bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 14
Judges 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 15 →
1
Samisoni adapita ku Timna ndipo kumeneko adaonako mtsikana wachifilisti.
2
Atabwerera kwao adakauza bambo ndi mai wake kuti, “Ku Timna ndaonako mtsikana wachifilisti. Mukanditengere ameneyo, ndidzamkwatire.”
3
Koma bambo ndi mai wake adamufunsa kuti, “Kodi palibe mkazi woti ungakwatire pakati pa ana a achibale akoŵa kapena pakati pa anthu a mtundu wathu, kuti uzikatenga mkazi pakati pa Afilisti, anthu osaumbalidwa?” Koma Samisoni adauza bambo wake kuti, “Ine ndiye kanditengereni yemweyo, pakuti ndiye ndamkonda kwambiri.”
4
Bambo ndi mai wake sankadziŵa kuti zimenezo zinali zochokera kwa Chauta, pakuti Chauta ankafunafuna poŵapezera chifukwa Afilistiwo. Nthaŵi imeneyo nkuti Afilisti akulamulira Aisraele.
5
Tsono Samisoni adapita ku Timna pamodzi ndi bambo ndi mai wake. Atafika ku minda yamphesa ya ku Timna, Samisoni adamva mwanawamkango akumdzumira.
6
Pamenepo Mzimu wa Chauta udamtsikira Samisoni ndi kumsandutsa wankhongono. Motero ngakhale analibe chida m'manja, Samisoni adakadzula mkangowo, monga momwe munthu amakadzulira kamwanakambuzi. Koma sadauze bambo kapena mai wake zimene adachitazo.
7
Tsono Samisoni adapita kukalankhula naye mtsikana uja, ndipo adamkonda kwambiri mtsikanayo.
8
Patapita kanthaŵi Samisoni adabwerera kudzamtenga mtsikanayo. Pa njira adapatuka kukaona mkango adaaupha uja. Adangoona njuchi zili mu mkangowo pamodzi ndi uchi wake.
9
Samisoni adafula njuchizo, natenga uchi m'manja ndi kumapita naadya. Atafika kwa bambo ndi mai wake, adaŵapatsako uchiwo, iwo naadya. Koma sadaŵauze kuti uchiwo adaufula mu mkango wakufa.
10
Bambo wakeyo adapita kunyumba kwa mkazi uja, ndipo Samisoni adakonza phwando kumeneko, pakuti ndi m'mene ankachitira anyamata.
11
Pamene anthu adamuwona, adabwera ndi anyamata makumi atatu kuti akhale naye.
12
Samisoni adaŵauza kuti, “Bwanji ndikuphereni mwambi! Mukandiwuza tanthauzo lake, asanapite masiku asanu ndi aŵiri a phwando, ndidzakupatsani zovala zabafuta makumi atatu ndiponso zovala za tsiku lachikondwerero makumi atatu.
13
Koma mukalephera kundiwuza tanthauzo lake, mudzandipatsa ndinu zovala zabafuta makumi atatu, ndiponso zovala za tsiku lachikondwerero makumi atatu.” Iwo adamuyankha kuti, “Tiphere mwambiwo, tiwumve.”
14
Tsono adaŵauza kuti, “M'chodya zinzake mudatuluka chakudya. M'champhamvu mudatuluka chozuna.” Pa masiku atatu, anthuwo sadathe kuumasula mwambiwo.
15
Tsiku lachinai lake iwo adauza mkazi wa Samisoni kuti, “Umunyengerere mwamuna wako, kuti atiwuze tanthauzo lake la mwambi uja, mwinamwina tikutentha iweyo pamodzi ndi nyumba ya bambo wako. Monga inu mwatiitana kuno kuti mutisandutse osauka?”
16
Choncho mkazi wa Samisoni adayamba kulira pamaso pa mwamuna wake namuuza kuti, “Inu mumadana nane, simundikonda konse. Mwaŵaphera mwambi anthu a m'dziko mwangaŵa, koma ine osandiwuzako tanthauzo lake.” Apo Samisoni adamuuza kuti, “Ona, ngakhale bambo wanga ndi mai wanga sindidaŵauze, ndiye ndingauze iweyo?”
17
Mkaziyo ankangomulirira masiku onse asanu ndi aŵiri aphwandowo. Tsono pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adamuuza, chifukwa chakuti adaamkakamiza kwambiri. Pompo mkaziyo adakauza anthu a m'dziko mwake aja tanthauzo la mwambiwo.
18
Choncho anthu amumzinda aja adauza Samisoni pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri dzuŵa lisanaloŵe, kuti, “Nchiyani chozuna kuposa uchi? Nchiyani champhamvu kuposa mkango?” Samisoni adaŵauza kuti, “Mukadapanda kulima ndi msotiwang'ombe wanga, simukadatha kumasula mwambi wangawu.”
19
Apo Mzimu wa Chauta udamtsikira Samisoni mwamphamvu ndipo Samisoniyo adapita ku Asikeloni nakapha anthu makumi atatu am'mudzimo ndipo adatenga zovala zao za tsiku lachikondwerero, nazipereka kwa amene adamasula mwambi aja. Ndipo adabwerera ku nyumba ya bambo wake ali wokwiya kwambiri.
20
Nthaŵi yomweyo mkazi wa Samisoni uja bambo wake adamkwatitsa kwa mnzake wa Samisoniyo amene adaali mnzake womuperekeza paukwati paja.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21