bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 16
Judges 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 17 →
1
Samisoni adapita ku Gaza ndipo kumeneko adaonako mkazi wadama naloŵa m'nyumba yake.
2
Anthu a ku Gaza adauzidwa kuti, “Samisonitu adabwera kuno.” Tsono anthuwo adazinga malowo namubisalira usiku wonse pa chipata cha mzinda. Iwo adakhala chete usiku wonsewo namanena kuti, “Tiyeni tidikire mpaka m'maŵa kutacha, pamenepo timuphe.”
3
Koma Samisoni adagona mpaka pakati pa usiku. Pakati pa usikupo adadzuka, nagwira zitseko zapachipata ndi mafuremu ake onse aŵiri. Adazizula pamodzi ndi mpiringidzo ndi zina zonse. Adazisenza pa phewa, napita nazo pamwamba pa phiri loyang'anana ndi Hebroni.
4
Pambuyo pake Samisoni adayamba kukonda mkazi wina wa ku chigwa cha Soreki, dzina lake Delila.
5
Akalonga a Afilisti adabwera kwa mkaziyo namuuza kuti, “Umnyengerere mwamunayu, uwone pamene pagona mphamvu zake zoopsazi ndiponso m'mene tingathe kumpambanira, kuti timmange ndi kumgonjetsa. Ukatero, aliyense mwa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.”
6
Tsono Delila adauza Samisoni kuti, “Inu, tandiwuzani, kodi mphamvu zanu zoopsazi zagona poti? Kodi munthu atati akumangeni kuti akugonjetseni, nkofunika kuti atani?”
7
Samisoni adamuuza kuti, “Atandimanga ndi nsinga zatsopano zisanu ndi ziŵiri zosauma, ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.”
8
Tsono akalonga a Afilisti aja adadzampatsa mkaziyo nsinga zisanu ndi ziŵiri zatsopano zosauma, ndipo iye adamangira mwamuna wake.
9
Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo ataika anthu ombisalirawo m'chipinda cham'kati. Kenaka adafuula kwa mwamuna wake kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Koma iye adangomwetula nsingazo monga m'mene imamwetukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zakezo sichidadziŵikebe.
10
Apo Delila adauza Samisoni kuti, “Ndithu mwandipusitsa ndi kundinamiza. Chonde tandiwuzani m'mene munthu angakumangireni.”
11
Samisoni adauza mkaziyo kuti, “Atandimanga ndi zingwe zatsopano zimene sadazigwiritse ntchito, ndidzasanduka wofooka, ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.”
12
Choncho Delila adatenga zingwe zatsopano nammanga nazo, nafuula kwa iye kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Monsemo nkuti anthu amene ankambisalira aja ali m'chipinda cham'kati. Koma, Samisoni adangomwetula zingwezo kumanja kwake ngati thonje.
13
Pamenepo Delila adauzanso Samisoni kuti, “Mpaka tsopano lino mwakhala mukundipusitsa ndi kumandinamiza. Tandiwuzani m'mene munthu angathe kukumangirani.” Samisoni adamuuza kuti, “Ngati njombi zisanu ndi ziŵiri za kumutu kwanga uzilukirira m'cholukira nsalu ndi kuchimanga molimbika ndi chikhomo, ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi anthu ena.”
14
Choncho pamene Samisoni ankagona, Delila adatenga njombi za kumutu kwa Samisoni nazilukirira m'cholukira nsalu. Ndipo adachimanga molimbika ndi chikhomo nafuula kwa Samisoni kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Koma iye adadzukira kutulo nazula chikhomocho, ndipo njombi zake zidachoka m'cholukira chija.
15
Apo mkaziyo adamufunsa kuti, “Mungathe bwanji kunena kuti mumandikonda pamene mtima wanu suli pa ine? Mwakhala mukundipusitsa katatu konseka, ndipo simudandiwuze pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi.”
16
Tsono pamene adampanikiza ndi mau ake tsiku ndi tsiku ndi kumkakamiza, mtima wa Samisoni udatopa mpaka kufuna kufa.
