bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 19
Joshua 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 20 →
1
Mabanja a Simeoni adalandiranso gawo lao, Yoswa atachita maere kachiŵiri. Dziko lake linali m'kati mwenimweni mwa dziko la mabanja a Yuda.
2
Ndipo lidaphatikiza Beereseba, Molada,
3
Hazara-Suwala, Bala, Ezemu,
4
Elitoladi, Betuli, Horoma,
5
Zikilagi, Betemari-Kaboti, Hazarasusa,
6
Betelebaoti ndiponso Saruheni. Yonse inalipo mizinda 13, pamodzi ndi midzi yake.
7
Panalinso Aini, Rimoni, Eteri ndi Asani. Yonse inalipo mizinda inai, pamodzi ndi midzi yake.
8
Imeneyi idaphatikizapo midzi yozungulira mizindayo, mpaka kukafika ku Baala-Tibere, ndiye kuti Rama wakumwera. Dziko limeneli ndi limene mabanja a fuko la Simeoni adalandira kukhala choloŵa chao.
9
Gawo la Simeoni lidatapidwa ku gawo la Yuda, popeza kuti gawo la Yuda lidaali lalikulu kwambiri. Choncho choloŵa cha Simeoni chidatapidwa pa choloŵa cha Yuda.
10
Mabanja a fuko la Zebuloni adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachitatu. Dziko limene adalandiralo lidakafika mpaka ku Saridi.
11
Tsono malirewo adakwera naloŵa kuzambwe ku Mareyala, nakafika ku Debeseti ndi ku mtsinje wa kuvuma kwa Yokoneamu.
12
Pa mbali ina ya Saridi adapita chakuvuma ku malire a Kisiloti-Tabori, mpaka ku Debarati, nakafika ku Yafiya.
13
Kuchokera kumeneko, adabzola naloŵa chakuvuma kumapita ku Gatihefere ndi ku Etikazini, kuloŵa ku Neya njira yaku Rimoni.
14
Kumpoto malire amenewo adapita molunjika ku Hanatoni, nakathera ku chigwa cha Ifutahele.
15
Adaphatikizapo Katati, Nahalala, Simironi, Idala ndi Betelehemu. Yonse inalipo mizinda 12, pamodzi ndi midzi yake.
16
Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake inali m'dziko limene mabanja a fuko la Zebuloni adalandira ngati choloŵa chao.
17
Mabanja a fuko la Isakara adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachinai.
18
Gawo lao lidaphatikiza Yezireele, Kesuloti, Sunemu,
19
Hafaraimu, Siyoni, Anaharati,
20
Rabiti, Kisiyoni, Ebezi,
21
Remeti, Enganimu, Enihada ndi Betepazezi.
22
Malire amenewo adakafikanso ku Tabori, Sahazuma ndi ku Betesemesi, ndi kutsikira ku Yordani. Lidaphatikiza mizinda 16 pamodzi ndi midzi yake.
23
Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yakeyo, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Isakara adalandira ngati choloŵa chao.
24
Mabanja a fuko la Asere adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachisanu.
25
Gawo lake lidaphatikiza Helekati, Hali, Beteni, Akisafu,
26
Alamumeleki, Amada ndi Misala. Kuzambwe malire adakafika ku Karimele ndi ku Sihori-Libinati.
27
Adakhotera kuvuma naloŵera ku Betedagoni, nkukafika ku dziko la Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifitaele pa njira yakumpoto, kumapita ku Betemeke ndi ku Neiyeli. Adabzola kupita kumpoto mpaka kukafika ku Kabulu,
28
Ebroni, Rehobu, Hamoni ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu.
29
Tsono malirewo adakhotera ku Rama, nakafika mpaka ku Tiro, mzinda wozingidwa ndi linga. Pamenepo adakhoteranso ku Hosa, nkukatulukira ku nyanja, m'dera la Akizibu,
30
Uma, Afeki ndi Rehobu. Yonse pamodzi inalipo mizinda 22, pamodzi ndi midzi yake.
31
Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yakeyo, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Asere adalandira ngati choloŵa chao.
32
Mabanja a fuko la Nafutali adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachisanu ndi chimodzi.
33
Malire ake adayambira ku Helefe kuchokera ku mtengo wogudira wa ku Zaananimu. Adachokeranso ku Adami-Nekebu ndi ku Yabinele mpaka ku Lakumu, nakathera ku Yordani.
34
Ndipo malirewo adakhotera kuzambwe ku Azinoti-Tabori. Kuchoka kumeneko adaloŵera ku Hukoko, nakafika ku dziko la Zebuloni chakumwera, ndi ku dziko la Asere chakuzambwe, ndi ku mtsinje wa Yordani chakuvuma.
35
Mizinda yamalinga inali iyi: Zidumu, Zeri, Hamati, Rakati, Kinereti,
36
Adama, Rama, Hazori,
37
Kedesi, Ederei, Enihazori,
38
Yironi, Migidalele, Horemu, Betanati, ndi Betesemesi. Yonse inalipo mizinda 19, pamodzi ndi midzi yake.
39
Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yakeyo, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Nafutali adalandira ngati choloŵa chao.
40
Mabanja a fuko la Dani adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachisanu ndi chiŵiri.
41
Dziko laolo lidaphatikiza Zola, Esitaoli, Irisemesi,
42
Saalabimu, Ayaloni, Itila,
43
Eloni, Timna, Ekeroni,
44
Eliteke, Gibetoni, Baalati,
45
Yehudi, Beneberaki, Gatirimoni,
46
Meyarikoni ndi Rakoni, ndiponso dziko loyang'anana ndi Yopa.
47
Pamene anthu a fuko la Dani adalandidwa dziko lao, adapita nakathira nkhondo Lesemu, nagonjetseratu ndi kuwononga adani onse. Tsono atatero, adalanda mzindawo, nakhazikika kumeneko. Ndipo adasintha dzina la mzindawo kuti likhale Dani, pakuti limeneli linali dzina la kholo lao Dani.
48
Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yake, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Dani adalandira ngati choloŵa chao.
49
Tsono Aisraele atatha kugaŵana zigawo zosiyanasiyana za dzikolo, adamgaŵirako Yoswa mwana wa Nuni dera lina la dzikolo kuti likhale choloŵa chake.
50
Potsata zimene Chauta adalamula, adampatsako mzinda wa Timnati-Sera umene Yoswayo mwiniwake adaapempha, umene unali m'dziko la Efuremu lamapiri lija. Kumeneko ndiko kumene adamanga mzinda wake, nakhazikika komweko.
51
Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, pamodzi ndi atsogoleri amabanja a Aisraele, ndiwo amene adagaŵa dziko limeneli zigawozigawo, pochita maere pamaso pa Chauta. Ndipo ankachita zimenezi ku Silo, ku chipata choloŵera ku chihema chamsonkhano chija. Choncho adamaliza kuligaŵa dzikolo.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24