bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 21
Joshua 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 22 →
1
Tsiku lina atsogoleri a mabanja a fuko la Levi adabwera kwa wansembe Eleazara, kwa Yoswa, mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraele.
2
Aleviwo adafika ku Silo m'dziko la Kanani, nanena kuti, “Chauta adalamula kudzera mwa Mose kuti ife atipatse mizinda yokhalamo, ndiponso atipatse mabusa pozungulira mizindayo, kuti tizidyetsapo zoŵeta zathu.”
3
Motero Aisraele adapatsa Aleviwo mizindayo pochita maere, pamodzi ndi mabusa a zoŵeta, kuchokera pa magawo ao omwewo, potsata zomwe Chauta adalamula.
4
Mabanja a Kohati ndiwo anali oyambirira kupatsidwa mizinda. Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aroni adapatsidwa mizinda 13, kuchokera m'mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini.
5
Ndipo Akohati otsalawo adapatsidwa mizinda khumi kuchokera m'mafuko a Efuremu ndi Dani ndiponso theka la fuko la Manase lokhala kuzambwe kwa Yordani.
6
Ageresoni adapatsidwa mizinda 13, kuchokera m'mafuko a Isakara, Asere, Nafutali ndi theka la fuko la Manase lokhala ku Basani.
7
Mabanja a Merari adapatsidwa mizinda 12, kuchokera m'mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.
8
Aisraele onse pamodzi adapereka mizinda imeneyi kwa Alevi mwamaere, pamodzinso ndi mabusa odyetsapo zoŵeta, potsata zomwe Chauta adaalamula kudzera mwa Mose.
9
Mizinda ya Yuda ndi Simeoni imene idapatsidwa
10
kwa zidzukulu za Aroni, ku banja lina limodzi la Akohati amene anali Alevi, maina ake ndi aŵa:
11
adaŵapatsa mzinda wa Kiriyati-Ariba. (Araba anali bambo wa Anaki), dzina lake linanso ndi Hebroni. Mzindawo unali m'dziko la Yuda lamapiri lija, pamodzinso ndi mabusa a zoŵeta kuzungulira mzindawo.
12
Komabe minda ya mzindawo pamodzi ndi midzi yake yomwe, adaipatsa Kalebe mwana wa Yefune, kuti ikhale choloŵa chake.
13
Choncho midzi yonse imene ili m'munsimuyi, adaipatsa zidzukulu za Aroni wansembe. Poyamba Hebroni, umene unali mzinda wopulumukiramo aliyense woimbidwa mlandu wa kupha mnzake mwangozi, pamodzi ndi mabusa odyetsapo zoŵeta, ndiponso Libina,
14
Yatiri, Esitemowa,
15
Holoni, Debiri,
16
Aini, Yuta ndi Betesemesi. Yonse pamodzi inalipo mizinda isanu ndi inai kuchokera m'mafuko aŵiri aja a Yuda ndi Simeoni, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
17
A fuko la Benjamini adapereka Gibiyoni, Geba,
18
Anatoti ndi Alimoni. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
19
Ansembe, zidzukulu za Aroni, adapatsidwa mizinda 13, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
20
Mabanja ena a Kohati, a fuko la Levi, adapatsidwa mizinda ina kuchokera ku fuko la Efuremu.
21
Adapatsidwa Sekemu pamodzi ndi mabusa a zoŵeta. Mzindawo unali m'dziko lamapiri la Efuremu. Unalinso mzinda wopulumukiramo munthu aliyense wopha mnzake mwangozi. Adalandiranso Gezere,
22
Kibizaimu ndi Betehoroni. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
23
Kuchokera ku fuko la Dani adalandirako Elitele, Gibetoni,
24
Ayaloni ndi Gatirimoni. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
25
Kuchokera ku theka la Manase wakuzambwe adalandira mizinda iŵiri, Taanaki ndi Ibleamu, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
26
Mabanja a Akohati ameneŵa adalandira mizinda khumi yonse pamodzi, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
27
Ageresoni, gulu lina la fuko la Levi, adalandira mizinda iŵiri kuchokera ku theka la Manase wakuvuma: Golani ku Basani, mzinda wopulumukirapo munthu wopha mnzake mwangozi, ndi Besetera, pamodzi ndi mabusa a zoŵeta.
28
Kuchokera ku fuko la Isakara, adalandira Kisiyoni, Daberati,
29
Yaramuti ndi Enganimu. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
30
Kuchokera ku fuko la Asere adalandira Misalu, Abidoni,
31
Helekati ndi Rehobu. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
32
Kuchokera ku fuko la Nafutali, adalandira Kedesi wa ku Galilea, mzinda wopulumukiramo aliyense wopha mnzake mwangozi, ndiponso Hamotidori ndi Karitani. Yonse pamodzi inalipo mizinda itatu, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
33
Mabanja osiyanasiyana a Ageresoni adalandira mizinda khumi ndi itatu, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
34
Onse otsala a fuko la Levi amene anali a m'banja la Merari, adalandira mizinda iyi kuchokera ku fuko la Zebuloni: Yokoneamu, Karita,
35
Dimina ndi Mahalala. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
36
Kuchokera ku fuko la Rubeni adalandira Bezeri, Yahazi,
37
Kedemoti ndi Mefaati. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
38
Kuchokera ku fuko la Gadi adalandira Ramoti ku Giliyadi, mzinda wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi, ndiponso Mahanaimu,
39
Hesiboni ndi Yazere. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.
40
Motero mabanja a Merari, adapatsidwa mizinda khumi ndi iŵiri mwamaere.
41
Mizinda 48 ya m'dziko limene Aisraele adalandira idapatsidwa kwa Alevi, pamodzi ndi mabusa a zoŵeta.
42
Mzinda uliwonse unali ndi mabusa a zoŵeta.
43
Motero Chauta adapatsa Aisraele dziko limene Iye yemwe adaalonjeza molumbira kuti adzapatsa makolo ao. Aisraele adalandira dzikolo, nakhazikika komweko.
44
Chauta adaŵapatsa mtendere pakati pa anthu ena onse oŵazungulira, potsata zomwe Iye adaalonjeza makolo ao. Panalibe ndi mmodzi yemwe mwa adani ao amene adatha kugonjetsa Aisraele, chifukwa choti Chauta adaŵapatsa mphamvu zopambanira adani ao.
45
Zoonadi Chauta adasunga malonjezo onse amene adaachita ndi Aisraele.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24