bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 23
Joshua 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 24 →
1
Padapita nthaŵi yaikulu chiyambire pamene Chauta adakhazikitsa mtendere pakati pa Aisraele ndi adani ao oŵazungulira. Pamenepo nkuti Yoswa atatheratu nkukalamba.
2
Tsono Yoswayo adaitana Aisraele onse, pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, aweruzi ndi akapitao a anthuwo, naŵauza kuti “Tsopano ine ndakalamba.
3
Zonse zimene Chauta wachitira mitundu ina yonseyi chifukwa cha inu, mwazipenya. Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene wakumenyerani nkhondo.
4
Tamvani tsono, mitundu imene simudaipambanebe, ndaipereka kwa mafuko anu, chimodzimodzi mitundu inayo imene ndidaiwononga pakati pa Yordani ndi Nyanja Yaikulu kuzambweko.
5
Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzaŵathaŵitse pamaso panu. Inuyo mudzatenga maiko ao monga momwe Chauta, Mulungu wanu, wakulonjezerani.
6
Motero, muchenjere kuti mumvere ndi kumachitadi zonse zomwe zidalembedwa m'buku la malamulo a Mose. Musanyozere gawo lina lililonse la malamulowo,
7
ndipo musagwirizane ndi anthu aŵa amene atsala pakati panu. Musamatchula maina a milungu yao kapena kulumbira poitchula, kapena kumaitumikira, kapenanso kumaigwadira.
8
Mukamakhulupirira Chauta, monga momwe mwachitira mpaka tsopano lino,
9
Chauta adzakupirikitsirani mitundu yaikuluikulu ndi yamphamvu. Mpaka pano, palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulimbana nanu.
10
Aliyense mwa inu angathe kuthamangitsa anthu chikwi chimodzi, chifukwa Chauta ndiye akukumenyerani nkhondo monga adalonjezera.
11
Musamale kwambiri tsono kuti mukonde Chauta, Mulungu wanu.
12
Mukabwerera m'mbuyo ndi kuphatikizana ndi mitundu yotsalira ili pakati panuyi, ndi kumakwatirana nayo,
13
pamenepo mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, sadzapirikitsa mitundu imeneyi pamaso panu. Koma anthuwo adzakhala ngati msampha kwa inu, kapenanso ngati khwekhwe. Adzakhalanso ngati chikoti choŵaŵa pamsana panu, kapena ngati minga zokulasani m'maso mwanu. Zimenezi zidzachitikabe mpaka inuyo mutatha m'dziko labwinoli limene Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani.
14
“Ine ndi ulendo uno tsopano. Aliyense mwa inu akudziŵa bwino lomwe mumtima mwake ndi mumzimu mwake kuti Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani zinthu zonse zabwino zimene adaalonjeza. Zonse zimene adaalonjeza, zachitika. Palibe lonjezo ndi limodzi lomwe limene silidachitike.
15
Monga momwe Chauta, Mulungu wanu, wakuchitirani zabwino zonse zimene adaanena kuti adzachita, choncho angathe kukuchitani zoipa, mpaka kukuchotsani m'dziko lokomali limene Iye adakupatsani.
16
Ngati simusunga chipangano chomwe Chauta adakulamulani, mukamapita kukatumikira milungu ina ndi kumakaigwadira, Chauta adzakupserani mtima, ndipo sipadzatsala ndi mmodzi yense m'dziko labwino limene adakupatsanilo.”
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24