bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 25
2 Kings 25
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
1
Tsono Zedekiya adapandukira mfumu ya ku Babiloni. Ndiye pa chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Zedekiyayo, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adabwera ndi ankhondo ake onse, kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Adauzinga ndi zithando zankhondo ponseponse.
2
Motero mzindawo udaazingidwa ndi zithandozo mpaka chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya.
3
Tsono pa tsiku lachisanu ndi chinai pa mwezi wachinai chaka chimenecho, pamene njala inali itakula kwambiri mumzindamo, kotero kuti anthu analibiretu chakudya m'dzikomo,
4
malinga a mzindawo adabooledwa. Pamenepo mfumu Zedekiya adathaŵa usiku pamodzi ndi ankhondo ake onse kutulukira pa chipata cha pakati pa makoma aŵiri, pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababiloni anali atauzinga mzinda wonsewo. Ndipo adaloŵera cha ku Araba.
5
Koma gulu lankhondo la ku Babiloni lidamlondola mfumu Zedekiya nkukamgwirira m'zigwa za ku Yeriko. Ankhondo ake adabalalika namsiya.
6
Apo a ku Babiloni aja atamgwira Zedekiyayo, adapita naye kwa Nebukadinezara, ku Ribula. Komweko Nebukadinezarayo adagamula mlandu wa Zedekiya uja.
7
Pompo adapha ana a Zedekiya iyeyo akupenya, ndipo adamkolowola maso Zedekiyayo, nammanga ndi maunyolo, nkupita naye ku Babiloni.
8
Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mwezi, chaka cha 19 cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, mmodzi mwa alangizi ake, adadza ku Yerusalemu.
9
Ndipo adatentha Nyumba ya Chauta, nyumba ya mfumu, ndi nyumba zina zonse za ku Yerusalemu. Adatentha nyumba yaikulu iliyonse.
10
Tsono gulu lonse lankhondo la ku Babiloni limene linali ndi mkulu wa asilikali uja, lidagumula malinga ozinga Yerusalemu.
11
Anthu ena onse amene adaatsala mumzindamo, ndi ena amene adaathaŵa kupita kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi ena otsala, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali uja, adaŵatenga kupita nawo ku Babiloni.
12
Koma mkulu wa asilikaliyo adasiyako anthu ena osauka kwambiri am'dzikomo, kuti azisamala minda yamphesa ndi minda ina.
13
Ankhondo a ku Babiloni adaphwanya nsanamira zamkuŵa za m'Nyumba ya Chauta ndiponso maphaka ndi chimbiya chamkuŵa, ndipo adatenga mkuŵawo, napita nawo ku Babiloni.
14
Ankhondowo adachotsanso mbiya, zoolera phulusa, zozimira nyale, mbale zofukizira lubani kudzanso ziŵiya zonse zamkuŵa zimene ankagwiritsira ntchito ku Nyumba ya Chauta.
15
Mkulu wa asilikali uja adatenganso ziwaya zosonkhapo moto ndiponso mbale zowazira madzi, ndi zina zonse zagolide ndi zasiliva.
16
Kunena za nsanamira ziŵiri zija, chimbiya, ndi maphaka zimene Solomoni adaapangira Nyumba ya Chauta, kulemera kwake kwa mkuŵa wa zonsezo kunali kosaŵerengeka.
17
Msinkhu wa nsanamira imodzi unali mamita asanu ndi atatu, ndipo pamwamba pake panali mutu wamkuŵa. Msinkhu wa mutuwo unali mita imodzi ndi theka. Ukonde wake pamodzi ndi makangaza ake, zonsezo zinali zamkuŵa, ndipo zinali pamwamba pa mutu uja mozungulira. Nsanamira yachiŵiri inali yolingana ndi inayo, ndipo inalinso ndi ukonde.
18
Tsono mkulu wa asilikali uja adagwira Seraya mkulu wa nsembe ndi Zefaniya wachiŵiri kwa mkulu wa ansembe, ndi alonda atatu apakhomo.
19
Mumzindamo adagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo ndiponso anthu asanu amene anali aphungu a mfumu mumzindamo. Adagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo amene ankapemba anthu am'dzikomo ndiponso akuluakulu ena 60, amene anali mumzindamo.
20
Nebuzaradani, mkulu wa asilikali uja, adaŵatenga onsewo napita nawo kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula.
21
Ndipo mfumuyo idalamula kuti aŵakwapule ndi kuŵaphera ku Ribula, m'dziko la Hamati. Umu ndimo m'mene Ayuda adatengedwera ukapolo kuŵachotsa ku dziko lao.
22
Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adaika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti akhale kazembe woyang'anira anthu otsala aja amene Nebukadinezarayo adaŵasiya ku dziko la Yuda.
23
Tsono atsogoleri Achiyuda ndi ankhondo ao onse amene anali atathaŵa, atamva kuti mfumu ya ku Babiloni idaika Gedaliya kuti akhale kazembe, adadza kwa Gedaliya ku Mizipa, iwo pamodzi ndi anthu ao. Atsogoleriwo maina ao anali aŵa: Ismaele mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti wa ku Netofa ndi Yazaniya mwana wa Maakati.
24
Iwowo pamodzi ndi anthu ao, Gedaliya adaŵalonjeza molumbira kuti, “Musaope chifukwa cha atsogoleri a Ababiloniwo. Khalani m'dzikomu, muzimvera mfumu ya ku Babiloni, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.”
25
Koma pa mwezi wa chisanu ndi chiŵiri Ismaele mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa banja laufumu, adadza pamodzi ndi anthu khumi. Adadzathira nkhondo Gedaliya, napha iyeyo ndiponso Ayuda ndi anthu a ku Babiloni amene anali naye limodzi ku Mizipa.
26
Pamenepo Aisraele onse, olemera ndi osauka omwe, pamodzi ndi atsogoleri ankhondo, adanyamuka kupita ku Ejipito, poti ankaopa Ababiloni.
27
Pa chaka cha 37 cha kutengedwa ukapolo Yehoyakini mfumu ya ku Yuda, pa mwezi wa 12 pa tsiku la 27 la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babiloni, pa chaka choyamba cha ufumu wake, adakomera mtima Yehoyakiniyo nammasula m'ndende.
28
Adamchitira zabwino, namkweza kupambana mafumu ena onse amene anali naye limodzi ku Babiloni.
29
Motero Yehoyakini adaloledwa kuchotsa zovala zakundende, ndi kumadya ku tebulo la mfumu masiku onse a moyo wake.
30
Mfumuyo inkampatsa phoso tsiku lililonse pa moyo wake wonse.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25