bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 8
2 Kings 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 9 →
1
Ndiye kuti Elisa anali atauza mai amene adaamuukitsira mwana wake uja kuti, “Nyamuka upite pamodzi ndi a pabanja pako, ukakhale nawo kulikonse kumene ungathe kukakhala, pakuti Chauta akubweretsa pa dziko njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri.”
2
Motero maiyo adanyamuka, ndipo adachitadi monga momwe munthu wa Mulungu uja adaanenera. Adapita pamodzi ndi a pabanja pake, nakakhala nawo ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziŵiri.
3
Tsono zitatha zaka zisanu ndi ziŵirizo, mai uja adabwerako ku dziko la Afilisti kuja, ndipo adapitanso kwa mfumu ya ku Israele kukafunsa za nyumba yake ndi munda wake.
4
Atafika kwa mfumu, adapeza mfumuyo ikulankhula ndi Gehazi, mtumiki wa munthu wa Mulungu uja, nimafunsa kuti, “Tandiwuza zonse zikuluzikulu zimene Elisa wachita.”
5
Pamene mtumikiyo ankauza mfumuyo m'mene Elisa adaukitsira anthu akufa, mkazi uja, amene mwana wake Elisa adamuukitsira, adadzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake. Pamenepo Gehazi adati, “Inu mbuyanga mfumu, pano pali mai, ndipo mwana wake ndi uyu amene Elisa adamuukitsa.”
6
Mfumu itamufunsa maiyo, iyeyo adaifotokozera kuti Elisa adaukitsadi mwana wake. Choncho mfumu ija idamuikira nduna maiyo niiwuza kuti, “Umbwezere zonse zimene zidaali zake, pamodzi ndi phindu lonse lochokera ku zokolola za kumunda kwake, kuyambira tsiku limene adachoka mpaka tsopano lino.”
7
Tsiku lina Elisa adapita ku Damasiko, pa nthaŵi imene Benihadadi mfumu ya ku Siriya ankadwala. Mfumuyo itamva kuti kwabwera munthu wa Mulungu,
8
idauza Hazaele nduna yake yaikulu kuti, “Tenga mphatso, upite kukakumana naye munthu wa Mulunguyo. Tsono upemphe nzeru kwa Chauta kudzera mwa iyeyo kuti, ‘Kodi mfumu idzachira matenda ameneŵa?’ ”
9
Motero Hazaele adapita kukakumana ndi mneneri Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso ndi zinthu zokoma zosiyanasiyana za ku Damasiko. Atafika, adakaima pamaso pa Elisa, munthu wa Mulungu uja, nati, “Munthu wanu Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, wandituma kuti ndikufunseni kuti, kodi ati adzachira?”
10
Elisa adayankha kuti, “Chauta wandiwonetsa kuti adzafa, komabe pita ukamuuze kuti adzachira.”
11
Atatero, Elisa adamuyang'ana kwambiri Hazaele mpaka adachita manyazi. Apo Elisayo adayamba kulira.
12
Tsono Hazaele adamufunsa kuti, “Mbuyanga, mukuliranji?” Iyeyo adayankha kuti, “Chifukwa ndikudziŵa zoipa zimene mudzaŵachita Aisraele. Mudzatentha malinga ao ankhondo ndipo mudzapha ankhondo ao ambiri. Mudzapondereza tiana tao, ndipo mudzang'amba akazi ao apakati.”
13
Apo Hazaele adafunsa kuti, “Kodi kapolo wanune amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita zinthu zazikulu zoterezi?” Elisa adayankha kuti, “Chauta wandiwonetsa kuti iweyo udzakhala mfumu ya Asiriya.”
14
Pomwepo Hazaeleyo adasiyana naye Elisa, napita kwa mbuyake. Mbuyakeyo adamufunsa kuti, “Kodi Elisa wakuuza zotani?” Hazaele adayankha kuti, “Inuyo muchira ndithu.”
15
Koma m'maŵa mwake, Hazaele adatenga chofunda nachiviika m'madzi nkuchiphimba kumaso kwa mfumu, ndipo mfumu ija idafa. Motero Hazaele adaloŵa ufumu m'malo mwake.
16
Chaka chachisanu cha ufumu wa Yoramu, mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israele, Yehoramu, mwana wa Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adayambapo kulamulira dziko la Yuda.
17
Yehoramu anali ndi zaka 32 pamene ankaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu.
18
Tsono Yehoramuyo ankatsata makhalidwe oipa a mafumu a ku Aisraele, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, pakuti adaakwatira mwana wa Ahabu. Tsono ankachita zoipa zili zonse pamaso pa Chauta.
19
Komabe Chauta sadafune kuwononga Yuda, chifukwa cha Davide mtumiki wake, popeza kuti Chauta adaalonjeza kuti adzampatsa nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
20
Pa nthaŵi yakeyo anthu a ku Edomu adaukira ulamuliro wa Yuda ndipo adadzisankhira mfumu yao.
21
Tsono Yehoramu adapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse ankhondo. Adanyamuka usiku nakaŵakantha Aedomu amene adaamzinga iyeyo pamodzi ndi atsogoleri a magaleta ake. Ankhondo ake onse adathawa napita kwao.
22
Motero Aedomu ngoukira ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Pa nthaŵi imeneyo mzinda wa Libina nawonso udaukira ulamuliro wake.
23
Tsono ntchito zina za Yehoramu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
24
Choncho Yehoramu adamwalira naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Ndipo Ahaziya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
25
Pa chaka cha 12 cha ufumu wa Yoramu, mwana wa Ahabu, mfumu ya ku Israele, Ahaziya mwana wa Yehoramu, mfumu ya ku Yuda, adayamba kulamulira.
26
Ahaziya anali ndi zaka 22 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira chaka chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Ataliya, mdzukulu wake wa Omuri mfumu ya ku Israele.
27
Iyeyonso ankatsata chitsanzo choipa cha banja la Ahabu. Adachita zoipa pamaso pa Chauta monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, poti anali mkamwini m'banja la Ahabu lomwelo.
28
Tsono mfumu Ahaziya adapita pamodzi ndi Yoramu, mwana wa Ahabu, kuti akamenyane nkhondo ndi Hazaele, mfumu ya ku Siriya, ku Ramoti ku Giliyadi. Kumeneko Asiriya adalasa Yoramu.
29
Tsono Yoramuyo adabwerera napita ku Yezireele, kuti akamchiritse mabala amene Asiriya adaamlasa ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaele mfumu ya ku Siriya. Motero Ahaziya, mwana wa Yehoramu, mfumu ya ku Yuda, adapita ku Yezireele kukazonda Yoramu mwana wa Ahabu, chifukwa chakuti ankadwala.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25