bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Kings 7
2 Kings 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 8 →
1
Elisa adayankha nati, “Mverani, zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, ‘Maŵa pa nthaŵi ngati yomwe ino makilogramu atatu a ufa wosalala adzaŵagulitsa pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu asanu ndi limodzi a barele adzaŵagulitsanso pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha ku Samariya’ ”
2
Tsono phungu wokhulupirika wa mfumu adafunsa munthu wa Mulungu uja kuti, “Ngakhale Chauta mwiniwake atachita kutikhuthulira mvula yochuluka chotani, zoterezi nkuchitika ngati?” Koma Elisa adati, “Ndithu udzaziwona zimenezo ndi maso ako, koma iweyo sudzazilaŵa.”
3
Nthaŵi imeneyo panali anthu akhate anai amene ankakhala pa chipata. Iwowo adayamba kufunsana kuti, “Chifukwa chiyani tikungotambalala pano kumangodikira imfa?
4
Tikati tiyeni tiloŵe mumzindamu, njala ili m'menemo kumene, ndiye tikaferamo. Komanso tikangotambalala pompano, tifabe. Tsono tiyeni tingopita ku zithando za Asiriya. Akatileka ndi moyo, chabwino, koma akatipha, palibe kanthu.”
5
Motero adanyamuka ndi chisisira kupita ku zithando za Asiriya. Koma atafika ku malire a zithando za Asiriya, adaona kuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe.
6
Chauta anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lankhondo pakati pa ankhondo a Asiriya. Ndiye iwowo adayamba kuuzana kuti, “Tamvani phokosolo, mfumu ya ku Israele yalemba mafumu a Ahiti ndi a Aejipito kuti adzatithire nkhondo!”
7
Motero adathaŵa ndi chisisila, nasiya mahema, akavalo, abulu ndiponso katundu wao yense monga momwe adaaliri, nathaŵa kuti apulumutse moyo wao.
8
Choncho akhate aja atafika ku malire a zithandozo, adakaloŵa mu hema limodzi, ndipo adadya ndi kumwa. Atatero adatengako siliva, golide ndi zovala, nakazibisa. Pambuyo pake adabwerera nakaloŵa mu hema linanso, natengamo zinthu, nkukazibisanso.
9
Kenaka akhate aja adayamba kuuzana kuti, “Ife sitikuchita bwinotu pamenepa. Lero ndilo tsiku limene tili ndi uthenga wabwino kwambiri! Tikakhala chete ndi kumadikira mpaka m'maŵa, tidzalangidwa. Nchifukwa chake tsono tiyeni tikauze nduna za mfumu.”
10
Motero adapita ku Samariya nakaitana alonda a pa chipata cha mzinda naŵauza kuti, “Ife tidaapita ku zithando za Asiriya, ndipo tidangoona kuti kulibe munthu ndi mmodzi yemwe. Ngakhale kumva mau sitidamve, koma tidangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire, ndiponso mahema monga momwe adaaliri.”
11
Tsono alonda apachipata aja adalengeza uthengawo ndipo okhala kunyumba kwa mfumu adaumva.
12
Pamenepo mfumu idadzuka usiku nikauza nduna zake kuti, “Ndikuuzeni zimene Asiriya atikonzera. Iwowo akudziŵa kuti ife tili ndi njala. Nchifukwa chake atuluka m'zithando kuti akabisale ku thengo. Choncho tikangotuluka mumzinda muno, iwowo atigwira amoyo ndipo aloŵa mumzinda muno.”
13
Koma mmodzi mwa nduna zake adati, “Anthu a mumzinda muno posachedwa adzatsirizikanso monga Aisraele onse amene afa kaleŵa. Ndiye ife tiyeni tisankhe ena kuti atenge akavalo asanu amene atsalawo, tiŵatume kuti akaone.”
14
Motero adasankha anthu aŵiri okwera pa akavalo, ndipo mfumuyo idaŵatuma kuti akalondole gulu la ankhondo la Asiriya. Idati, “Pitani mukaone chimene chachitika.”
15
Anthu aja adaŵalondola Asiriya mpaka ku Yordani. Ndipo ndithu m'njira monse ankapeza zovala zili mbwee ndiponso katundu amene Asiriya ankapita nataya chifukwa cha kuthaŵa mofulumira. Pomwepo amithengawo adabwerera, nakauza mfumu.
16
Tsono anthu a mu Samariya adatuluka nakafunkha ku zithando za Asiriya. Motero makilogramu atatu a ufa wosalala ankaŵagulitsadi pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu asanu ndi limodzi a barele ankaŵagulitsanso chimodzimodzi potsata m'mene adaanenera Chauta.
17
Pamene zinkachitika zimenezi, nkuti mfumu itaika phungu wake wokhulupirika uja kuti akhale wolamulira pa chipata. Koma anthu adapondereza phunguyo kuchipata kuja, kotero kuti adafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu adaanenera pamene mfumu idaapita kukamuwona.
18
Paja mneneri Elisa adaauza mfumu kuti, “Makilogramu asanu ndi limodzi a barele adzaŵagulitsa pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu atatu a ufa wosalala adzaŵagulitsanso pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva maŵa pa nthaŵi ngati yomwe ino ku chipata cha Samariya.”
19
Pamenepo phungu wokhulupirika uja adaayankha Elisa munthu wa Mulungu uja, kuti, “Ngakhale Chauta mwiniwake atachita kutikhuthulira mvula yochuluka chotani, zoterezi nkuchitika ngati?” Apo mpamene Elisa adaamuuza kuti, “Ndithu udzaziwona zimenezo ndi maso ako, koma iweyo sudzazilaŵa.”
20
Motero zidamchitikiradi, pakuti anthu adampondereza pa chipata ndipo adafera pomwepo.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25