bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 16
2 Kings 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 17 →
1
Chaka cha 17 cha ufumu wa Peka mwana wa Remaliya, Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu.
2
Ahazi anali wa zaka 20 pamene adaloŵa ufumu ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Iyeyo sadachite zolungama pamaso pa Chauta monga m'mene Davide kholo lake ankachitira.
3
Koma adatsata zitsanzo zoipa za mafumu a ku Israele. Adapereka mwana wake wamwamuna ngati nsembe yopsereza potsatira miyambo yonyansa ya anthu a mitundu ina imene Chauta adaaipirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraele.
4
Ndipo ankapereka nsembe ndi namafukiza lubani ku akachisi opembedzerako mafano, pa mapiri ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.
5
Tsono Rezini mfumu ya ku Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya ku Israele adabwera kudzathira nkhondo Yerusalemu namzinga Ahazi ndi zithando zankhondo, koma sadathe kumgonjetsa.
6
Nthaŵi imeneyo Rezini mfumu ya ku Edomu adapirikitsa Ayuda ku Elati, nalanda mzindawo, kuubwezera kwa Aedomu, ndipo iwo adakhala kumeneko mpaka lero lino.
7
Pamenepo Ahazi adatuma amithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya kukanena kuti, “Ine ndine mwana wanu ndiponso mtumiki wanu. Bwerani mudzandipulumutse kwa mfumu ya ku Siriya ndi kwa mfumu ya ku Israele, amene akundithira nkhondo.”
8
Ndipo Ahazi adatenga siliva ndi golide amene adampeza m'Nyumba ya Chauta ndi mosungira chuma cha ku nyumba ya mfumu, namtumiza kwa mfumu ya ku Asiriya kuti zikhale ngati mphatso.
9
Tsono mfumu ya ku Asiriya idamvera Ahazi ndipo idakathira nkhondo Damasiko nilanda mzindawo ndi kupha Rezini. Anthu ake idaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Kiri.
10
Pamene mfumu Ahazi adapita ku Damasiko kuti akakumane ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya, adaonako guwa kumeneko. Tsono adatumizira wansembe Uriya chitsanzo chake cha guwalo ndi maonekedwe ake, osasiyapo nkanthu komwe.
11
Ndiye wansembe Uriya adamanga guwalo, Mfumu Ahazi asanafike kuchokera ku Damasiko. Adalimanga potsata chitsanzo chimene Ahazi adaatumiza kuchokera ku Damasiko.
12
Mfumu itabwera kuchokera ku Damasiko, nipenya guwa lija, idasendera pafupi ndi guwalo ndi kukwera kuguwako.
13
Tsono mfumuyo idapereka nsembe yopsereza ndi chopereka cha chakudya. Idathiranso nsembe yake yachakumwa, ndipo idawaza magazi a nsembe yake yamtendere paguwapo.
14
Kenaka mfumu Ahazi adachotsa guwa lamkuŵa limene linali lomangira Chauta, pakati pa guwa lake ndi Nyumba ya Chauta, ndipo adalisuntha nakalikhazika chakumpoto kwa guwa lakelo.
15
Kenaka mfumuyo idalamula wansembe kuti, “Pa guwa lalikululo uperekepo nsembe zopsereza zam'maŵa, ndiponso chopereka chamadzulo cha chakudya. Uziperekanso nsembe zopsereza ndi nsembe zaufa za mfumu, ndiponso za anthu a m'dziko monsemo, pamodzi ndi zopereka za chakumwa. Ndipo pa nsembezo uwazepo magazi onse a nsembe zopsereza ndi a nsembe zonse. Koma guwa lamkuŵalo ndidzaligwiritsa ntchito poombeza.”
16
Tsono wansembe Uriya adachita zonsezo, monga momwe mfumu Ahazi adaalamulira.
17
Pambuyo pake mfumu Ahazi adamasula mafulemu a maphaka, nachotsapo beseni. Ndipo chimbiya chimene chinali pamwamba pa ng'ombe zamkuŵa adachitsitsa ndi kuchikhazika pa maziko amiyala.
18
Ndipo chifukwa chofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya, adachotsa kadenga ka pamwamba pa mpando waufumu kamene anali atakamanga m'kati mwa Nyumba ya Chauta, ndiponso adatseka khomo la panja pamene mfumu inkaloŵera m'Nyumbamo.
19
Tsono ntchito zina za Ahazi pamodzi ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
20
Ahazi adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25