17
Choncho adamuululira mkaziyo maganizo ake onse namuuza kuti, “Pamutu pangapa sipanapite lumo, popeza kuti ndakhala ndili Mnaziri wopatulikira Mulungu, kuyambira ndili m'mimba mwa mai wanga. Atangondimeta tsitsi langali, mphamvu zanga zidzandichokera. Ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.”
18
Pamene Delila adaona kuti waulula maganizo ake onse, adatuma uthenga kukaŵaitana akalonga a Afilisti aja ndipo adaŵauza kuti, “Bweraninso kamodzi kokha, pakuti wandiwululira maganizo ake onse.” Tsono akalonga a Afilisti adafika kwa mkazi uja atatenga ndalama m'manja mwao.
19
Mkaziyo adamgonetsa tulo Samisoni pamiyendo pake. Ndipo adaitana munthu kuti amete njombi zisanu ndi ziŵiri za kumutu kwa Samisoni. Pamenepo iyeyo adayamba kufooka ndipo mphamvu zake zidamchokera.
20
Kenaka Delila adafuula kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Samisoni adadzuka akuganiza kuti, “Ndituluka monga momwe ndimachitira nthaŵi zonse, ndipo ndidzimasula.” Koma sadadziŵe kuti Chauta wamsiya.
21
Pompo Afilisti adamgwira namkoloola maso ake, ndipo adapita naye ku Gaza atammanga ndi maunyolo amkuŵa. Kumeneko ankapera pa mphero m'ndende.
22
Pambuyo pake tsitsi la kumutu kwake lomwe adaalimeta, lidayamba kumeranso.
23
Tsiku lina akalonga a Afilisti adasonkhana kudzapereka nsembe yaikulu kwa Dagoni mulungu wao ndi kudzakondwerera, pakuti ankati, “Mulungu wathu watithandiza kugonjetsa Samisoni, mdani wathu.”
24
Pamene anthu adamuwona, adayamba kutamanda mulungu wao. Ankati, “Mulungu wathu watithandiza kugonjetsa mdani wathu, munthu woononga dziko lathu uja amene adapha anthu ambiri.”
25
Pamene mitima yao inkasangalala adati, “Muitaneni Samisoni kuti adzatisangalatse.” Choncho adamtulutsa m'ndende, ndipo iye adayamba kuŵasangalatsa. Kenaka adamuimiritsa pakati pa mizati.
26
Apo Samisoni adauza mnyamata amene adamgwira dzanja kuti, “Undilole ndikhudze mizati imene yachirikiza nyumba yonseyi, kuti ndiitsamire.”
27
M'menemo nkuti nyumbayo ili yodzaza ndi anthu, amuna ndi akazi. Akalonga onse a Afilisti anali momwemo, ndipo padenga pake panali pafupi anthu 3,000, amuna ndi akazi, amene ankaonera Samisoni akuseŵera.
28
Tsono Samisoni adatama Chauta mopemba nati, “Inu Chauta, kumbukireni kamodzi kokhaka, ndapota nanu, ndipo mundilimbitse Inu Mulungu, kuti ndiŵalipsire Afilistiŵa chifukwa cha maso anga aŵiriŵa.”
29
Pomwepo Samisoni adagwira mizati iŵiri yapakati imene inkachirikiza nyumbayo. Adaitsamira ndi mphamvu zake zonse, dzanja lake lamanja lili pa mzati wina, lamanzere lili pa mzati winanso.
30
Ndipo Samisoni adati, “Ndifere kumodzi ndi Afilistiŵa.” Tsono adakankha ndi mphamvu zake zonse, ndipo nyumbayo idaŵagwera akalonga aja pamodzi ndi anthu onse aja amene anali m'menemo. Choncho kuchuluka kwa anthu amene Samisoni adaŵapha pa nthaŵi ya kufa kwake kudaposa kwa anthu amene iye adaŵapha pa nthaŵi imene anali moyo.
31
Tsono abale a Samisoni adabwera pamodzi ndi banja lao lonse kudzamtenga ndipo adakamuika pakati pa Zora ndi Esitaoli, m'manda a Manowa bambo wake. Samisoni adatsogolera Aisraele zaka makumi aŵiri.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21