bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 21
2 Kings 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 22 →
1
Manase anali wa zaka khumi ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 55 ku Yerusalemu. Mai wake anali Hepeziba.
2
Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta, potsata ntchito zonyansa za anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa pofika Aisraele.
3
Manaseyo adamanganso akachisi amene bambo wake Hezekiya adaaononga ku mapiri. Adamangira Baala maguwa, napanga mafano monga m'mene ankachitira Ahabu mfumu ya Aisraele. Ndipo ankapembedza zinthu zakuthambo namazitumikira.
4
Adamangira mafanowo maguwa m'Nyumba ya Chauta imene Chautayo adaanena kuti, “Ku Yerusalemu ndiye kumene azikandipembedzerako.”
5
Manase yemweyo adamangira zinthu zakuthambo maguwa m'mabwalo aŵiri a Nyumba ya Chauta.
6
Pambuyo pake adapereka mwana wake wamwamuna ngati nsembe. Ankatama mizimu mopemba ndiponso ankaombeza maula, namachita zobwebwetetsa ndi zaufiti. Adachita zoipa zambiri zimene zidakwiyitsa Chauta.
7
Adaika m'Nyumba ya Chauta fano losema la Asera. Nyumba imeneyo, Chauta anali atauza Davide ndi Solomoni mwana wake kuti, “M'nyumba iyi ndi mu Yerusalemu muno, ndimo m'mene ndasankha pakati pa mafuko onse a Israele kuti azindipembedzeramo mpaka muyaya.
8
Tsono sindidzalola kuti Aisraele adzachotsedwe m'dziko lao limene ndidapatsa makolo ao, malinga kuti iwowo azisamala kuchita zinthu zonse motsata Malamulo amene ndaŵalamula, ndiponso motsata Malamulo amene Mose mtumiki wanga adaŵalamula.”
9
Koma anthuwo sadamve zimenezo, ndipo Manase adaŵasokeretsa ndi kuŵachimwitsa kwambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵaononga pofika Aisraele.
10
Nchifukwa chake Chauta adalankhula kudzera mwa atumiki ake aneneri, nati,
11
“Manase mfumu ya ku Yuda wachita zonyansa zambiri, ndipo wachita zoipa kupambana zoipa zonse zimene ankachita Aamori amene adaalipo kale iye asanabadwe, ndipo wachimwitsanso anthu a ku Yuda ndi mafano akewo.
12
Nchifukwa chake Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, ‘Ndithu, ndidzabweretsa pa Yerusalemu ndi pa Yuda choipa chakuti aliyense amene adzachimve, adzadodoma nkupukusa mutu.
13
Ndidzalanga Yerusalemu monga ndidalangira Samariya ndi Ahabu, pamodzi ndi banja lake. Tsono ndidzayeretsa Yerusalemu pochotsa anthu ake, monga momwe munthu amachitira popukuta mbale, ndipo ataipukuta amaivundikira pansi.
14
Tsono anthu otsala ndidzaŵachotsa m'dziko ndi kuŵapereka m'manja mwa adani ao. Adzaphedwa ndipo adaniwo adzaŵalanda zonse.
15
Zidzatero popeza kuti akhala akundichimwira ndipo andikwiyitsa, kuyambira tsiku limene makolo ao adatuluka ku Ejipito mpaka lero lino.’ ”
16
Tsono Manase uja adakhetsa kwambiri magazi a anthu osachimwa, mpaka magaziwo kuyenderera m'miseu ya Yerusalemu kuyambira mbali ina mpaka mbali ina. Izi zidaonjezera pa machimo amene adachimwitsa nawo Ayuda pakuŵachititsa zoipa zonyoza Chauta.
17
Tsono ntchito zina za Manase ndi zonse zimene adachita, ndiponso machimo amene adachita, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
18
Choncho Manase adamwalira, naikidwa m'manda m'munda wa ku nyumba yake, m'munda wa Uza. Tsono Amoni mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
19
Amoni anali wa zaka 22 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka ziŵiri ku Yerusalemu. Mai wake anali Mesulemeti, mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.
20
Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta monga m'mene ankachitira Manase bambo wake.
21
Iyeyo ankatsata chitsanzo choipa cha bambo wake pazonse, namatumikira mafano amene bambo wake ankaŵatumikira ndi kumaŵapembedza.
22
Adakana Chauta, Mulungu wa makolo ake, ndipo sadamvere malamulo ake.
23
Tsono anyamata ake adamchita chiwembu, namupha m'nyumba mwake momwe.
24
Koma anthu am'dzikomo adapha onse aja amene adamchita chiwembu mfumu Amoniyo. Kenanaka anthuwo adalonga Yosiya mwana wake kuti akhale mfumu m'malo mwake.
25
Tsono ntchito zonse zimene adachita Amoni zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
26
Atamwalira adaikidwa m'manda m'munda wa ku nyumba yake, m'munda wa Uza. Ndipo mwana wake Yosiya adaloŵa ufumu m'malo mwake.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25