bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 5
2 Kings 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 6 →
1
Panali mkulu wina wa gulu lankhondo la mfumu ya ku Siriya, dzina lake Naamani, amene anali munthu wokhulupirika kwambiri kwa mbuye wake. Mbuye wakeyo ankamkonda Naamaniyo kwambiri, chifukwa choti ankhondo ake ankapambana pa nkhondo, popeza kuti Chauta anali naye Naamaniyo. Naamaniyo anali munthu wamphamvu ndiponso wolimba mtima, koma anali wakhate.
2
Nthaŵi ina Asiriya adaagwirako mtsikana ku dziko la Israele kumene adakathirako nkhondo, ndipo mtsikanayo adasanduka mdzakazi wa mkazi wa Naamani.
3
Tsono mtsikana uja adauza mkazi wa Naamani kuti, “Bwanji kodi osati ambuyanga apite kwa mneneri ku Samariya, kuti mneneriyo akaŵachize khate laoli.”
4
Naamani atamva zimene adaanena mtsikana uja, adapita kwa mfumu nakaiuza kuti, “Mtsikana amene tidakagwira ku Israele uja wanena kuti ati ndipite ku Samariya, kuti mneneri wakumeneko akandichize.”
5
Pamenepo mfumuyo idamuuza kuti, “Ai ndithu upite, ine ndilemba kalata yofotokozera kwa mfumu ya ku Israele.” Choncho Naamani adanyamuka ulendo wopita ku Samariya, atatenga ndalama zasiliva 30,000, ndalama zagolide 6,000, ndiponso zovala khumi zapachikondwerero.
6
Atafika kwa mfumu ya ku Israele, adapereka kalata ija imene mau ake anali akuti, “Landirani kalatayi. Tsono amene ndakutumiziraniyo ndi Naamani mtumiki wanga, ndipo ndikufuna kuti inuyo mumchize khate lake.”
7
Koma mfumu ya ku Israele ija itaŵerenga kalatayo, idang'amba zovala zake chifukwa cha chisoni, ndipo idati, “Kodi ine ndine Mulungu amene amapha ndi kupatsanso moyo, kuti munthu ameneyu azindilembera mau oti ndichize khate la munthu wake? Nchodziŵikiratu kuti iyeyo akungofuna chifukwa choti ayambane nane.”
8
Koma mneneri Elisa atamva kuti mfumu ya ku Israele idang'amba zovala zake, adatumiza mau kwa mfumuyo akuti, “Chifukwa chiyani mwang'amba zovala zanu? Alendowo abwere kwa ine tsopano lino, kuti adziŵe kuti ku Israele kuli mneneri.”
9
Motero Naamani adadza ndi akavalo ake ndi magaleta ake, nakaima pakhomo pa nyumba ya Elisa.
10
Tsono Elisa adamtumira wamthenga kukamuuza kuti, “Pitani mukasambe mu mtsinje wa Yordani kasanunkaŵiri, ndipo muchira ndi kuyeretsedwa.”
11
Koma Naamani atamva zimenezi, adakwiya kwambiri nachokapo. Popita iye ankati, “Ha! Ine ndimaganiza kuti atuluka kubwera pano, ndipo aimirira natama dzina la Chauta Mulungu wake mopemba, naweyula dzanja lake pamwamba pa nthendapo, ndi kundichiritsa motero.
12
Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko, siposa mitsinje yonse ya ku Israele kuno? Monga sindikadatha kukasamba m'mitsinje imeneyo ndi kuchiritsidwa?” Pomwepo adapotoloka, nachokapo molunda.
13
Koma atumiki ake adasendera pafupi namufunsa kuti, “Pepani bambo, kodi mneneri akadakulamulani chinthu chachikulu, inu simukadachita? Monga nchapatali kukasamba monga momwe mneneriyo wakuuziranimo?”
14
Motero Naamaniyo adapita ku Yordani, nakakhuvula m'madzimo kasanunkaŵiri, malinga ndi m'mene adaamuuzira munthu wa Mulungu uja. Pompo adachira ndipo thupi lake lidangoti see ngati la kamwana, choncho adakhala woyeretsedwa.
