bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 5
Joshua 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 6 →
1
Mafumu onse a Aamori amene ankakhala kuzambwe kwa Yordani, pamodzi ndi mafumu a Akanani okhala m'mphepete mwa nyanja, adamva kuti Chauta adaumitsa Yordani pamene Aisraele ankaoloka. Choncho adachita mantha, ndi kutayiratu mtima chifukwa cha Aisraelewo.
2
Tsono Chauta adauza Yoswa kuti, “Sema miyala ngati mipeni, kuti uumbalire Aisraeleŵa.”
3
Yoswa adasemadi mipeni yamiyalayo, naŵaumbala onsewo ku phiri lotchedwa “Koumbalira.”
4
Adachita zimenezi chifukwa amuna amene anali oyenera kuponya nkhondo onse adaatha nkufa m'chipululu atatuluka ku Ejipito kuja.
5
Anthu onse amene adaatuluka ku Ejipito anali ataumbalidwa kale, koma onse obadwira m'chipululu pa nthaŵi ya ulendo wofuma ku Ejipito anali osaumbalidwa.
6
Aisraele adakhala akuyenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka adafa amuna onse amene potuluka ku Ejipito anali a msinkhu woyenera pa nkhondo. Adatha nkufa, popeza kuti sadamvere Chauta. Iye adaachita kuŵalumbirira kuti sadzaloŵamo m'dziko lamwanaalirenji lija limene adaalonjeza kwa makolo ao kuti adzaŵapatsa.
7
Koma ana ao amene adaloŵa m'malo mwao, sadaumbalidwe pamene anali paulendo m'chipululumo, ndipo ndiwo amene Yoswa adalamula kuti aumbalidwe.
8
Kuumbalako kutatha, Aisraele onse ankangokhala m'zithandomo kudikira kuti zilonda zipole.
9
Tsono Chauta adauza Yoswa kuti, “Lero ndakuchotserani manyazi a ukapolo wanu uja umene munali nawo ku Ejipito.” Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Giligala, ndipo mpaka lero lino malo ameneŵa akudziŵika ndi dzina limeneli.
10
Pamene Aisraele anali m'zithando ku Giligala m'chigwa cha ku Yeriko, adachita Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo.
11
M'maŵa mwake mpamene anthu aja adayamba kudya chakudya cha ku Kanani. Adakazinga tirigu, naphikanso buledi wosatupitsa tsiku limenelo.
12
Zitangotero, mana uja adaleka kugwa, ndipo sadapezekenso pakati pa Aisraele. Kuyambira nthaŵi imeneyo adayamba kudya chakudya cha ku Kanani.
13
Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, mwadzidzidzi adaona munthu ataimirira kutsogolo kwake, lupanga losolola lili m'manja. Tsono Yoswa adapita pomwe panali munthupo, namufunsa kuti, “Kodi iwe ndiwe mmodzi wa ankhondo athu kapena ndiwe mdani wathu?”
14
Munthu uja adayankha kuti, “Sindine mmodzi mwa ankhondo anu kapenanso mdani wanu. Ndine mtsogoleri wa gulu lankhondo la Chauta pano.” Choncho Yoswa adadzigwetsa pansi chafufumimba naati, “Ine ndine wantchito wanu, mbuyanga. Nanga mufuna kuti ndichite chiyani?”
15
Wolamula gulu lankhondo la Chauta uja adamuyankha kuti, “Vula nsapato zako. Malo amene ukuimirirapoŵa ngoyera.” Yoswa adachitadi zimene adamuuzazo.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24