bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 16
Joshua 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 17 →
1
Dziko limene lidapatsidwa kwa zidzukulu za Yosefe lidayambira ku mtsinje wa Yordani pafupi ndi Yeriko, cha kuvuma kwa akasupe a Yeriko, kukaloŵa m'chipululu. Lidayambiranso ku Yeriko, ndi kukaloŵa m'dziko lamapiri chakuzambwe, mpaka kukafika ku chipululu cha Betele.
2
Kuchokera ku Betele malire ake adakafika ku Luzi, nabzola ku Ataroti kumene kunkakhala Aaraki.
3
Tsono lidapitirira ndithu kuzambwe, kudera la Ayafaleti, mpaka kufika kunsi kwa Betehoroni. Kuchokera kumeneko malire ake adalunjika ku Gezere, nakalekeza mpaka ku nyanja.
4
Choncho ana a Yosefe, Manase ndi Efuremu adalandira choloŵa chao.
5
Dziko la mabanja a Efuremu ndi ili: malire ake akuvuma anali Ataroti-Adara mpaka kukafika kumtunda kwake kwa Betehoroni.
6
Kuchokera kumeneko malirewo adatsikira mpaka ku nyanja. Mikimetati anali kumpoto kwake. Kuvuma malirewo adakhotera cha ku Taanatisilo, napitirira malo amenewo chakuvuma, mpaka kukafika ku Yanowa.
7
Tsono kuchokera ku Yanowa, adatsikira ku Ataroti ndi ku Naara. Adakafika ku Yeriko ndi kukathera m'Yordani.
8
Malirewo adaloŵera kuzambwe kuchokera ku Tapuwa mpaka ku mtsinje wa Kana, ndi kutsikira mpaka ku nyanja. Dziko limenelo ndilo lidapatsidwa kwa mabanja a Aefuremu kuti likhale choloŵa chao,
9
kuphatikizapo mizinda ndi midzi yopatsidwa kwa Aefuremu, koma yokhala m'kati mwa dziko la anthu a fuko la Manase.
10
Komatu Akanani amene ankakhala ku Gezere, Aefuremu sadaŵapirikitse, kotero kuti Akanani ameneŵa alipobe pakati pa Aefuremu mpaka lero lino. Komabe Akananiwo ankakakamizidwa kugwira ntchito yathangata.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24