bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 17
2 Kings 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 18 →
1
Chaka cha 12 cha ufumu wa Ahazi mfumu ya ku Yuda, Hoseya mwana wa Ela adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya. Ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zinai.
2
Tsono adachita zoipa kuchimwira Chauta, komabe osalingana ndi mafumu a ku Israele amene ankalamulira, iyeyo asanaloŵe ufumu.
3
Salimanezere, mfumu ya ku Asiriya, adadza kudzamthira nkhondo, ndipo Hoseya adamgonjera, namakhoma msonkho kwa iyeyo.
4
Koma tsiku lina mfumu ya ku Asiriya idaona kuti Hoseya akuchita zaupandu. Ndiye kuti Hoseyayo anali atatuma amithenga kukapempha chithandizo kwa So, mfumu ya ku Ejipito, Ndiponso adaaleka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, m'menemo kale ankakhoma chaka ndi chaka. Nchifukwa chake mfumu ya ku Asiriya itamva zimenezi, idamanga Hoseya ndi kumuika m'ndende.
5
Nthaŵi yomweyo Salimanezere, mfumu ya ku Asiriya, adathira nkhondo dziko la Israele nakafika ku Samariya, nkukauzinga mzindawo ndi zithando zankhondo zaka zitatu.
6
Chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Hoseya, mfumu ya ku Asiriya idagonjetsa Samariya, ndipo idatenga Aisraele kuŵachotsa kwao kupita nawo ku Asiriya. Idaŵakhazika ena ku mzinda wa Hala, ena kufupi ndi mtsinje wa Habori m'dera la Gozani, ndipo enanso ku mizinda ya Amedi.
7
Zimenezo zidaoneka chifukwa Aisraele adachimwira Chauta Mulungu wao, amene adaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, kuŵachotsa m'manja mwa Farao mfumu ya ku Ejipito. Aisraelewo ankapembedza milungu ina,
8
ndipo ankayenda motsata miyambo ya anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa pamene ankafika Aisraele. Ankatsatanso miyambo yachilendo imene mafumu ena a Aisraele anali ataiyambitsa.
9
Ndipo Aisraele ankachita zinthu zoipa mobisika namachimwira Chauta Mulungu wao. Adadzimangira akachisi opembedzerako mafano ku midzi yao yonse ndi ku mizinda yomwe.
10
Adadzimangira zipilala zoimiritsa ndiponso mafano pa phiri lililonse lalitali ndi patsinde pa mitengo yogudira.
11
Ndipo anthuwo ankafukiza lubani ku akachisi onse, monga m'mene ankachitira anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraelewo.
12
Tsono adapembedza mafano kuchimwira Chauta amene anali ataŵauza kuti, “Musadzachite zimenezi.”
13
Monsemo Chauta adatuma amithenga ndi aneneri ake ku Israele ndi ku Yuda, okalalika kuti, “Musinthe makhalidwe anu auchimo ndipo mumvere Malamulo anga amene ndidaŵapereka kwa makolo anu, kudzera mwa aneneri, atumiki anga.”
14
Koma anthuwo sankamva, anali ouma mitu monga momwe analiri makolo ao amene sadakhulupirire Chauta Mulungu wao.
15
Iwowo adanyoza malamulo a Chauta ndi chipangano cha Chauta chimene Iye adachita ndi makolo ao. Adanyozanso zochenjeza za Chauta. Adatsata milungu yachabechabe, ndipo iwo omwe adasanduka achabechabe. Ankatsata zitsanzo za anthu a mitundu ina okhala nawo pafupi, ngakhale Chauta anali atalamula kuti asamachite mofanana ndi mitundu imeneyo.
16
Motero adasiya malamulo onse a Chauta Mulungu wao, nadzipangira mafano aŵiri osungunula anaang'ombe. Adapanganso mafano ena a Asera namapembedza zinthu zakumlengalenga ndiponso Baala.
17
Anthuwo adapereka ngati nsembe ana ao aamuna ndi ana ao aakazi, ndipo ankaombeza maula, namachitanso zanyanga. Adadzipereka kuti azichita zoipa zochimwira Chauta, namkwiyitsa.
18
Nchifukwa chake Chauta adakwiya nawo kwambiri Aisraele, ndipo adaŵachotsa osafuna kuŵaonanso. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adatsalako, kupatula a fuko la Yuda okha.
19
Nawonso a fuko la Yuda sadasunge malamulo a Chauta Mulungu wao, koma ankayenda motsata miyambo imene Aisraele adaiyambitsa.
20
Choncho Chauta adakana zidzukulu zonse za Aisraele, nazizunza, nkuzipereka mu ulamuliro wa anthu ofunkha, mpaka ataŵachotseratu onse.
21
Chauta ataŵalekanitsa Aisraele kuŵachotsa pa banja la Davide, iwo adaika Yerobowamu mwana wa Nebati kuti akhale mfumu yao. Yerobowamuyo adaletsa Aisraele kuti asatsate Chauta, ndipo adaŵachimwitsa kwambiri Aisraelewo.
