya mfumu.
21
Yowasiyo anali wa zaka zisanu ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25