bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 20
Judges 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 21 →
1
Aisraele onse adanyamuka kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, kudzanso dziko la Giliyadi, ndipo adasonkhana pamaso pa Chauta ku Mizipa.
2
Atsogoleri a anthu onse ndi a mafuko onse a Aisraele adabwera ku msonkhano wa anthu a Mulungu. Onse pamodzi analipo 400,000 oyenda pansi omenya nkhondo ndi lupanga.
3
M'menemo nkuti anthu a fuko la Benjamini atamva kuti Aisraele apita ku Mizipa. Tsono Aisraele adati, “Tiwuze, kodi zoipa zoterezi zachitika bwanji?”
4
Apo Mlevi uja, mwamuna wa mkazi wophedwayo, adati, “Ndidafika ku Gibea, mzinda wa Abenjamini, ineyo ndi mzikazi wanga, kuti tigone kumeneko.
5
Anthu a ku Gibea adandiwukira nazinga nyumba imene munali ine nthaŵi ya usiku. Ankafuna kundipha ndipo adamchita zoipa mzikazi wangayo mwakhakhamizo mpaka iye adafa.
6
Ndidamtenga mzikaziyo ndi kumduladula nthulinthuli, nkuzitumiza kwa fuko lililonse la Aisraele. Ndithudi anthu amene aja achita zinthu zonyansa ndi zoipa kwabasi m'dziko lino la Israele.
7
Nzimenezotu, inu Aisraele, ndikuuza nonsenu, mupereke malangizo anu ndipo mupangane pompano.”
8
Anthu onse adadzuka pamodzi nati, “Palibe munthu ndi mmodzi yemwe mwa ife amene apite ku hema lake, palibe amene abwerere kunyumba kwake.
9
Koma tsono zimene tiŵachite anthu a ku Gibea ndi izi: tipita kukalimbana nawo mzindawo potsata zimene maere atiwuze.
10
M'mafuko onse a Aisraele tisankhula anthu khumi pa anthu 100 aliwonse. Ameneŵa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Gibea, mzinda wa ku Benjamini, chifukwa cha tchimo lao lonyansa zedi limene adachita m'dziko la Israele.”
11
Motero Aisraele onse adasonkhana atagwirizana chimodzi pofuna kulimbana nawo mzindawo.
12
Mafuko a Aisraele adatuma anthu kwa fuko lonse la Benjamini, kuti akafunse kuti, “Kodi zoipa zimene mwachita pakati panupazi nzotani?
13
Ndiye ife tsopano tikuti mubwere nawo anthuwo, anthu achabechabe aja a ku Gibea, kuti tiŵaphe, kuti potero tichotse kulaulaku m'dziko la Israele.” Koma Abenjamini sadafune kumva mau a Aisraele, abale ao.
14
Choncho Abenjamini onse adatuluka m'mizinda yao ku Gibea kukamenyana nkhondo ndi Aisraele.
15
Tsiku limenelo Abenjamini adasonkhanitsa ankhondo 26,000, osaŵerenga anthu ena a ku Gibea 700 osankhidwa.
16
Mwa anthu onseŵa panali anthu 700 amanzere, amene ankatha kulasa ndi mwala ngakhale tsitsi limodzi, osaphonya konse.
17
Aisraele onse, kupatula Abenjamini, adasonkhanitsa anthu amalupanga 400,000, anthu ake odziŵa bwino nkhondo.
18
Aisraele adanyamuka napita ku Betele kukafunsa kwa Mulungu kuti, “Ndani mwa ife amene ayambe kukamenyana nkhondo ndi Abenjamini?” Chauta adayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo limene liyambe.”
19
Tsono Aisraele adadzuka m'maŵa nakamanga zithando zao moyang'anana ndi Gibea.
20
Aisraele adapita kukamenyana nkhondo ndi Abenjamini, nakhazika ankhondo ao kuyang'ana mzinda wa Gibea.
21
Nawonso Abenjamini adatuluka ku Gibea ndipo tsiku limenelo adapha Aisraele 22,000.
22
Koma Aisraelewo adalimbitsana mtima ndipo adakhazika ankhondo ao kachiŵiri pa malo omwe aja pamene adaaŵakhazika tsiku loyamba lija.
23
Tsono Aisraelewo adapita kukalira pamaso pa Chauta mpaka madzulo. Adakafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kachiŵiri kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu?” Chauta adayankha kuti, “Inde pitani mukamenyane nawo.”
24
Choncho Aisraele adafika pafupi, kuti akalimbane ndi Abenjamini tsiku lachiŵiri lake.
25
Abenjamini adatulukanso mu mzinda wa Gibea, kukalimbana nawo tsiku lachiŵirilo, ndipo adapha ankhondo a Aisraele 18,000.
26
Tsono Aisraele onse, ndiye kuti gulu lonse la ankhondo, adapita ku Betele ndi kukalira kumeneko. Adakhala pansi pamaso pa Chauta, nasala chakudya tsiku limenelo mpaka madzulo, ndipo adapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere pamaso pa Chauta.
