bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joshua 17
Joshua 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 18 →
1
Gawo lina la dzikolo lidapatsidwa kwa fuko la Manase amene anali mwana wachisamba wa Yosefe. Makiri, kholo la anthu okhala ku Giliyadi, ndiye anali mwana wachisamba wa Manase. Makiri analinso msilikali, motero maiko aŵa, Giliyadi ndi Basani, adapatsidwa kwa iyeyo.
2
Mabanja otsala a Manase amene adapatsidwanso dziko ndi aŵa: Abiyezere, Heleki, Asiriele, Sekemu, Hefere ndi Semida. Ameneŵa ndiwo zidzululu za Manase, mwana wa Yosefe, komanso ndiwo amene anali eni mbumba.
3
Panali Zelofehadi mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase. Zelofehadiyo analibe mwana wamwamuna ndi mmodzi yemwe, koma aakazi okhaokha. Maina a ana aakaziwo ndi aŵa: Mahala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza.
4
Iwoŵa adabwera kwa Eleazara wansembe, nafikanso kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa atsogoleri, ndipo adati, “Chauta adalamula Mose kuti ife ndi alongo athu atipatse gawo lina la dziko ngati choloŵa chathu.” Motero iwowo, pamodzi ndi abale a bambo wao, adapatsidwa dziko kuti likhale lao potsata zimene Chauta adalamula.
5
Choncho kuwonjeza pa maiko a Giliyadi ndi Basani a kuvuma kwa Yordani, a fuko la Manase adalandiranso magawo khumi,
6
popeza kuti ana aakazi a Manase ndi ana ake aamuna, onsewo adalandira magawo ao. Dziko la Giliyadi lidapatsidwa kwa otsala mwa zidzukulu za Manase.
7
Dziko la Manase malire ake adachokera ku Asere, ndipo adakafika ku Mikimetati kuvuma kwa Sekemu. Tsono malire adapita kumwera kuloza kwa anthu a ku Entapuwa.
8
Dzikolo linali la Manase, koma mzinda wa Tapuwa wapamalire unali wa fuko la Efuremu, ngakhale kuti m'pakati penipeni pa mizinda ya Manase.
9
Tsono malire ake adatsikira ku kamtsinje ka Kana. Mizinda yakumwera kwa kamtsinje kameneka inali ya fuko la Efuremu, ngakhale inali m'dziko la Manase. Malire a dziko la Manase adalambalala chakumpoto kwa kamtsinjeko, nakalekezera ku nyanja.
10
Efuremu anali kumwera, Manase anali kumpoto, ndipo Nyanja Yaikulu inali malire akuzambwe. Malirewo adakafika ku Asere kumpoto chakuzambwe ndi ku Isakara kumpoto chakuvuma.
11
M'dziko la Isakara ndi la Asere munalinso gawo lina la Manase lotchedwa Beteseani, kuphatikizapo midzi yozungulira. Panalinso Akanani amene ankakhala ku Ibleamu, ku Dori mzinda wa m'mbali mwa nyanja, ku Endori, ku Taana ndi ku Megido, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
12
Komabe anthu a fuko la Manase sadathe kuŵapirikitsa Akanani okhala m'mizinda imeneyo. Motero Akananiwo adangokhalabe komweko.
13
Ngakhale pamene Aisraele anali amphamvu m'dzikomo, sadapirikitse Akanani onse, koma adangoŵasandutsa anthu ogwira ntchito yathangata.
14
Zidzukulu za Yosefe zidafunsa Yoswa kuti, “Bwanji ife mwangotigaŵira gawo limodzi lokha la dziko, kuti likhale choloŵa chathu? Ifetu tilipo ambiri chifukwa Chauta adatidalitsa.”
15
Yoswa adaŵayankha kuti, “Ngati mulipo ambiri, ndipo ngati dziko lamapiri la Efuremulo likucheperani, loŵani ku nkhalango, mudule mitengo ndi kudzikonzera malo oti mukhalepo m'dziko la Aperizi ndi Arefaimu.”
16
Pamenepo zidzukulu za Yosefezo zidati, “Zoonadi dziko lamapirilo silingatikwanire ife, komanso Akanani amene ali ku zigwa ali ndi magaleta achitsulo, ngakhale amene ali ku Beteseani ndi ponse pozungulira, ndiponso amene ali m'chigwa cha Yezireele.”
17
Yoswa adauza zidzukulu za Yosefe za m'fuko la Efuremu ndi la Manase kuti, “Inu mulipo ambiri zedi ndipo ndinu amphamvu. Mudzalandira magawo enanso.
18
Mudzalandiradi dziko lamapirilo. Ngakhale lili ndi nkhalango, inuyo mudzadula mitengo, ndipo mudzalandira dziko lonselo kuti likhale lanu. Akanani mudzaŵapirikitsa, ngakhale ali ndi magaleta achitsulo ndiponso ngakhale iwo ngamphamvu.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24