bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 14
Joshua 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 15 →
1
Maiko amene Aisraele adalandira ku Kanani adagaŵidwa motere: Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mabanja a mafuko a Aisraele, onseŵa ndiwo adagaŵa maikowo, kugaŵira Aisraele.
2
Potsata zimene Mulungu adalamula Mose, dziko lonse lidagaŵidwa mwamaere kwa mafuko asanu ndi anai ndi theka.
3
Mose adagaŵira mafuko aŵiri ndi theka aja magawo ao a dziko kuvuma kwa Yordani, koma Alevi okha sadaŵagaŵire.
4
Tsono fuko la Yosefe adaligaŵa paŵiri, Manase ndi Efuremu. Alevi sadalandire gawo lililonse la dziko. Adangolandira mizinda kuti azikhalamo ndi timaiko todyetsamo zoŵeta zao.
5
Aisraelewo adangogaŵana dzikolo potsata zimene Chauta adaalamula Mose.
6
Anthu a fuko la Yuda adabwera kwa Yoswa ku Giligala. Kalebe mmodzi mwa iwowo, mwana wa Yefune Mkenizi, adauza Yoswa kuti, “Inu mukudziŵa zimene Chauta adauza Mose, munthu wa Mulungu uja, za inu ndi ine ku Kadesi-Baranea.
7
Nthaŵi imene ija ndinali ndi zaka makumi anai pamene Mose mtumiki wa Chauta adandituma kuchokera ku Kadesi-Baranea kukazonda dziko lija. Nditabwerako, ndidamuuzadi zoona zonse zimene ndidaona.
8
Komabe anthu amene anali nane pa ulendowo, adachititsa mantha anthu. Koma ine ndidamvera mokhulupirika Chauta, Mulungu wanga.
9
Pamenepo Mose adandilonjeza kuti, ‘Chifukwa choti wamvera mokhulupirika Chauta, Mulungu wanga, iweyo pamodzi ndi ana ako, udzalandiradi dziko limene walipondalo, kuti likhale choloŵa chako.’ ”
10
Kalebe adapitiriranso kunena kuti, “Koma tsopano, papita zaka 45 Chauta atauza kale Mose zimenezi. Taonani, ndili ndi zaka 85 tsopano,
11
komabe ndikadali ndi mphamvu lero, monga ndidaaliri muja, pamene Mose adandituma. Ndikadali wamphamvu, mwakuti ndingathe kumenya nkhondo ndithu, ndiponso ndingathe kuchita zina zonse.
12
Tsopano mundigaŵire dziko lamapiri lomwe Chauta adandilonjezeratu. Paja mudamva kuti Aanaki, anthu amphamvu, adalipodi kumeneko m'mizinda yao yamalinga. Komabe mwina Chauta adzakhala nane, ndipo ndidzaŵapirikitsa monga momwe Chauta adanenera.”
13
Pamenepo Yoswa adadalitsa Kalebe, mwana wa Yefune, nampatsa Hebroni kuti likhale dziko lake.
14
Mpaka lero lino dziko la Hebroni ndi la zidzukulu za Kalebe, mwana wa Yefune Mkenizi, poti adamvera mokhulupirika Chauta, Mulungu wa Aisraele.
15
Zisanachitike zimenezi, Hebroni ankatchedwa Kiriyati-Ariba. Arabayo ndiye anali wotchuka kopambana pakati pa Aanaki. Pambuyo pake m'dziko lonselo mudakhala mtendere.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24