bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 4
2 Kings 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 5 →
1
Tsiku lina mkazi wa mmodzi wa m'gulu la aneneri adapita kwa Elisa. Adampempha mokweza kuti, “Mwamuna wanga, amene anali mtumiki wanu, adamwalira. Ndipo inu mukudziŵa kuti mtumiki wanuyo ankaopa Chauta. Tsono kwafika munthu amene mwamuna wanga adakongola zinthu zake, ndipo akuti atenge ana anga aŵiri, kuti akhale akapolo ake chifukwa cha ngongoleyo.”
2
Elisa adafunsa maiyo kuti, “Nanga mukuti ineyo nditani? Tanenani, muli ndi chiyani m'nyumba mwanu?” Maiyo adayankha kuti, “Mdzakazi wanune ndilibe nkanthu komwe m'nyumba, koma kambiya ka mafuta basi.”
3
Apo Elisayo adamuuza kuti, “Pitani, kabwerekeni mitsuko yambirimbiri kwa anzanu.
4
Mukaloŵe m'nyumba mwanu, mukadzitsekere momwemo inuyo ndi ana anuwo. Ndipo mukatsanyulire mafuta m'mbiya zonsezo. Ina ikadzaza, mukaiike pambali.”
5
Mai uja adachoka kwa Elisayo, nakadzitsekera ndi ana ake aŵiri aja. Tsono iyeyo ankati akathira mafuta m'mbiya nidzaza, ana ake ankabwera ndi mbiya ina.
6
Mbiyazo zitadzaza zonse, maiyo adauza mwana wake kuti, “Bwera ndi inanso mbiya.” Koma mwanayo adauza mai wake kuti, “Palibenso ina.” Pomwepo mafuta aja adaleka kutuluka m'kambiya kaja.
7
Tsono mai uja adapita kukafotokozera Elisa, munthu wa Mulungu uja. Ndipo Elisayo adauza maiyo kuti, “Mai, pitani mukagulitse mafutawo, ndipo mukabweze ngongole zanuzo. Tsono ndalama zotsala zikhale zothandizira inu ndi ana anu.”
8
Tsiku lina Elisa adapita ku Sunemu kumene kunkakhala mai wina wachuma. Maiyo adaumiriza Elisayo kuti adye chakudya kunyumba kwake. Motero Elisa ankati akamadzera njira imeneyo, nthaŵi zonse ankapatuka kunyumbako nkukadya nao.
9
Tsono maiyo adauza mwamuna wake kuti, “Tsopano ndikudziŵa kuti munthu amene amadutsa pano kaŵirikaŵiriyu ngwoyera wa Mulungu.
10
Tiyeni timmangire kachipinda kakang'ono kam'mwamba, ndipo timuikiremo bedi, tebulo, mpando ndi nyale, kuti nthaŵi zonse akatichezera, azitha kumakakhala m'menemo.”
11
Tsiku lina Elisa uja adafika ku Sunemu, nakaloŵa m'kachipinda kam'mwamba kaja kuti akapumule m'menemo.
12
Pambuyo pake adauza mtumiki wake Gehazi kuti aitane maiyo. Gehazi adamuitana maiyo, ndipo adafika kwa Elisa.
13
Elisa adalamula Gehazi kuti amuuze maiyo kuti, “Ndithu mwavutika potichitira zonsezi. Nanga ife tikuchitireni chiyani? Kodi muli ndi mau oti tikakunenereni kwa mfumu, kapena kwa mtsogoleri wankhondo?” Maiyo adayankha kuti, “Ine ndimakhala mwaufulu pakati pa anthu a mtundu wanga.”
14
Ndipo Elisa adafunsanso Gehazi kuti, “Nanga tsono timchitire chiyani?” Gehazi adayankha kuti, “Pepani, mai ameneyu alibe mwana wamwamuna, ndipo mwamuna wake ngwokalamba.”
15
Elisa adati, “Tamuitananso.” Ndipo atamuitana, maiyo adaima pa khomo.
16
Tsono Elisa adauza mai uja kuti, “Pa nthaŵi yonga yomwe ino chaka chamaŵachi, mudzakhala mukululuza mwana wamwamuna.” Ndipo maiyo adati, “Pepani mbuyanga, inu munthu wa Mulungu, musandinamizetu ine mdzakazi wanu.”
17
Koma mai uja adaimadi ndipo chaka chotsatira, nthaŵi ngati yomweyo, adabala mwana wamwamuna, monga momwe Elisa adaamuuzira.
18
Mwana uja atakula, tsiku lina adapita kwa bambo wake amene ankayang'anira anthu odula tirigu.
19
Mwadzidzidzi mwanayo adalira mofuula kwa bambo wake kuti, “Mayo! Mutu wanga ine! Mutu wanga ine!” Bambo wake uja adauza wantchito wake kuti, “Kampereke kwa mai wake.”
20
Adamunyamula, nakampereka kwa mai wake. Mwanayo adakhala pamiyendo pa mai wake mpaka masana, basi nkumwalira.
21
Pomwepo mkazi uja adanyamula mwana wake nakwera ku chipinda cham'mwamba chija, nakamgoneka pa bedi la Elisa, mtumiki wa Mulungu uja, nkumtsekera momwemo, iye nkutuluka.
22
Tsono adaitanitsa mwamuna wake, namuuza kuti, “Tumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu wa Mulungu uja, nkubwerakonso.”
23
Apo mwamuna wakeyo adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukupita kwa iyeyo lero? Lerotu si tsiku lokhala mwezi, kapenanso tsiku la Sabata ai.” Mai uja adati, “Palibe kanthu.”
