bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 5
Judges 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 6 →
1
Tsiku limenelo la kupambana kwa Debora ndi Baraki, mwana wa Abinowamu, adaimba nyimbo iyi yakuti,
2
“Pakuti atsogoleri adatsogoleradi m'dziko la Israele, ndipo anthu adadzipereka okha mwaufulu, tamandani Chauta.
3
“Imvani, inu mafumu, tcherani khutu, inu olamulira. Ndidzaimba nyimbo yokoma, kuimbira Chauta, Mulungu wa Israele.
4
“Inu Chauta, pamene munkatuluka m'Seiri, pamene munkayenda kuchokera ku Edomu, dziko lidagwedezeka, kumlengalenga kudanjenjemera, mitambo idasungunuka nigwetsa madzi.
5
Mapiri adagwedezeka pamaso pa Chauta, phiri la Sinai lidagwedezeka pamaso pa Chauta, Mulungu wa Aisraele.
6
“Pa nthaŵi ya Samigara, mwana wa Anati, pa nthaŵi ya Yaele, m'miseu munali zii, alendo ankangolambalala m'tinjira takumbali.
7
Anthu adaathaŵa ku midzi, midzi idaatha ku Israele, mpaka pamene iwe Debora udafika, udafika ngati mai ku Israele.
8
Pamene anthu adasankhula milungu ina, nkhondo idafika m'dziko. Mwa anthu 40,000 ku Israele, ndani adatenga chishango kapena mkondo?
9
Mtima wanga uli ndi atsogoleri a ankhondo a ku Israele, uli ndi anthu amene adadzipereka mwaufulu, kudzipereka mwaufulu pakati pa anzao. Tamandani Chauta!
10
“Inu okwera pa abulu oyera ambee, inu okwera pa zishalo, ndi inu oyenda pa mseu, musimbe zimenezi.
11
Ku zitsime oimba akuimba nyimbo zokondwerera kuti Chauta wagonjetsa, zokondwerera kuti anthu ake ku Israele apambana.” “Tsono anthu a Chauta adasonkhana kuchokera ku midzi yao.
12
“Adati, ‘Tsogolera ndiwe Debora, tsogolera, tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo. Pita patsogolo Baraki, tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinowamu.’ ”
13
Pambuyo pake anthu okhulupirika adabwera kwa atsogoleri ao, anthu a Chauta adapita kukamenyera Chauta nkhondo, polimbana ndi adani amphamvu.
14
Adakaloŵa m'chigwa kuchokera ku Efuremu, akukutsata iwe Benjamini, pamodzi ndi achibale ako. Kwa Makiri kudachokera atsogoleri a ankhondo, kwa Zebuloni kudachokera onyamula ndodo yaudindo.
15
Olamulira a Isakara adabwera ndi Debora, anthu a kwa Isakara adatsatanso Baraki, nathamangira ku zigwa akumutsata. Anthu a fuko la Rubeni anali osiyana maganizo, osadziŵa chenicheni choyenera kuchita.
16
Chifukwa chiyani ankachedwa ku makola a nkhosa, kumangomvetsera zitoliro zoitanira nkhosa? Anthu a fuko la Rubeni anali osiyana maganizo, osadziŵa chenicheni choyenera kuchita.
17
Agiliyadi adatsala patsidya pa Yordani. Nawonso anthu a kwa Dani, chifukwa chiyani ankachedwa m'zombo? Aasere ankangokhala m'madooko pa gombe la nyanja, ankangokhala m'madooko mwao.
18
Azebuloni ndi fuko limene lidaika moyo wake m'zoopsa. Nawonso Anafutali adaika moyo wao pa minga, pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri.
19
“Mafumu adabwera namenya nkhondo, mafumu a ku Kanani adamenya nkhondo ku Taanaki pafupi ndi madzi a ku Megido, koma sadapateko zofunkha zasiliva, kapena china chilichonse.
20
Ngakhale nyenyezi zakumwamba zidamenya nkhondo, zidathira nkhondo Sisera, zikuyenda m'njira zake mu mlengalenga.
21
Chigumula cha madzi a mtsinje wa Kisoni chidaŵakokolola onsewo, madzi othamanga, madzi amphamvu a Kisoni. Mtima wanga, limbika, yenda mwamphamvu!
22
“Tsono ziboda za akavalo zidamveka kwambiri, akavalo ali paliŵiro, akuthamanga kwambiri.
23
“Mngelo wa Chauta akuti, ‘Utemberere Merozi, utemberere koopsa nzika zake, chifukwa chakuti sizidabwere kudzathandiza Chauta, pakulimbana ndi adani ake amphamvu.’
24
“Yaele, mkazi wa Hebere Mkeni, akhale wodala kupambana akazi onse, ndithudi akhale wodala kupambana akazi onse am'dziko.
25
Munthu uja adapempha madzi akumwa, koma Yaele adamupatsa mkaka, adamupatsa chambiko m'chikho chachifumu.
26
Adatenga chikhomo cha hema natenganso nyundo m'dzanja lake lamanja, adakhoma nacho Sisera, naphwanya mutu wake, adamutswanya ndi kumuboola m'litsipa mwake.
27
Sisera adathifuka naagwa; adangoti thasa ku mapazi a Yaele. Adathifukadi nagwera ku mapazi a Yaele. Kumene adaathifukirako, adagwera komweko, naafa.”
28
Mai wake a Sisera adasuzumira pa zenera, nanena kuti, “Chifukwa chiyani galeta lake silikufika msanga? Bwanji mdidi wa akavalo a magaleta ake ukuchedwa?
29
Amai ake anzeru kopambana adamuyankha, mwiniwake yemwenso adadziyankha yekha kuti,
30
‘Kodi sakufunafuna zofunkha kuti agaŵane? Akugaŵira wankhondo aliyense mkazi mmodzi kapena aŵiri. Akugaŵira Sisera zofunkha, zovala zonyika mu utoto, zovala zopeta zonyika mu utoto, zovala ziŵiri zonyika mu utoto, zopeta kuti ndizivala m'khosi?’
31
“Motero Inu Chauta, adani anu aonongeke! Koma abwenzi anu akhale ngati dzuŵa lotuluka ndi mphamvu zake zonse.” Tsono dziko lidakhala pa mtendere zaka makumi anai.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21