27
Bokosi lachipangano la Chauta linali kumeneko masiku amenewo.
28
Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni, ndiye ankayang'anira bokosilo masiku amenewo. Choncho Aisraele adafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu, kapena tingoleka?” Chauta adayankha kuti, “Pitaninso, pakuti maŵa ndidzaŵapereka m'manja mwanu.”
29
Choncho Aisraele adaika anthu obisalira mozungulira mzinda wa Gibea.
30
Adapita kukamenyana ndi Abenjamini tsiku lachitatu lake, nakhazika ankhondo ao kuti athire nkhondo mzinda wa Gibea monga masiku ena aja.
31
Abenjamini nawonso adatuluka kukamenyana nawo anthuwo, napita chapatali ndithu ndi mzindawo. Ndipo monga mwa masiku onse, adayamba kuŵamenya koopsa ndi kupha Aisraele makumi atatu amene anali m'miseu yaikulu, ena mu mseu waukulu wa ku Betele, ena mu mseu waukulu wa ku Gibea ndiponso ena kwina koyera.
32
Ndipo adati, “Taŵapirikitsa monga poyamba paja.” Koma Aisraele adati, “Tiyeni tithaŵe kuti apite ku miseu chapatali ndithu ndi mzinda wao.”
33
Choncho Aisraelewo adanyamuka m'malo ao, nakandanda ku Baala-Tamara. Pamenepo Aisraele amene adaabisalira aja adatuluka m'malo ao kuzambwe kwa Geba.
34
Aisraele osankhidwa amene adabwera kudzalimbana ndi mzinda wa Gibea analipo 10,000, ndipo nkhondo idalimba kumeneko. Koma Abenjamini sankadziŵa kuti zoopsa zili pafupi kuŵagwera.
35
Tsono Chauta adagonjetsa Abenjamini pamaso pa Aisraele, ndipo Aisraelewo adaononga ankhondo a Abenjamini okwanira 25,100 tsiku limenelo.
36
Motero Abenjamini adaona kuti agonjetsedwa. Paja gulu lalikulu la Aisraele lidaathaŵa Abenjamini chifukwa linkadalira anthu aja amene lidaaŵaika kuti abisalire mzinda wa Gibea.
37
Apo anthu obisalira aja adafulumira kuuthira nkhondo mzinda wa Gibeawo. Adapha anthu onse amumzindamo ndi lupanga.
38
Tsono chizindikiro chimene adaapangana Aisraele a gulu lalikulu ndi anthu obisalira aja chinali chakuti, akafukiza utsi wambiri ngati mtambo mumzindamo,
39
Aisraele ambiriwo abwerere kudzamenya nkhondo. M'menemo nkuti Abenjamini atayamba kuŵamenya Aisraelewo koopsa ndi kupha anthu makumi atatu. Iwo ankati, “Ndithu, taŵapha monga poyamba paja.”
40
Koma pamene utsi wachizindikiro uja udayamba kuti tolotolo kukwera kumwamba mumzindamo, Abenjamini adayang'ana kumbuyo, nkuwona mu mzinda wonsewo utsi uli tolotolo kukwera kumwamba.
41
Pomwepo Aisraele adabwerera ndipo Abenjamini adayamba kuwopa ndi kutaya mtima, pakuti adaaona kuti zoopsa zili pafupi kuŵagwera.
42
Nchifukwa chake Abenjamini adayamba kuthaŵa Aisraelewo, naloŵa njira ya ku dondo. Koma nkhondo idaŵapeza, ndipo adaphedwa ndi Aisraele amene ankatuluka mu mzinda.
43
Adaŵazinga Abenjaminiwo naŵapirikitsa ndi kuŵaonongeratu osaŵachitira chifundo mpaka ku dera la Gibea kuvuma kwake.
44
Abenjamini amene adaphedwa analipo 18,000. Onsewo anali anthu olimba mtima kwambiri.
45
Anthu amene adatsalira, adatembenuka nathaŵira ku dondo ku thanthwe la Rimoni. Mwa iwowo anthu 5,000 adaphedwa m'miseu yaikulu. Adaŵapirikitsabe Abenjaminiwo mkaka ku Gidomu, naphanso enanso 2,000.
46
Choncho Abenjamini onse amene adafa tsiku limenelo adakwanira ankhondo 25,000. Onsewo anali anthu olimba mtima kwambiri.
47
Koma anthu 600 okha adakafika ku dondo ku thanthwe la Rimoni, nakakhala ku thanthwe la Rimoniko miyezi inai.
48
Tsono Aisraele adabwerera m'mbuyo kukamenyana ndi Abenjamini otsala, naŵapha ndi lupanga, anthu ndi nyama zomwe, pamodzi ndi zonse zimene adakumana nazo. Ndipo adatentha mizinda yonse imene adaipeza.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21