bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 17
Judges 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 18 →
1
Ku dziko lamapiri la Efuremu kunali munthu wina dzina lake Mika.
2
Iyeyu adauza mai wake kuti, “Pamene munthu adaakuberani ndalama zasiliva 1,100, inu mudaamutemberera wakubayo, matembererowo ine ndidaŵamva. Ndalamazo ndi izi, zili ndi ine. Ndine ndidaatenga.” Mai wakeyo adamuuza kuti, “Chauta akudalitse mwana wanga.”
3
Tsono iye adabwezera ndalama zonse kwa mai wake, ndipo maiyo pofuna kuchotsa temberero lija, adati, “Ndikuzipatula ndalama zasilivazi kuti zikhale za Chauta. Ndidzazipereka kuti aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Choncho ndikubwezera ndalamazo.”
4
Tsono Mika atabweza ndalamazo kwa mai wake, mai wakeyo adatengapo ndalama zasiliva 200 nazipereka kwa mmisiri wosula siliva. Munthuyo adasema fano nasungunula ndalamazo, nakutira fanolo ndi siliva. Ndipo Mika adaliimika m'nyumba mwake.
5
Mikayo anali ndi kachisi wakewake, ndipo adapanga chovala chaunsembe cha efodi ndiponso mafano am'nyumba otchedwa terafimu, nakhazika mmodzi mwa ana ake kuti akhale wansembe wake.
6
Masiku amenewo ku Israele kunalibe mfumu. Munthu aliyense ankangochita zimene zinkamkomera.
7
Ku Betelehemu m'dziko la Yuda kunali mnyamata wina wa fuko la Yuda amene anali Mlevi.
8
Munthuyo adachoka ku mudzi wa Betelehemu uja ku Yuda, kukafunafuna kwina kokakhala. Akuyenda ulendo wakewo adakafika ku dziko lamapiri la ku Efuremu ku nyumba ya Mika.
9
Mika uja adamufunsa kuti, “Kodi inu kwanu nkuti?” Munthuyo adayankha kuti, “Ine ndine Mlevi wa ku Betelehemu m'dziko la Yuda, ndikufunafuna koti ndikhale nao.”
10
Apo Mika adamuuza kuti, “Khalani ndi ine, mukhale mlangizi wanga ndi wansembe wanga, ine ndizikupatsani ndalama zasiliva khumi pa chaka, ndizikupatsaninso zovala ndi zakudya.”
11
Mleviyo adavomera kukhala naye munthuyo, ndipo adasanduka ngati mmodzi mwa ana ake.
12
Tsono Mika adalonga Mleviyo unsembe, ndipo iyeyo ankakhala m'nyumba mwa Mika.
13
Apo Mika adati, “Tsopano ndikudziŵa kuti Chauta adzandilemeza, popeza kuti Mleviyu ndiye wansembe wanga.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21