bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 10
Judges 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 11 →
1
Atafa Abimeleki, padabwera winanso wodzapulumutsa Aisraele. Iyeyu anali Tola, mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo, wa fuko la Isakara. Ankakhala ku Samiri, m'dziko lamapiri la Efuremu.
2
Adaweruza Aisraele zaka 23. Pambuyo pake adamwalira, naikidwa ku Samiri.
3
Atafa Tola padabwera Yairo Mgiliyadi amene adaweruza Aisraele zaka 22.
4
Iyeyu anali nawo ana makumi atatu amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Anawo anali nayonso mizinda makumi atatu imene mpaka pano ikutchedwa Havoti-Yairo m'dziko la Giliyadi.
5
Pambuyo pake Yairo adamwalira, naikidwa ku Kamoni.
6
Aisraele adachitanso zoipira Chauta potumikira Abaala ndi Aasitaroti, milungu ya ku Siriya, milungu ya ku Sidoni, milungu ya ku Mowabu, milungu ya Aamoni ndiponso milungu ya Afilisti. Aisraelewo adasiyadi Chauta osamamtumikiranso ai.
7
Tsono Chauta adaŵapsera mtima Aisraele, ndipo adalola kuti Afilisti ndi Aamoni aŵagonjetse.
8
Chaka chimenecho anthuwo adagonjetseratu Aisraele nayamba kuŵasautsa. Pa zaka 18, adakhala akuŵasautsa Aisraele onse amene anali patsidya pa mtsinje wa Yordani m'dziko la Aamori, ku Giliyadi.
9
Ndipo Aamoni adaoloka mtsinje wa Yordani kukamenyana nkhondo ndi fuko la Yuda, la Benjamini ndiponso la Efuremu, kotero kuti Aisraele adazunzika kwambiri.
10
Tsono Aisraele adalira kwa Chauta nati, “Takuchimwirani popeza kuti tasiya Inu Mulungu wathu ndipo tatumikira Abaala.”
11
Chauta adafunsa Aisraele kuti, “Kodi suja Ine ndidakupulumutsani kwa Aejipito, Aamori, Aamoni ndi Afilisti?
12
Pamene Asidoni, Aamaleke ndi Amaoni, adaakusautsani, inu nkundilirira kuti ndikuthandizeni, suja Ine ndidakupulumutsani kwa anthu amene aja?
13
Komabe Ine mwandisiya, mukutumikira milungu ina. Nchifukwa chake sindidzakupulumutsaninso.
14
Pitani mukalirire milungu imene mwaisankhulayo. Ikupulumutseni milungu imeneyo pa nthaŵi ya kuzunzika kwanu.”
15
Apo Aisraele adayankha Chauta kuti, “Ai, tachimwadi ife, tichiteni zimene zikukomereni. Tapota nanu, mungotipulumutsako lero lokha.”
16
Choncho adachotsa milungu yachilendo pakati pao nayamba kutumikira Chauta, ndipo Chauta adamva chisoni poona Aisraele akuzunzika.
17
Nthaŵi imeneyo Aamoni adasonkhana kuti adzamenye nkhondo, ndipo adakamanga zithando zankhondo ku Giliyadi. Aisraele nawonso adasonkhana nakamanga zithando zao ku Mizipa.
18
Tsono anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi adayamba kufunsana kuti, “Kodi munthu woti ayambe kumenyana ndi Aamoniŵa ndani? Iyeyo ndiye amene akhale mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21