bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 9
Joshua 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 10 →
1
Mafumu onse okhala kuzambwe kwa Yordani adamva zimenezi. Onse okhala ku mapiri, m'zigwa ndiponso m'mbali mwa Nyanja Yaikulu cha kumpoto kwa Lebanoni, nawonso adamva. Ameneŵa ndiwo mafumu a Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.
2
Ndiye onseŵa adapangana za kulimbana ndi Yoswa ndi Aisraele onse.
3
Tsono Ahivi a ku Gibiyoni atamva zimene Yoswa adaachita mzinda wa Yeriko ndi wa Ai,
4
adaganiza zoti amugwire m'maso. Adapita nasenzetsa abulu chakudya cha m'matumba akalekale, ndiponso matumba a vinyo a chikopa cha zigamba zokhazokha.
5
Adavala nsapato zothaitha za zigamba zokhazokha, ndiponso zovala zansanza. Buledi amene adatenga anali wouma ndi wachuku.
6
Tsono adapita kwa Yoswa ku zithando ku Giligala kuja, namuuza iyeyo pamodzi ndi Aisraele onse kuti, “Ife tachoka ku dziko lakutali, ndipo tikufuna kuti tichite nanu chipangano.”
7
Koma Aisraele adayankha kuti, “Mwina mwake kwanu nkufupi konkuno. Nanga tingachite nanu chipangano bwanji?”
8
Iwo adauza Yoswa kuti, “Ife ndife akapolo anu.” Tsono Yoswa adaŵafunsa kuti, “Kodi inu ndinu yani? Mwachoka kuti?” Anthuwo adamuuza nkhani yonse, adati,
9
“Ife tachoka kutali kwambiri, chifukwa choti tamva za Chauta, Mulungu wanu. Tamva mbiri yonse ya zimene Iye adachita ku Ejipito,
10
ndiponso zimene adachita kwa mafumu aŵiri a Aamori kuvuma kwa Yordani, kwa Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndiponso kwa Ogi, mfumu ya ku Basani, imene imakhala ku Asitaroti.
11
Tsono atsogoleri athu ndi anthu onse okhala m'dziko lathu adatiwuza kuti, ‘Konzani chakudya chapaulendo, pitani mukakumane nawo anthu amenewo ndipo mukanene kuti, “Ife tadzagonja, chonde mupangane nafe zamtendere.” ’
12
Tangoonani bulediyu. Pochoka kwathu, buledi ameneyu anali wofunda ndithu, koma tangoonani ali gwaa ndiponso wochita chuku.
13
Pamene tinali kuthira vinyo, matumbaŵa anali atsopano ndithu, koma taonani ngong'ambika. Zovala zathu ndi nsapatozi zangokhala nsanza zokhazokha, chifukwa cha kutalika kwa ulendo.”
14
Ndipo Aisraele adalaŵako chakudya chao, osafunsa Chauta.
15
Motero Yoswa adapangana nawo za mtendere, nanena kuti sadzaŵapha. Atsogoleri a Aisraelewo adatsimikiza chipanganocho ndi malumbiro.
16
Patangopita masiku atatu atachita chipanganocho, Aisraele adaŵazindikira anthuwo kuti ngochokera pafupi.
17
Tsono Aisraele adachoka napita kwao kwa anthuwo, napeza kuti mizinda yao inali Gibiyoni, Kefira, Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.
18
Komatu Aisraele sadathe kuŵapha anthuwo, poti paja atsogoleri ao anali atalonjeza m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, za anthu ameneŵa; apo Aisraele ena adayamba kudandaula kwa atsogoleri za zimenezi.
19
Koma atsogoleriwo adayankha kuti, “Ife tidaŵalonjeza m'dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndipo tsopano sitingathe kuŵapha.
20
Tiŵalole akhale moyo, kuti ukali wa Mulungu ungatigwere.
21
Alekeni akhale moyo, komatu azitidulira nkhuni ndi kumatitungiranso madzi.” Zimenezi ndizo zimene adanena atsogoleri aja.
22
Yoswa adaŵaitana Agibiyoniwo, naŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mudatinyenga potiwuza kuti mwachokera kutali, chikhalirecho ndinu a pafupi pompano?
23
Popeza kuti mwachita zimenezi, Mulungu wakutembererani. Nthaŵi zonse inu ndiye muzidzatidulira nkhuni, ndi kutitungira madzi ku Nyumba ya Mulungu.”
24
Ndipo iwo adayankha kuti, “Mbuyathu, ife tidachita zimenezi chifukwa choti tidamva kuti Chauta, Mulungu wanu, adalamula mtumiki wake Mose kuti adzakupatseni dziko lonseli, ndipo kuti mudzaphe anthu onse kulikonse kumene mukaŵapeze. Motero tidachita zimenezi poti tidakuwopani kwambiri ndipo tidafuna kupulumutsa moyo wathu.
25
Tsopano lino, otilamulira ndinu, ndipo mungotichita zimene zingakukomereni,”
26
Apo Yoswa adaŵatchinjiriza anthuwo, kuti Aisraele angaŵachite zoipa, kapena kuŵapha.
27
Komabe nthaŵi yomweyo, adasanduka odulira anthu nkhuni, ndiponso otunga madzi a ku guwa lansembe la Chauta. Mpakana lero lino, akuchitabe zimenezi ku malo aliwonse amene Chauta adasankha.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24