24
Pompo maiyo adaika chishalo nakwera bulu, ndipo adauza wantchitoyo kuti, “Thamangitsa buluyo. Usaleze mpaka ntakuuza.”
25
Motero adayenda nakafika kwa Elisa, munthu wa Mulungu uja, ku phiri la Karimele. Tsono mneneri Elisa ataona kuti mai uja akudza, adauza Gehazi mtumiki wake kuti, “Taona patsidyapo, Msunamu uja akubwera.
26
Thamanga msanga ukamchingamire, ndipo ukamufunse kuti, ‘Kodi nkwabwino? Kodi mwamuna wanu ali bwino? Nanga mwana uja ali bwino?’ ” Mkaziyo adayankha Gehazi kuti, “Inde, nkwabwino.”
27
Tsono atafika kuphiriko kwa Elisa munthu wa Mulungu uja, maiyo adagwada, nagwira mapazi a Elisa. Gehazi adadza kuti amkankhe. Koma Elisa adati, “Mleke, kodi sukuwona kuti ali pa mavuto aakulu? Chauta wandibisira ine zimenezi, sadandiwuze.”
28
Tsono mkaziyo adati, “Kodi inu mbuyanga, ine ndidaakupemphani mwana? Kodi suja ndidaakuuzani kuti musandinamize?”
29
Elisa adauza Gehazi kuti, “Vala lamba wako, fulumira, utenge ndodo yanga ndipo upite. Ukakumana ndi munthu wina aliyense pa njira, usampatse moni, ndipo wina aliyense akakupatsa moni, usayankhe. Tsono ukagoneke ndodo yangayi pa nkhope ya mwanayo.”
30
Apo mai wake wa mwana uja adati, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine ndiye sindikusiyani ai.” Tsono Elisa adanyamuka natsatira maiyo.
31
Gehazi adatsogolako, ndipo adakaigoneka ndodoyo pa nkhope ya mwana uja, koma sipadamveke mau kapena kuwoneka chizindikiro china cha moyo. Choncho Gehaziyo adangobwerera kukakumana ndi Elisa, ndipo adamuuza kuti, “Mwana uja sadauke ai.”
32
Elisa ataloŵa m'chipinda muja adaona mwana wakufayo atamgoneka pabedi pake.
33
Motero adatseka chitseko nkukhala okha aŵiriwo, ndipo adayamba kupemphera kwa Chauta.
34
Tsono adakamgonera mwanayo, nakhudzitsa pakamwa pake ndi pakamwa pa mwanayo. Ndipo m'mene ankadzitambalitsa choncho pa mwanayo, thupi la mwana uja lidayamba kufunda.
35
Elisayo adadzuka nayenda kamodzi cha uku ndi uku m'chipindamo. Kenaka adakamgoneranso mwana uja, ndipo mwanayo adayetsemula kasanunkaŵiri, nkuphenyula maso.
36
Pomwepo Elisa adaitana Gehazi nati, “Muitane mai uja.” Iye adamuitana maiyo. Ndipo atabwera, Elisayo adati, “Nayu mwana wanu.”
37
Pamenepo maiyo adagwada pa mapazi a Elisa, naŵeramitsa mutu wake pansi. Kenaka adanyamula mwana wake uja, natuluka pa bwalo.
38
Pambuyo pake Elisa adabwereranso ku Giligala, ndipo m'dzikomo munali njala. Tsiku lina Elisa ankaphunzitsa gulu la aneneri, ndipo patapita nthaŵi, adauza mtumiki wake kuti, “Ikapo nkhali yaikulu pa moto, uŵaphikire chakudya a m'gulu la aneneriŵa.”
39
Mmodzi mwa aneneriwo adapita ku thengo kukathyola ndiwo. Kumeneko adakapezako mpesa wakuthengo nathyola zipatso zake kudzaza nsalu yake. Adabwera nazo naziduladula, nkuziika m'nkhali muja, osadziŵa kuti nchiyani.
40
Tsono adapakula naŵapatsa anthuwo kuti adye. Koma pamene adayamba kudya chakudyacho, anthuwo adafuula kuti, “Inu, munthu wa Mulungu, muli dziphe m'nkhalimu.” Choncho sadathe kudya chakudyacho.
41
Tsono Elisa adaŵauza kuti, “Bwerani ndi ufa.” Elisayo adathira ufawo m'nkhali nati, “Apakulireninso anthu chakudyacho kuti adye.” Ndipo adapeza kuti munalibenso zoopsa m'nkhali muja.
42
Tsiku lina munthu wina wochokera ku Baala-Salira adabwera kwa Elisa atamtengerako buledi wopangidwa ndi zokolola zatsopano, mitanda makumi aŵiri ya buledi wa barele ndiponso ngala zatirigu zatsopano. Zonsezi adaazitengera m'thumba mwake. Tsono Elisa adati, “Agaŵire anthu chakudyachi kuti adye.”
43
Koma wantchito wake adamufunsa kuti, “Kodi chakudya chimenechi ndingachigaŵe motani kwa anthu 100 onseŵa?” Elisayo adanenanso kuti, “Apatseni anthuwo, pakuti Chauta akunena kuti, ‘Anthuwo adzadya ndipo chakudyacho chidzatsalako.’ ”
44
Motero wantchitoyo adaŵagaŵira anthuwo chakudyacho, naadya, ndipo adasiyako, monga momwe Chauta adaanenera.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25