22
Aisraele ankachita zoipa zonse zimene adachita Yerobowamu mfumu yao. Sadaleke zimenezo,
23
mpaka Chauta adaŵachotsa Aisraele kotheratu, monga momwe adaalankhulira kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri. Motero Aisraele adatengedwa ukapolo kuchoka ku dziko lakwao kupita ku Asiriya, ndipo ali kumeneko mpaka pano.
24
Pambuyo pake mfumu ya ku Asiriya idabwera ndi anthu kuchokera ku mizinda ya Babiloni, Ava, Hamati ndi Sefaravaimu, nkudzaŵakhazika ku dziko la Samariya m'malo mwa Aisraele amene adatengedwa ukapolo. Tsono anthuwo adaloŵa m'midzi ya Samariyayo naisandutsa yaoyao.
25
Koma iwowo chiloŵere chao kumeneko sankapembedza Chauta. Nchifukwa chake Chauta adatumiza mikango pakati pao, nipha ena mwa iwowo.
26
Motero mfumu ya ku Asiriya idamva kuti, “Anthu a mitundu ina aja amene mudaŵakhazika m'midzi ya ku Samariya, sakudziŵa kupembedza Mulungu wa dzikolo. Nchifukwa chake Mulungu adaŵatumizira mikango pakati pao, ndipo ikuŵapha, chifukwa sakuchita zimene Mulunguyo akufuna.”
27
Tsono mfumu ya ku Aasiriya idalamula kuti, “Tumani mmodzi mwa ansembe amene mudaŵagwira kumeneko, akakhale komweko, kuti akaŵaphunzitse kupembedza Mulungu wa dzikolo.”
28
Motero mmodzi mwa ansembe amene adaŵatenga ku Samariya adadzakhala ku Betele, nayamba kuŵaphunzitsa anthu kupembedza Chauta.
29
Koma mtundu uliwonse wa anthuwo unkapangabe mafano a milungu yaoyao, ndipo ankaika milunguyo m'nyumba zachipembedzo zimene Asamariya adaazimanga. Mtundu uliwonse wa anthuwo unali ndi nyumba za mulungu wao ku mzinda uliwonse kumene ankakhala.
30
Anthu a ku Babiloni adadzipangira fano lotchedwa Sukoti-Benoti. Anthu a ku Kuta adapanga fano lotchedwa Neregali, anthu a ku Hamati adapanga fano lotchedwa Ashima.
31
Aavi adapanga fano lotchedwa Nibihazi ndiponso Taritaki. Asefaravaimu ankapereka ana ao ngati nsembe zopsereza kwa Adrameleki ndi kwa Anameleki, milungu ya Asefaravaimu.
32
Anthuwo ankapembedzanso Chauta nadzisankhira pakati pao anthu wamba, kuti akhale ansembe otumikira ku nyumba zao zachipembedzo. Ansembe amenewo ndi amene ankaperekera anthu nsembe m'nyumba zopembedzeramo milungu yao ku zitunda.
33
Motero ankapembedza Chauta, kwinaku ankatumikirabe milungu yao, potsata makhalidwe a mitundu ya anthu a kumene adatengedwa ukapoloko.
34
Akuchitabe zimene ankachita kale mpaka lero lino. Iwowo salemekeza Chauta kwenikweni ndipo satsata zogamula kapena zolengeza, ngakhale malangizo kapena malamulo amene Chauta adalamula zidzukulu za Yakobe, amene adamtchula kuti Israele.
35
Chauta adaachita nawo Aisraele chipangano naŵalamula kuti, “Musapembedze milungu ina kapena kuilambira kapena kuitumikira, kapena kuiperekera nsembe.
36
Koma muzipembedza Ine Chauta amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito ndi mphamvu zanga zazikulu ndi mkono wanga wokutetezani. Muzigwadira Ine Chauta, ndipo muzipereka nsembe kwa Ine ndekha.
37
Ndipo inu muzisamala zogamula ndi zolengeza, malangizo ndi malamulo amene Ine Chauta ndidakupatsani. Musamapembedza milungu ina ai,
38
ndipo musaiŵale chipangano chimene ndidachita ndi inu. Musamapembedze milungu ina,
39
koma muzipembedza Ine Chauta Mulungu wanu, ndipo ndidzakupulumutsani kwa adani anu.”
40
Komabe iwowo sankamva zimenezi, koma ankachitabe zimene adakhala akuchita kuyambira kale.
41
Motero mitundu ya anthu imeneyi inkapembedza Chauta, kwinaku nkumatumikira milungu yao yachabechabe ija. Ana ao adachitanso zomwezo, adzukulu ao adachita zokhazokhazo zimene ankachita makolo ao, ndipo akuchitabe zomwezo mpaka pano.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25