bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 15
Joshua 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 16 →
1
Mabanja onse a fuko la Yuda adalandira chigawo cha dzikolo motero: dziko lao lidalekeza ku malire a Edomu, mpaka ku chipululu cha Zini, kumwera kwenikweni.
2
Malire ake akumwera adayambira kumwera kwenikweni kwa Nyanja Yakufa,
3
napita cha kumwera kokhakokha kuyambira ku chikweza cha ku Akarabimu, nkudzera pa mpata wa mapiri a ku Zini. Kuchokera kumeneko, adabzola cha kumwera kwa Kadesi-Baranea, kupitirira Hezironi mpaka ku Adara, ndi kutembenukira ku Karaka.
4
Adapitirira mpaka ku Azimoni, natsata mtsinje wa m'malire a Ejipito mpaka ku nyanja. Ameneŵa ndiwo malire akumwera.
5
Malire akuvuma anali Nyanja Yakufa mpaka kumene Yordani amathira m'Nyanja Yakufa. Tsono malire akumpoto adayambira kunyanjako,
6
napitirira mpaka ku Betehogila, nakafika kumpoto kwa Betaraba. Adapitirira mpaka kukafika ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni.
7
Ndipo malirewo adachokeranso ku chigwa cha Mavuto mpaka ku Debiri, mpakanso kumpoto kuloŵera ku Giligala, kuyang'anana ndi chikweza cha Adumimupasi cha ku mbali yakumwera ya chigwa. Tsono adapitiriranso ku akasupe a Enisemesi, natulukira ku Enirogele.
8
Ndipo adakwera kubzola chigwa cha mwana wa Hinomu cha mbali ya kumwera kwa Ayebusi, (ndiye kuti ku Yerusalemu). Malirewo adapitirira kukafika pamwamba pa phiri moyang'anana ndi chigwa cha Hinomu chakuzambwe, ku mathero akumpoto a chigwa cha Refaimu.
9
Tsono adachokeranso pamwamba pa phiri, nakafika mpaka ku akasupe a Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya ku phiri la Efuroni. Kuchoka uko nkutsikira ku Baala, (ndiye kuti Kariyati-Yearimu),
10
kumene adazungulira cha kuzambwe kwa Baala, kuloza ku dziko lamapiri la Seiri. Adapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu, (ndiye kuti Kesaloni), natsikira ku Betesemesi mpaka kubzola Timna.
11
Tsono malirewo adatulukira ku matsitso a phiri cha kumpoto kwa Ekeroni. Adakhotera ku Sikeroni, kubzola phiri la Baala, mpaka kukafika ku Yabinele. Malire amenewo adakathera ku nyanja.
12
Kuzambwe malire anali gombe la Nyanja Yaikulu yomwe. Ameneŵa ndiwo malire amene adazungulira maiko opatsidwa kwa fuko la Yuda.
13
Monga momwe Chauta adalamulira Yoswa, gawo lina la dziko la fuko la Yuda lidapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune. Yoswa adampatsa Kiriyati-Ariba ndiye kuti Hebroni. (Araba anali bambo wa Anaki).
14
Kalebe adapirikitsa mafuko atatu a Anaki m'dzikomo, maina ao ndi aŵa: Sesai, Ahimani ndi Talimai.
15
Kuchokera kumeneko adapita kukalimbana ndi anthu a ku Debiri. Mzinda umenewu kale unkatchedwa Kiriyati-Sefere.
16
Tsono Kalebe adati, “Mkulu wa ankhondo amene athire nkhondo mzinda wa Kiriyati-Sefere, naulanda, ndidzampatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.”
17
Mbale wake wa Kalebe, Otiniyele, mwana wa Kenazi, adaulanda mzindawo. Choncho Kalebe adampatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.
18
Tsiku lina, Akisayo atafika, Otiniyele adaumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo wake. Tsono Akisa atatsika pa bulu wake, Kalebe adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kanthu?”
