bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 14
2 Kings 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 15 →
1
Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya ku Israele, Amaziya mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu.
2
Iyeyo anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yehowadani wa ku Yerusalemu.
3
Tsono Amaziya adachita zolungama pamaso pa Chauta, komabe osati nthaŵi zonse monga Davide kholo lake. Ankachita zonse monga m'mene ankachitira Yowasi bambo wake.
4
Koma akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu adapitirirabe kupereka nsembe ndi kumafukiza lubani pa malo amenewo.
5
Atangolandira mphamvu zonse zaufumu m'manja mwake, Amaziya adapha anyamata ake amene adaapha mfumu ija, bambo wake. Koma ana a anthuwo sadaŵaphe,
6
potsata zimene zidalembedwa m'malamulo a m'buku la Mose, m'mene Chauta adalamula kuti, “Atate sadzaphedwa chifukwa cha ana ao, kapena ana kuphedwa chifukwa cha atate ao. Koma aliyense adzafera machimo ake.”
7
Tsono Amaziya adaphanso Aedomu okwanira 10,000 ku chigwa cha Mchere, nalanda mzinda wa Sela, ndipo adautchula dzina lakuti Yokitele, ndipo dzina lake ndi lomwelo mpaka pano.
8
Nthaŵi ina Amaziya adatuma amithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi, mdzukulu wa Yehu, mfumu ya ku Israele, kukanena momputa kuti, “Ubwere kuno, tidzaonane maso ndi maso.”
9
Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adabweza mau kwa Amaziya, mfumu ya ku Yuda, kuti, “Padangotere, mtungwi wa ku Lebanoni udaatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amkwatire.’ Koma chilombo cha ku Lebanoni chidadzera pomwepo, nkuupondereza mtungwiwo.
10
Inde iwe wagonjetsa Edomu, ndipo tsopano ukudzikuza. Badzitamira kupambana kwakoko, koma ai tsono khala kwanu komweko. Bwanji ukufuna kuutsa mavuto dala? Bwinotu ungagwe, iweyo pamodzi ndi anthu a ku Yuda.”
11
Koma Amaziya sadasamaleko zimenezi. Motero Yehowasi mfumu ya ku Israele adapita kukamenyana nkhondo ndi Amaziya mfumu ya ku Yuda ku Betesemesi m'dziko la Yuda.
12
Anthu a ku Yuda adagonjetsedwa ndi a ku Israele, ndipo wankhondo aliyense adathaŵira kwao.
13
Tsono ku Betesemesiko Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adagwirako Amaziya, mfumu ya ku Yuda, mwana wa Yowasi, mdzukulu wa Ahaziya, nabwera naye ku Yerusalemu. Ndipo Yehowasi adagumula khoma la Yerusalemu mamita 200, kuyambira ku chipata cha Efuremu mpaka ku chipata Chapangodya.
14
Pamenepo adalanda golide ndi siliva yense, ndi ziŵiya zonse zimene adazipeza m'Nyumba ya Chauta ndi m'nyumba zosungira chuma cha mfumu. Adagwiranso anthu ena ngati chikole, nabwerera ku Samariya.
15
Ntchito zina zonse za Yehowasi, makamaka za mphamvu zake, ndi za m'mene ankamenyerana nkhondo ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
16
Ndipo Yehowasi adamwalira naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo, mafumu a ku Israele ku Samariya. Ndiye Yerobowamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
17
Amaziya mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, adakhala moyo zaka 15 atafa Yehowasi, mwana wa Yehowahazi, mfumu ya ku Israele.
18
Tsono ntchito zina zonse zimene adachita Amaziya zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
19
Ndiye kuti anthu ena adaapangana zomchita chiwembu Amaziyayo ku Yerusalemu, iye nkuthaŵira ku Lakisi. Adani akewo adatuma anthu omlondola, nakamphera komweko.
20
Tsono adamtengera pa akavalo, nakamuika ku Yerusalemu m'manda momwe adaikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide.
21
Pamenepo anthu onse a ku Yuda adatenga Azariya, mwana wake, namlonga ufumu m'malo mwa Amaziya bambo wake. Azariyayo anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu.
22
Azariya adagonjetsa mzinda wa Elati naumanganso nkuubwezera ku dziko la Yuda, bambo wake atamwalira.
23
Chaka cha 15 cha ufumu wa Amaziya, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, Yerobowamu mwana wa Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adaloŵa ufumu ku Samariya, ndipo adalamulira zaka 42.
24
Iyeyo ankachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa zonse zimene ankachita kholo lake lija Yerobowamu, mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.
25
Adalandanso madera ena amene kale anali a dziko la Israele, kuyambira ku chipata cha Hamati kumpoto mpaka kumwera kukafika ku Nyanja ya Araba. Motero zidachitikadi zimene Chauta, Mulungu wa Israele, adaalankhula kudzera mwa Yona mtumiki wake, mwana wa Amitai, mneneri wa ku Gatihefere.
26
Chauta adaona kuti mavuto a Aisraele anali oopsa. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotsala, kapolo kapena mfulu, woti angaŵathandize Aisraelewo.
27
Koma Chauta sadaanena kuti adzafafaniza ufumu wa Israele pa dziko lapansi ai. Motero adaŵapulumutsa Aisraele kudzera mwa Yerobowamu mwana wa Yehowasi.
28
Tsono ntchito zina zonse za Yerobowamu, makamaka za mphamvu zake, za m'mene ankamenyera nkhondo, ndiponso za m'mene adagonjetsera mzinda wa Damasiko ndi wa Hamati naibwezeranso mizindayo ku Israele, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
29
Ndipo Yerobowamu adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo, mafumu a ku Israele. Tsono Zekariya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25