bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 2
2 Kings 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 3 →
1
Idafika nthaŵi imene Chauta adafuna kutenga Eliya m'kamvulumvulu kunka kumwamba. Tsiku limenelo Eliya ndi Elisa anali pa ulendo kuchokera ku Giligala.
2
Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, Elisa, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Betele.” Koma Elisa adati, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adapita ku Betele.
3
Tsono a m'gulu la aneneri amene anali ku Beteleko adadzakumana ndi Elisa, namufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti lero Chauta akulandani mbuyanu?” Elisa adayankha kuti, “Inde, ndikudziŵa, koma musakambe za zimenezi.”
4
Tsiku lomwelo Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, Elisa, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Yeriko.” Koma Elisa adati, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adakafika ku Yeriko.
5
Ndipo a m'gulu la aneneri amene anali ku Yeriko adadzakumana ndi Elisa, namufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti lero Chauta akulandani mbuyanu?” Elisa adayankha kuti, “Inde, ndikudziŵa, koma musakambe za zimenezi.”
6
Pambuyo pake Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Yordani.” Koma Elisa adauza Eliyayo kuti, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adapitiriza ulendo wao.
7
Anthu makumi asanu a m'gulu la aneneri aja adapita nawo ndipo adakaimirira chapatali potero, pamene Eliya ndi Elisa adaakaima pa gombe la mtsinje wa Yordani.
8
Apo Eliya adatenga mwinjiro wake naupinda, kenaka adamenya madzi ndi mwinjirowo. Tsono madziwo adapatukana, ena kwina ena kwina, mpaka aneneri aŵiriwo adaoloka pouma.
9
Ataoloka, Eliya adauza Elisa kuti, “Undipemphe choti ndikuchitire ndisanakusiye.” Elisa adati, “Ndikukupemphani kuti ndilandire chigawo chachikulu cha mphamvu zanu za uneneri.”
10
“Eliya adauza Elisayo kuti, ‘Wapempha chinthu chapatali. Komabe ukandipenya pa nthaŵi imene ndikukusiya, zimene wapemphazi zidzakuchitikiradi. Koma ukapanda kundipenya, sizidzachitika.’ ”
11
Tsono iwowo akuyendabe ndi kumakamba, adangoona galeta lamoto ndi akavalo ake amoto zikuŵasiyanitsa aŵiriwo. Ndipo Eliya adakwera kumwamba m'kamvulumvulu.
12
Elisa adaona zimenezi nafuula kuti, “Bambo wanga, Bambo wanga! Magaleta a Aisraele ndi anthu ake okwera pa akavalo.” Ndipo sadamuwonenso Eliyayo. Tsono Elisa adagwira zovala zake nazing'amba paŵiri.
13
Kenaka adatenga mwinjiro wa Eliya umene udaagwa, nabwerera nkukaima pa gombe la Yordani.
14
Adagwira mwinjiro wa Eliyawo namenya nawo madzi aja, nati, “Ali kuti Chauta, Mulungu wa Eliya?” Atamenya madziwo choncho, madzi aja adapatukana, ena kwina, ena kwina. Ndipo Elisa adaoloka.
15
Pamene a m'gulu la aneneri amene ankakhala ku Yeriko adaona Elisayo akuwoloka, adati, “Mphamvu ndi nzeru za Eliya zaloŵa mwa Elisa.” Tsono adabwera kudzakumana naye, namgwadira Elisayo, nkuŵeramitsa mitu yao pansi.
16
Ndipo iwo adamuuza kuti, “Taonani tsono, ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Chonde mulole kuti anyamuke akamufunefune mbuyanu Eliya. Mwina mwake mzimu wa Chauta wamtenga nkukamponya kuphiri kwina kapena ku chigwa.” Elisayo adati, “Iyai musaŵatume.”
17
Koma adamkakamiza mpaka Elisayo mwamanyazi adaŵalola naŵauza kuti, “Chabwino, atumeni.” Ndiye iwo adaŵatuma anthu makumi asanuwo. Ndipo anthuwo adakafunafuna Eliya masiku atatu, koma osampeza.
18
Tsono adabwerera kwa Elisayo pamene iyeyo ankadikira ku Yeriko, ndipo iye adaŵauza kuti, “Kodi suja ndidaanena kuti musapite?”
19
Tsiku lina anthu amumzinda adauza Elisa kuti, “Onani, mzinda wathuwu ngwabwino kwambiri, zonse zili bwino monga mukuwoneramu, koma madzi okha ngoipa, ndipo nthaka yake njosabereka.”
20
Apo Elisa adati, “Patseni mbale yatsopano, ndipo muikemo mchere.” Anthuwo adabweradi ndi mchere m'mbale.
21
Tsono Elisa adapita ku kasupe wa madzi, nathiramo mchere m'kasupemo, nati, “Chauta akunena kuti, ‘Madzi ameneŵa ndaŵakonza. Kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo, m'madzi ameneŵa simudzakhala chinthu chopha anthu kapena choletsa nthaka kubereka.’ ”
22
Motero madziwo ngabwinobe kwambiri mpaka lero lino, potsata mau amene Elisa adaalankhula.
23
Kuchokera kumeneko Elisa adapita ku Betele. Ndipo pamene anali pa njira, anyamata ena amumzindamo adatuluka nayamba kumseka kuti, “Choka apa, chidazi! Choka apa, chidazi!”
24
Tsono Elisayo adatembenuka, ndipo ataŵaona anyamatawo, adaŵatemberera m'dzina la Chauta. Pompo padatuluka zimbalangondo ziŵiri zazikazi kuchokera kuthengo, nkuphapo anyamata 42.
25
Atachoka kumeneko, Elisa adapitirira kunka ku phiri la Karimele, ndipo pochoka kumeneko adabwerera ku Samariya.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25