bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 1
Joshua 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 2 →
1
Mose, mtumiki wa Chauta, atamwalira, Chauta adalankhula ndi mthandizi wake wa Moseyo, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, kuti,
2
“Mose, mtumiki wanga, wafa. Tsono iwe, konzeka tsopano pamodzi ndi Aisraele onseŵa, muwoloke mtsinje wa Yordaniwu, ndipo muloŵe m'dziko limene ndikuŵapatsalo.
3
Paliponse pamene muponde phazi lanu, ndakupatsani inu, monga momwe ndidalonjezera Mose.
4
Kuyambira ku chipululu kumwera, mpaka ku mapiri a Lebanoni kumpoto, kuchokeranso ku mtsinje waukulu wa Yufurate kuvuma, mpaka dziko lonse la Ahiti, kukafika ku Nyanja Yaikulu kuzambwe, lonseli lidzakhala dziko lanu.
5
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kukugonjetsa iwe Yoswa, nthaŵi yonse ya moyo wako. Ine ndidzakhala nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose, sindidzakusiya konse.
6
Ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima, chifukwa udzatsogolera anthu ameneŵa pokalandira dziko limene ndidalonjeza kwa makolo ao.
7
Komatu ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti usunge malamulo onse amene Mose mtumiki wanga adakupatsa. Usatayepo ndi kagawo kamodzi komwe, ndipo kulikonse kumene udzapite, udzapambana.
8
Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana.
9
Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
10
Pamenepo Yoswa adalamula atsogoleri a Aisraele naŵauza kuti,
11
“Pitani ku zithando zonse, mukauze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu, chifukwa atapita masiku atatu, mudzaoloka Yordani ndi kulandira dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.’ ”
12
Ndipo Yoswa adauza fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti,
13
“Kumbukirani zija zimene Mose, mtumiki wa Chauta, adakuuzani, kuti, ‘Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani dziko limeneli kuti likhale lanu.’
14
Tsono akazi anu pamodzi ndi ana anu atsalire m'dziko lino la kuvuma kwa Yordani limene Mose adakupatsani. Ng'ombe zanu zitsalenso, koma ankhondo okha pakati panupa ndiwo aoloke atatenga zida, apite kutsogolo kwa Aisraele anzanu kuti akaŵathandize.
15
Ndipo iwowo akadzalandira dzikolo ndi kukhazikikamo, pamenepo ndiye inu mudzabwerere ndi kudzakhala m'dziko lanu limene adakupatsani Mose, mtumiki wa Chauta, konkuno kuvuma kwa Yordani.”
16
Onsewo adayankha Yoswa kuti, “Zonse zimene mwatilamulazi tidzachita, ndipo kulikonse kumene mudzatitume, tidzapita.
17
Tidzakumverani monga momwe tidamverera Mose. Chauta, Mulungu wanu, akhale nanu, monga momwe adakhalira ndi Mose!
18
Aliyense wokangana ndi inu kapena wosamvera malamulo anu, adzaphedwa. Inu mukhale amphamvu, ndipo mulimbe mtima kwambiri.”
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24