bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 12
Judges 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 13 →
1
Aefuremu adakonzeka kuti akamenye nkhondo, ndipo adaolokera ku Zafoni nakafunsa Yefita kuti, “Chifukwa chiyani udaaoloka kukamenya nkhondo ndi Aamoni, ife osatiitana kuti tipite nao? Tikutenthera m'nyumba mwakomu.”
2
Yefita adaŵauza kuti, “Ine ndi anthu anga tidaakangana kwambiri ndi Aamoni. Ndidakuitanani, koma inu simudadzandipulumutse kwa iwowo.
3
Ndipo nditaona kuti simunkafuna kundipulumutsa, ndidangochita utotomoyo nkuwoloka Yordani kukalimbana nawo Aamoni. Chauta adatithandiza kuŵagonjetsa. Chifukwa chiyani tsono mwabwera kwa ine lero lino kuti mudzachite nane nkhondo?”
4
Tsono Yefita adasonkhanitsa anthu onse a ku Giliyadi namenyana nkhondo ndi Aefuremu. Ndipo Agiliyadi adagonjetsa Aefuremu chifukwa chakuti Aefuremuwo ankati, “Inu Agiliyadi ndinu othaŵa ku Efuremu, ochokera pakati pa Aefuremu ndi Amanase.”
5
Ndipo Agiliyadi adalanda Aefuremu madooko a mtsinje wa Yordani. Pamene aliyense wothaŵa ku Efuremu ankati, “Ndiloleni ndiwoloke,” Agiliyadi ankamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Mwefuremu?” Iye akayankha kuti, “Ai”,
6
iwo ankamuuza kuti, “Chabwino, nena kuti, ‘Shiboleti.’ ” Munthuyo ankati, “Siboleti,” pakuti sankatha kutchula bwino mauwo. Ankamugwira ndi kumupha pompo pa madooko a mtsinje wa Yordani. Nthaŵi imeneyo adaphedwa Aefuremu 42,000.
7
Yefita adaweruza Aisraele zaka zisanu ndi chimodzi. Pambuyo pake Yefita, amene anali Mgiliyadi, adamwalira, ndipo adaikidwa mu mzinda wake wa Giliyadi.
8
Atafa Yefita, Ibizani wa ku Betelehemu adaweruza Aisraele.
9
Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu ndiponso ana aakazi makumi atatu. Adakwatitsa ana aakazi makumi atatuwo kwa anthu osakhala a fuko lake, ndipo adakatengera ana ake aamuna aja ana aakazi makumi atatu a fuko lachilendo. Ibizaniyo anali mtsogoleri wa Aisraele zaka zisanu ndi ziŵiri.
10
Pambuyo pake adamwalira, ndipo adaikidwa ku Betelehemu.
11
Ibizani atafa, Eloni Mzebuloni adasanduka mtsogoleri wa Aisraele. Iyeyu adatsogolera Aisraele zaka khumi.
12
Pambuyo pake adamwalira, naikidwa ku Ayaloni m'dziko la Zebuloni.
13
Atafa iyeyo, Abidoni mwana wa Hilele Mpiratoni, adatsogolera Aisraele.
14
Iye anali ndi ana aamuna makumi anai ndi adzukulu makumi atatu amene ankakwera pa abulu makumi asanu ndi aŵiri. Iye adatsogolera Aisraele zaka zisanu ndi zitatu.
15
Ndipo Abidoniyo adamwalira, naikidwa ku Piratoni m'dziko la Efuremu, ku mapiri a Aamaleke.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21