bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 13
Judges 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 14 →
1
Aisraele adachimwiranso Chauta. Ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Afilisti pa zaka makumi anai.
2
Ku Zora kunali munthu wina, wa fuko la Dani, dzina lake Manowa. Mkazi wake analibe ana, anali wosabereka.
3
Mngelo wa Chauta adamuwonekera mkaziyo namuuza kuti, “Inu mai, ngakhale mpaka pano muli opanda ana, komabe mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna.
4
Ndiye inu mudzisamale bwino, musamamwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa, ndipo musamadye chakudya chilichonse chosaloledwa.
5
Pakuti ndithu mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa, kumutu kwake kusadzapite lumo, pakuti mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulikira Mulungu kuyambira tsiku la kubadwa kwake. Ndipo adzayambapo ntchito yopulumutsa Aisraele kwa Afilisti.”
6
Tsono mkaziyo adadzauza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kuno, ndipo nkhope yake inali yoopsa kwambiri ngati nkhope ya mngelo wa Mulungu. Sindidamufunse kumene akuchokera, iyenso sadandiwuze dzina lake.
7
Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Ndiye musamamwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa, ndipo musamadye chakudya chosaloledwa chilichonse, chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, wopatulikira Mulungu, kuyambira tsiku la kubadwa kwake mpaka tsiku la kufa kwake.’ ”
8
Tsono Manowa adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, ndapota nanu, mulole kuti munthu amene mudaamtuma uja abwerenso, adzatiphunzitse zimene tiyenera kuchita naye mnyamata amene adzabadweyo.”
9
Mulungu adamvera pemphero la Manowa, ndipo mngelo wa Mulungu uja adabweranso kwa mkaziyo nampeza atakhala pansi m'munda. Koma mwamuna wake Manowa sanali nao.
10
Mkazi uja adathamanga nakauza mwamuna wake kuti, “Munthu uja adaabwera kuno tsiku lijaliyu wandiwonekeranso.”
11
Apo Manowa adanyamuka natsata mkazi wake, ndipo adakafika kumene kunali munthuyo nakamufunsa kuti, “Kodi inu ndinu amene mudaalankhula ndi amaiŵa?” Iye adayankha kuti, “Inde ndinedi.”
12
Manowa adamufunsa kuti, “Tsono zimene mudanenazi zikadzachitikadi, kodi mnyamatayo azidzakhala bwanji, ndipo azidzachita chiyani?”
13
Mngelo wa Chauta uja adauza Manowa kuti, “Zonse zimene ndidaŵauza amaiŵa asamale kuti azichitadi.
14
Asati adye chilichonse chochokera ku mphesa, ndipo asati amwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa kapenanso kudya chinthu chosaloledwa chilichonse. Asunge zonse zimene ndidaŵalamula.”
15
Manowa adauza mngelo wa Chauta kuti, “Pepani, tayambani mwaima, tikuti tikuwotchereni kamwanakambuzi.”
16
Koma mngelo wa Chauta adauza Manowa kuti, “Ngakhaletu mukundidikiritsa chakudyacho, ine sindidya ai. Koma ngati mukonze nsembe yopsereza, muipereke kwa Chauta.” (Monsemo nkuti Manowa ali wosazindikira kuti mlendoyo ndi mngelo wa Chauta.)
17
Apo Manowa adauza mngeloyo kuti, “Timati mutiwuze dzina lanu kuti tidzakulemekezeni, zikadzachitikadi zimene mwanenazi.”
18
Mngelo wa Chautayo adafunsa Manowa kuti, “Chifukwa chiyani mukufuna kudziŵa dzina langa? Dzina laketu nlodabwitsa.”
19
Pamenepo Manowa adatenga kamwanakambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya, nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Chauta, Iye amene amachita zodabwitsa.
20
Pamene malaŵi a moto ankakwera kumwamba kuchokera paguwapo, mngelo wa Chauta uja adakwera m'malaŵi a motowo, Manowa ndi mkazi wake akuyang'ana. Apo iwo adadzigwetsa pansi, naŵeramitsa mitu pansi.
21
Mngelo wa Chauta uja sadaŵaonekerenso Manowa ndi mkazi wake. Choncho Manowa adazindikira kuti anali mngelo wa Chauta.
22
Tsono adauza mkazi wake kuti, “Ife ndiye tifatu basi, nanga sitaona Mulungu!”
23
Koma mkazi wake adati, “Akadakhala kuti Chauta akufuna kutipha, sakadailandira nsembe yathu yopsereza ndi chopereka chathu cha chakudya chija. Ndiponso sakadatiwonetsa zinthu zonsezi kapenanso kutiwuza tsopano zinthu zonga ngati zimenezi.”
24
Motero mkaziyo adabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Samisoni. Mnyamatayo adakula ndipo Chauta adamdalitsa.
25
Ndipo Mzimu wa Chauta udayamba kumlimbitsa pamene anali ku zithando za anthu a fuko la Dani, pakati pa Zora ndi Esitaoli.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21