bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 15
2 Kings 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 16 →
1
Chaka cha 27 cha ufumu wa Yerobowamu mfumu ya ku Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu.
2
Iyeyu anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 52 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu.
3
Azariya adachita zolungama pamaso pa Chauta, monga momwe ankachitira bambo wake Amaziya.
4
Komabe akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu ankaperekabe nsembe ndi kumafukiza lubani pa malo amenewo.
5
Tsono Chauta adailanga mfumuyo ndi nthenda ya khate mpaka kufa kwake, ndipo inkakhala m'nyumba yakeyake yapadera. Choncho Yotamu mwana wa mfumuyo ndiye amene ankayang'anira banja la mfumu, namalamulira anthu m'dzikomo m'malo mwake.
6
Tsono ntchito zina za Azariya ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
7
Ndipo adamwalira naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Ndiye Yotamu mwana wake adaloŵa ufumu.
8
Chaka cha 38 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu, adaloŵa ufumu wa Aisraele ku Samariya kwa miyezi isanu ndi umodzi.
9
Iyeyo ankachita zoipa kuchimwira Chauta, monga momwe ankachitira makolo ake. Sadazileke zoipa zimene Yerobowamu mwana wa Nebati, adachimwitsa nazo Aisraele.
10
Tsono Salumu mwana wa Yabesi adamchita chiwembu Zekariya, ndipo adamphera ku Ibleamu. Choncho Salumuyo adaloŵa ufumu m'malo mwake.
11
Tsono ntchito zonse zimene adachita Zekariya zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Israele.
12
Izi ndi zimene Chauta adalonjeza Yehu, adati, “Ana ako aamuna adzalamulira Aisraele mpaka mbadwo wachinai.” Ndipo zidachitikadi momwemo.
13
Salumu mwana wa Yabesi adaloŵa ufumu pa chaka cha 39 cha ufumu wa Uziya mfumu ya ku Yuda, ndipo adalamulira mwezi umodzi ku Samariya.
14
Tsono Menahemu mwana wa Gadi, adachoka ku Tiriza nakafika ku Samariya. Adapha Salumu mwana wa Yabesi ku Samariyako, iyeyo nkuloŵa ufumu m'malo mwa Salumu.
15
Tsono ntchito zonse za Salumu ndi chiwembu chimene adachita, zonsezi zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
16
Nthaŵi imeneyo, kuchokera ku Tiriza Menahemu adakaononga mzinda wa Tapuwa ndi anthu onse amene anali m'menemo, kuphatikiza dziko lonse lozungulira, poti iwo sadamgonjere. Adaphanso akazi apathupi amumzindamo naŵang'amba.
17
Chaka cha 39 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Menahemu mwana wa Gadi adaloŵa ufumu wa ku Israele, ndipo adalamulira zaka khumi ku Samariya.
18
Menahemu ankachita zoipa kuchimwira Chauta. Masiku onse a moyo wake sadaleke kuchita zoipa zonse zimene ankachita Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.
19
Pambuyo pake Pulo, mfumu ya ku Asiriya, adadzathira nkhondo dziko la Israele. Ndipo Menahemu adakapereka kwa Pulo siliva wokwanira makilogramu 34,000, kuti Puloyo amthandize kukhazikitsa ufumu wake.
20
Menahemu adapeza ndalamazo kuchokera ku msonkho umene ankakhometsa Aisraele. Anthu onse olemera ankaŵakhometsa aliyense masekeli asiliva makumi asanu. Motero mfumu ya ku Asiriya idabwerera, ndipo sidakhale m'dzikomo.
21
Tsono ntchito zina za Menahemu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
22
Ndipo Menahemu adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo. Tsono Pekahiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
23
Chaka cha 50 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu, adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka ziŵiri.
24
Pekahiya adachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa zimene ankachita Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.
25
Tsono Peka mwana wa Remaliya nduna yake, pamodzi ndi anthu makumi asanu a ku Giliyadi, adapangana za chiwembu napha Pekahiya ku Samariya m'chipinda choteteza nyumba ya mfumu. Pambuyo pake Pekayo adaloŵa ufumu m'malo mwake.
26
Tsono ntchito zina za Pekahiya ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
27
Chaka cha 52 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Peka mwana wa Remaliya adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya. Ndipo adalamulira zaka makumi aŵiri.
28
Koma adachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.
29
Nthaŵi ya Peka mfumu ya ku Israele, Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya, adadzagonjetsa mizinda iyi: Iyoni, Abele-Beti-Maaka, Yanowa, Kedesi, Hazori, dziko la Giliyadi ndi la Galilea, ndiponso dziko lonse la Nafutali. Ndipo anthu onse am'menemo adaŵagwira ukapolo, napita nawo ku Asiriya.
30
Nthaŵi imeneyo Hoseya mwana wa Ela adachita chiwembu kuchitira mfumu Peka, namupha. Ndipo iyeyo adaloŵa ufumu m'malo mwake pa chaka cha 20 cha ufumu wa Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya ku Yuda.
31
Tsono ntchito zina za Peka ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Israele.
32
Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya ku Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu.
33
Anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yerusa, mwana wa Zadoki.
34
Yotamu adachita zolungama pamaso pa Chauta ndipo kutsata zonse zimene ankachita Uziya bambo wake.
35
Komabe akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu ankaperekabe nsembe namafukiza lubani pa malo amenewo. Yotamu ndiye adamanga chipata chakumpoto cha Nyumba ya Chauta.
36
Tsono ntchito zina za Yotamu, ndi zonse zimene ankachita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
37
Nthaŵi imene Yotamu ankalamulira, mpamene Chauta adayambapo kutuma Rezini mfumu ya ku Siriya ndi Peka mwana wa mfumu ya ku Israele, kuti akathire nkhondo dziko la Yuda.
38
Yotamu adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo, mu mzinda wa Davide kholo lake. Ndipo Ahazi mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25