15
Pambuyo pake Naamani pamodzi ndi onse omperekeza, adabwerera kwa mneneri wa Mulungu uja. Adadzaima pamaso pa Elisa namuuza kuti, “Ndithu, ine ndadziŵa tsopano kuti pa dziko lonse lapansi kulibe Mulungu wina, koma wa ku Israele yekha. Tsono landirani mphatsoyi kwa ine mtumiki wanu.”
16
Koma Elisa adati, “Pali Chauta, Mulungu wamoyo, amene ndimamtumikira, ine sindilandira zimenezi.” Naamani adamkakamiza kuti atenge, koma iye adakana ndithu.
17
Tsono Naamani adati, “Ngati mukukana, ine ndikukupemphani kuti mundilole ine mtumiki wanu nditengeko dothi lokwanira kunyamula abulu aŵiri. Pakuti kuyambira tsopano ine sindidzaperekanso nsembe zopsereza, kapena nsembe ina iliyonse, kwa mulungu wina aliyense, koma kwa Chauta basi.
18
Chauta andikhululukire ine pa chokhachi chakuti pamene mbuyanga mfumu akupita kukapembedza ku nyumba ya Chauta wake Rimoni, ine ndimatsagana naye ndipo ndimakagwada m'nyumba ya Rimoniyo. Chauta andikhululukire ine mtumiki wanu zimenezi.”
19
Elisa adamuuza kuti, “Ai, inu kafikeni bwino.”
20
Koma Naamani atangoyenda mtunda pang'ono, Gehazi, mtumiki wa Elisa mneneri wa Mulungu, adayamba kulingalira kuti, “Mbuyanga walekerera Naamani Msiriyayu, osalandira zimene adabwera nazo kudzapereka. Pali Chauta, Mulungu wamoyo, ine ndimthamangira kuti ndikalandireko kanthu.”
21
Motero Gehazi adalondola Naamani uja. Naamani ataona kuti munthu akumthamangira, adatsika pa galeta kuti amchingamire. Tsono adafunsa kuti “Kodi nkwabwino?”
22
Gehazi adati, “Inde, nkwabwino. Koma mbuyanga wandituma chifukwa tsopano apa kwangomufikira anthu aŵiri a m'gulu la aneneri, kuchokera ku dziko lamapiri la Efuremu. Tsono akukupemphani kuti chonde muŵapatseko ndalama zasiliva 3,000 ndi zovala ziŵiri zapaphwando.”
23
Pamenepo Naamani adati, “Inu tengani ndithu ngakhale 6,000 zimene.” Choncho adamkakamiza, nalonga m'matumba ndalama za silivazo, pamodzi ndi zovala zapaphwandozo, nasenzetsa antchito ake aŵiri. Ndipo adanyamuka, antchitowo patsogolo, Gehazi pambuyo pao.
24
Tsono Gehazi uja atafika kuphiri kumene kunali nyumba ya Elisa, adaŵalanda antchitowo ndalama zija nazilonga m'nyumba mwake. Ndipo adaŵauza kuti apite, iwo nkupita.
25
Pambuyo pake Gehazi adapita kwa mbuyake. Elisa adamufunsa kuti, “Kodi Gehazi, unali kuti?” Iyeyo adati, “Sindidayende kwina kulikonse, bambo.”
26
Koma Elisayo adamufunsanso kuti, “Kodi ukuyesa kuti sindidakuwone monse muja munthu uja amatsika pa galeta kuti adzakuchingamire? Kodi imeneyi inali nthaŵi yolandira ndalama ndi zovala, minda ya olivi ndi ya mphesa, kapena ng'ombe, akapolo kapena adzakazi?
27
Ndiyetu tsono khate la Naamani lidzakumatirira iweyo ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.” Motero Gehazi adatuluka m'nyumbamo ali ndi khate lambuu ngati chipale.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25