bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 20
Joshua 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 21 →
1
Chauta adauza Yoswa kuti,
2
“Uza Aisraele kuti, ‘Sankhulani mizinda yopulumukiramo, imene Ine ndidakuuzani kudzera mwa Mose.
3
Munthu aliyense wopha mnzake mwangozi, osati mwadala, angathe kuthaŵira kumeneko. Motero angathe kupulumuka kwa wofuna kumlipsira.
4
Angathe kuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyo, nakafika pa malo achiweruzo amene ali pa chipata cha mzindawo. Atafika, asimbire atsogoleri mlandu wakewo. Apo atsogoleriwo adzamlola kuloŵa mumzindamo, nadzampatsa malo oti azikhalako.
5
Munthu wofuna kulipsirayo akamlondola komweko, anthu amumzindamo asampereke munthu wopha mnzakeyo. Koma amtchinjirize chifukwa adachita zimenezo mwangozi, pakupha Mwisraele mnzake. Sadachite zimenezo mwachiwembu.
6
Munthuyo adzakhala mumzindamo mpaka ataweruzidwa pamaso pa anthu onse, ndiponso mpaka mkulu wa ansembe wa nthaŵi imeneyo atafa. Pamenepo munthuyo angathe kubwereranso kwao, kumudzi kumene adachoka mothaŵa kuja.’ ”
7
Motero cha kuzambwe kwa mtsinje wa Yordani adapatula Kedesi m'dera la Galilea, m'dziko lamapiri la Nafutali. M'dziko lamapiri la Efuremu adapatula Sekemu, ndipo m'dziko lamapiri la Yuda adapatula Kiriyati-Ariba (ndiye kuti Hebroni).
8
Kuvuma kwa Yordani, m'mapiri aja a kuvuma kwa Yeriko m'chipululu muja, adapatula Bezeri pakati pa mizinda ya fuko la Rubeni. Pakati pa mizinda ya fuko la Gadi ku Giliyadi adapatula Ramoti. Ndipo pakati pa mizinda ya fuko la Manase ku Basani adapatula Golani.
9
Imeneyi ndiyo inali mizinda yopulumukiramo ya Aisraele onse, ngakhalenso alendo amene ankakhala pakati pao. Aliyense wopha munthu mwangozi, osati mwadala, ankatchinjirizidwa kumeneko. Womlondola kuti amlipsire sankaloledwa kumupha munthu wothaŵayo, mlandu wake usanazengedwe pamaso pa mpingo wonse.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24