bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 4
Judges 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 5 →
1
Ehudi atamwalira, Aisraele adachitanso zinthu zoipira Chauta.
2
Ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanani, amene ankalamulira ku Hazori. Mtsogoleri wa ankhondo ake anali Sisera amene ankakhala ku Haroseti-Goimu.
3
Tsono Aisraele adalira kwa Chauta kuti aŵathandize, pakuti Sisera anali ndi magaleta achitsulo okwanira 900, ndipo adaazunza Aisraele mwankhalwe zaka makumi aŵiri.
4
Nthaŵi imeneyo Debora mneneri wamkazi, mkazi wa Lapidoti, ndiye amene ankatsogolera Aisraele.
5
Iye ankakhala patsinde pa mtengo wa mgwalangwa wa Debora, pakati pa Rama ndi Betele, m'dziko lamapiri la Efuremu, ndipo Aisraele ankabwera kwa iye kuti aŵaweruze.
6
Deborayo adatuma munthu kuti akaitane Baraki, mwana wa Abinowamu, wa ku Kedesi m'dziko la Nafutali. Baraki atabwera, Debora adamuuza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akukulamula kuti, ‘Pita ukasonkhanitse anthu ako ku phiri la Tabori, ndipo utenge anthu 10,000 m'fuko la Nafutali ndi m'fuko la Zebuloni.
7
Ine ndidzamkopa Sisera, mtsogoleri wa ankhondo a Yabini, kuti adzakumane nanu ku mtsinje wa Kisoni, atatenga magaleta ake ndi ankhondo ake, ndipo ndidzampereka m'manja mwanu.’ ”
8
Baraki adayankha kuti, “Mukapita, nanenso ndipita, koma mukapanda kupita, inenso sindipita.”
9
Debora adati, “Chabwino, ndipita nanu, komatu inu simudzalandirapo ulemu mutapambana, pakuti Chauta adzapereka Sisera m'manja mwa munthu wamkazi.” Tsono Debora adanyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki.
10
Baraki adaitana mafuko a Zebuloni ndi a Nafutali kuti abwere ku Kedesi. Anthu amene adamtsata analipo 10,000, ndipo Debora adapita nawo limodzi.
11
Nthaŵi imeneyo Mkeni wina, dzina lake Hebere, anali atadzipatula mwa Akeni anzake, zidzukulu za Hobabu, mlamu wa Mose, ndipo adakamanga hema lake kutali, pafupi ndi mtengo wa thundu ku Zananimu, pafupi ndi Kedesi.
12
Tsono pamene Sisera adamva kuti Baraki, mwana wa Abinowamu, wapita ku phiri la Tabori,
13
adaitanitsa magaleta ake achitsulo 900 onse aja ndi anthu onse amene anali naye. Iwo adanyamuka kuchokera ku Haroseti-Goimu mpaka ku mtsinje wa Kisoni.
14
Debora adauza Baraki kuti, “Dzukani, ndi lero tsiku limene Chauta wapereka Sisera m'manja mwanu. Kodi suja Chauta wakutsogolerani kale?” Pamenepo Baraki adatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumtsata.
15
Ndipo Chauta adasokoneza Sisera ndi magaleta ake onse, pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi ankhondo ake ankaŵatsata pambuyo alikupha anthu ambiri. Sisera adatsika pa galeta lake nayambapo kuthaŵa pansi.
16
Baraki adalondola magaletawo ndi ankhondowo mpaka ku Haroseti-Goimu, ndipo ankhondo onse a Sisera adaphedwa ndi lupanga. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene adapulumuka.
17
Koma Sisera adathaŵa pansi mpaka kukafika ku hema la Yaele, mkazi wa Hebere, Mkeni uja, pakuti panali mtendere pakati pa Yabini, mfumu ya ku Hazori, ndi banja la Hebere Mkeniyo.
18
Yaele adatuluka kukachingamira Sisera, namuuza kuti, “Loŵani mommuno mbuyanga, loŵani. Musaope kanthu.” Choncho adaloŵa m'hemamo ndipo adamfunditsa bulangete.
19
Siserayo adamuuza mkaziyo kuti, “Pepani ndithu mai, patseniko madzi akumwa pang'ono, ndili ndi ludzu.” Mkaziyo adatsekula thumba lachikopa la mkaka nampatsa kuti amwe, namfunditsanso bulangete.
20
Kenaka adauza mkazi uja kuti, “Mukaime pakhomo pa hema, ndipo munthu aliyense akabwera ndi kukufunsani kuti, ‘Kodi muli munthu m'menemo?’ Mumuuze kuti, Ai, mulibe.”
21
Koma Yaele, mkazi wa Hebere, adakatenga chikhomo cha hema, nakatenganso nyundo m'manja mwake, ndipo adayenda monyang'ama napita kwa Sisera uja. Pamene iyeyo anali m'tulo chifukwa chotopa, mkazi uja adakhomera chikhomo chija m'litsipa mwake. Chidatulukira kwinaku mpaka kuloŵa m'nthaka, iye kufa nkukhala komweko.
22
Pamene Baraki adabwera akulondola Sisera, Yaele adatuluka kukamchingamira, namuuza kuti, “Loŵani, ndikuwonetseni munthu amene mukumfunayo.” Iye adaloŵa m'hema la mkaziyo, ndipo adangoona Sisera ali thasa pansi atafa, chikhomo cha hema chili tototo m'litsipa mwake.
23
Motero tsiku limenelo Mulungu adagonjetsa anthu a Yabini, mfumu ya ku Kanani, pamaso pa Aisraele.
24
Ndipo Aisraele adapanikizabe Yabini, mfumu ya ku Kanani, mpaka kumuwonongeratu.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21