19
Iye adayankha kuti, “Ndimati mundipatseko mphatso. Popeza kuti mwandikhazika m'dziko la Negebu lopanda madzi, mundipatsenso akasupe a madzi.” Choncho Kalebe adampatsa akasupe akumtunda ndi akuchigwa omwe.
20
Ili ndilo dziko limene mabanja a fuko la Yuda adalandira ngati choloŵa chao.
21
Mizinda ya kumwera kwenikweni imene iwo adalandira yoyandikana ndi dziko la Edomu, inali iyi: Kabizeele, Edere, Yaguru,
22
Kina, Dimona, Adada,
23
Kedesi, Hazori, Itinani,
24
Zifi, Telemu, Bealoti,
25
Hazori-Hadata, Keriyoti-Hezironi, (ndiye kuti Hazori),
26
Amama, Sema, Molada,
27
Hazaragada, Hesimoni, Betepeleti,
28
Hazara-Suwala, Beereseba, Biziyotiya,
29
Baala, Iyimu, Ezemu,
30
Elitoladi, Kesili, Horoma,
31
Zikilagi, Madimana, Sanisana,
32
Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni. Yonse inalipo mizinda 29, pamodzi ndi midzi yake yozungulira yomwe.
33
Mizinda yakuchigwa inali iyi: Esitaoli, Zora, Asina,
34
Zanowa, Enganimu, Tapuwa, Enamu,
35
Taramuti, Adulamu, Soko, Azeka,
36
Saraimu, Aditaimu, Gedera ndi Gederotaimu. Yonse inalipo mizinda 14, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
37
Panalinso Zenani, Hadasa, Megidali-Gadi,
38
Dileani, Mizipa, Yokotele,
39
Lakisi, Bozikati, Egiloni,
40
Kaboni, Lahamasi, Kitilisi,
41
Gederoti, Betedagoni, Naama ndiponso Makeda. Yonse inali mizinda 16, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
42
Panalinso Libina, Eteri, Asani,
43
Ifuta, Asana, Nezibu,
44
Keila, Akizibu ndi Maresa. Yonse inali mizinda isanu ndi inai, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
45
Panalinso Ekeroni ndi midzi yake.
46
Yonse imene inali m'mbali mwa Nyanja Yaikulu, kuchokera ku Ekeroni mpaka ku Asidodi.
47
Adalandiranso mizinda yaikulu ya Asidodi ndi Gaza, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Malire ake adafika ku mtsinje wa ku Ejipito, ndipo mpaka ku Nyanja Yaikulu.
48
Ku dziko lakumapiri kunali Samiri, Yatiri, Soko,
49
Dana, Kiriyati-Sana, (ndiye kuti Debiri),
50
Anabu, Esitemowa, Animu,
51
Goseni, Holoni ndi Gilo. Yonse inalipo 11, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
52
Panalinso Arabu, Duma, Esani,
53
Yanimu, Betetapuwa, Afeka,
54
Humata, Kiriyati-Ariba (ndiye kuti Hebroni), ndi Aziyori. Yonse inalipo isanu ndi inai, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
55
Panalinso Maoni, Karimele, Zifi, Yuta,
56
Yezireele, Yokodeamu, Zanowa,
57
Kaini, Gibea ndi Timna. Yonse inalipo mizinda khumi, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
58
Panalinso Halahulu, Betezuri, Gedori,
59
Maarati, Betanoti ndi Elitekoni. Yonse inalipo mizinda isanu ndi umodzi, kuphatikizapo midzi yake yozungulira.
60
Panalinso Kiriyati-Baala (ndiye kuti Kiriyati-Yearimu) ndi Raba. Yonse inalipo mizinda iŵiri, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
61
Mizinda yam'chipululu inali Betaraba, Midini, Sekaka,
62
Nibisani, mzinda wa Mchere ndi Engedi. Yonse inalipo mizinda isanu ndi umodzi, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
63
Koma anthu a fuko la Yuda sadathe kupirikitsa Ayebusi amene ankakhala ku Yerusalemu. Ndipo mpaka pano Ayebusiwo amakhalabe mu Yerusalemu, pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24