bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 3
Joshua 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 4 →
1
M'mamaŵa kutacha Yoswa adanyamuka. Iye, pamodzi ndi Aisraele onse, adatuluka ku Sitimu kuja, napita ku Yordani, ndipo adagona kumeneko.
2
Patapita masiku atatu, atsogoleri adakayendera zithando zonse,
3
namauza anthu kuti, “Mukadzaona ansembe Achilevi aja atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wanu, mudzanyamuke pamalo panu ndi kuŵatsata.
4
Potero mudzaidziŵa njira yoyenera kutsata, popeza kuti nkale lomwe kumeneko simudadzereko. Komatu tsono Bokosi lachipanganolo musaliyandikire. Pakati pa inu ndi Bokosilo pazikhala mtunda wosachepera kilomita imodzi.”
5
Motero Yoswa adauza anthu onse kuti, “Mudzisungetu tsono, chifukwa maŵa Chauta adzachita zodabwitsa zazikulu pakati panu.”
6
M'maŵa mwake Yoswa adauza ansembe kuti, “Nyamulani Bokosi lachipangano la Chauta, muwoloke, mutsogolere anthuwo.” Iwowo adachitadi monga momwe Yoswa adanenera.
7
Apo Chauta adauza Yoswa kuti, “Zimene ndikuchita lerozi, ndizo zidzapatse Aisraele onse mtima wokulemekeza iwe, kuti ndiwe munthu wamkulu. Ndipo adzadziŵa kuti Ine ndili nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose.
8
Ansembe amene akunyamula Bokosi lachipangano la Chauta, uŵalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yordani, muloŵe m'madzimo ndi kuima m'mphepete.’ ”
9
Tsono Yoswa adaŵauza anthuwo kuti, “Bwerani kuno, mudzamve zimene Chauta, Mulungu wanu, akukuuzani.
10
Motero mudzadziŵa kuti Mulungu wamoyo ali pakati panu. Inu mukamapita patsogolo, Iye adzapirikitsa Akanani onse, pamodzi ndi Ahiti, Ahivi, Aperizi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi.
11
Pamenepo Bokosi lachipangano la Chauta wa dziko lonse lapansi liwoloke Yordani patsogolo panu.
12
Tsopano musankhe amuna khumi ndi aŵiri kuchokera ku fuko lililonse la Aisraele.
13
Ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi, akangoponda madziwo, madzi onse a Yordani ochokera kumtunda adzaleka kuyenda, ndipo adzaima ngati chipupa.”
14
Nyengo imeneyo inali ya kholola, ndipo mtsinje unali wodzaza kwambiri. Anthu onse adachoka ku zithando kukaoloka mtsinje wa Yordani uja. Ansembe ndiwo anali patsogolo, atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta lija.
15
Pamene ansembewo adafika pa chibumi cha Yordani, natsikira m'madzimo ndi kuponda madziwo,
16
madzi onse adaima osayendanso. Madzi akumtunda adaundana ngati khoma lalitali, kuchokera ku Adama mpaka ku mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ndiye kuti Nyanja Yakufa, adatheratu pamalopo, ndipo anthu adaolokera tsidya lina, pafupi ndi Yeriko.
17
Chonsecho nkuti ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta aja ataima pakatimpakati pa mtsinje wa Yordani uja, mpaka anthu onse adatha kuwoloka.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24