bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 18
Joshua 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 19 →
1
Ataligonjetsa dziko lonselo, Aisraele onse adasonkhana ku Silo, ndipo adamangako chihema chamsonkhano.
2
Nthaŵi imeneyo nkuti mafuko asanu ndi aŵiri asanapatsidwe magawo ao a dzikolo.
3
Motero Yoswa adafunsa Aisraele kuti, “Kodi mudzadikira mpaka liti kuti muloŵe m'dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakupatsani?
4
Tandipatsani amuna atatu a fuko lililonse. Ameneŵa ndiŵatuma kuti akayendere dziko lonselo, ndipo alembe bwino magawo ake onse, kuti tithandizidwe poligaŵa. Atatero, abwererenso kuno kwa ine.
5
Adzaligaŵe dzikolo magawo asanu ndi aŵiri. Yuda adzakhala m'dziko lake kumwera, ndipo Yosefe adzakhala m'dziko lake kumpoto.
6
Mudzalembe mau ofotokoza za magawo asanu ndi aŵiriwo a dziko limenelo, ndi kudzandipatsa ine. Ineyo ndiye ndidzakuchitireni maere pamaso pa Chauta, Mulungu wathu.
7
Alevi okha sadzalandira nao gawo la dzikolo, popeza kuti gawo lao ndi kutumikira Chauta pa unsembe. Fuko la Gadi ndi la Rubeni ndi theka la fuko la Manase adalandira kale dziko lao kuvuma kwa Yordani. Mose, mtumiki wa Chauta, ndiye adaŵapatsa.”
8
Tsono anthuwo adapitadi kukalemba za dzikolo, Yoswa ataŵalangiza kuti, “Pitani, kaliyendereni dziko lonselo, ndipo mukalembe bwino za dzikolo. Tsono mutatero, mubwererenso kwa ine kuno. Ine ndidzakuchitirani maere pamaso pa Chauta konkuno ku Silo.”
9
Pamenepo anthuwo adakaliyendera dziko lonselo, nalemba bwino m'buku za dzikolo. Adagaŵa dzikolo magawo asanu ndi aŵiri, ndipo adalembanso mndandanda wa midzi yonse. Atatero adabwerera kwa Yoswa ku zithando ku Silo kuja.
10
Tsono Yoswa adachita maere, naŵapemphera nzeru kwa Chauta. Ndipo fuko lililonse la Aisraele adalipatsa gawo la dzikolo.
11
Mabanja a fuko la Benjamini adalandira dziko la pakati pa Yuda ndi Yosefe.
12
Kumpoto malire ao adayambira ku mtsinje wa Yordani, nakwera chitunda cha kumpoto kwa Yeriko nabzola dziko lamapiri chakuzambwe, nakafika ku chipululu cha Betaveni.
13
Tsono malirewo adaloza ku Luzi, ndi kutsata mbali ya phiri loti Luzi, (lotchedwanso Betele). Tsono adatsikira ku Ataroti-Adara, kubzola phiri lili kumwera kwa Betehoroni wakunsi.
14
Ndipo malirewo adaloŵanso kwina, nalunjika kumwera kuchokera kuzambwe kwake kwa phiri limene limayang'anana ndi Betehoroni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati-Baala (wotchedwanso Kiriyati-Yeyarimu), mzinda wa fuko la Yuda. Ameneŵa ndiwo anali malire akuzambwe.
15
Malire akumwera adayambira pamphepete penipeni pa Kiriyati-Yearimu, napita kuzambwe mpaka kukafika ku Akasupe a ku Nefutowa.
16
Adatsikira m'mphepete mwa phiri limene limayang'anana ndi chigwa cha Benihinomu, cha kumpoto kwake kwa chigwa cha Arefaimu. Adapita chakumwera kubzola chigwa cha Hinomu, kumwera kwa chitunda cha Ayebusi, moyang'ana ku Enirogele.
17
Tsono malire adakhota, naloŵa kumpoto ku Enisemesi ndi kubzola mpaka kukafika ku Geliloti, kuyang'anana ndi pokwerera pa Aduminu. Atatero malirewo adatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni.
18
Adabzola cha kumpoto kwa chitunda cha Betaraba, natsikira ku chigwa cha Yordani.
19
Adapitiriranso kumpoto kwa chitunda cha Betehogila, ndipo adakathera chakumpoto ku mathiriro a mtsinje wa Yordani m'Nyanja Yakufa, kumwera kwake kwenikweni kwa Yordani.
20
Mtsinje wa Yordani ndiye udachita malire kuvuma kwake. Ameneŵa ndiwo anali malire a dziko limene mabanja a fuko la Benjamini adalandira, kuti likhale choloŵa chao.
21
Mizinda ya mabanja a Benjamini inali Yeriko, Betehogila, Emekezizi,
22
Betaraba, Zemaraimu, Betele,
23
Avimu, Para, Ofura,
24
Kefaramoni, Ofini ndi Geba. Yonse inalipo 12, pamodzi ndi midzi yake.
25
Panalinso Gibiyoni, Rama, Beeroti,
26
Mizipa, Kefira, Moza,
27
Rekemu, Iripele, Tarala,
28
Zela, Haelefe, Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu), Gibea ndi Kiriyati-Yearimu. Yonse inalipo 14, pamodzi ndi midzi yake. Dziko limeneli ndilo limene mabanja a Benjamini adalandira, kuti likhale choloŵa chao.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24