bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 21
Judges 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
1
Aisraele anali atalumbira ku Mizipa kuti, “Palibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene adzapereke mwana wake wamkazi kuti akwatiwe ndi Abenjamini.”
2
Anthuwo adafika ku Betele, nakhala pansi kumeneko pamaso pa Mulungu mpaka madzulo, ndipo adafuula nalira ndi chisoni chambiri.
3
Iwowo ankati, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa chiyani zimenezi zachitika m'dziko la Aisraele, kuti lero fuko la Benjamini lilipafupi kuchotsedwa m'dziko la Israele?”
4
M'maŵa mwake anthuwo adadzuka m'mamaŵa. Adamanga guwa kumeneko, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere.
5
Aisraele adati, “Kodi ndani pakati pa mafuko a Aisraele amene sadafike ku msonkhano wa Chauta?” Paja anali atachita malumbiro aakulu okhudza munthu amene sadapite kwa Chauta ku Mizipa kuti, “Munthu wotero ayenera kuphedwa.”
6
Koma Aisraele adamvera chifundo abale ao a fuko la Benjamini nati, “Fuko limodzi lachotsedwa m'dziko la Israele lero lino.
7
Kodi tidzaŵapezera kuti akazi anthu amene atsaliraŵa, popeza kuti talumbira kwa Chauta kuti sitidzaŵapatsa ana athu aakazi kuti aŵakwatire?”
8
Tsono iwowo adafunsa kuti, “Kodi m'fuko la Aisraele ndani amene sadabwere kwa Chauta ku Mizipa?” Tsono kudapezeka kuti panalibe ndi mmodzi yemwe wa ku Yabesi-Giliyadi amene adabwera ku msonkhano kuzithando kuja.
9
Pakuti m'mene anthu ankasonkhana, adangoona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe wa ku Yabesi-Giliyadi.
10
Choncho mpingo udatumiza kumeneko anthu 12,000 mwa anthu ao, olimba kwambiri, naŵalamula kuti, “Pitani mukaŵaphe anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndi lupanga. Mukaphenso akazi ndi ana omwe.
11
Zimene mukachite ndi izi, ‘Mukaphe amuna onse ndiponso mkazi aliyense amene adadziŵapo kale mwamuna.’ ”
12
Pakati pa anthu a ku Yabesi-Giliyadi adapeza anamwali 400 amene sadadziŵepo amuna. Amenewo adabwera nawo ku zithando ku Silo, mzinda umene uli m'dziko la Kanani.
13
Pamenepo mpingo wonse udatumiza uthenga kwa Abenjamini amene anali ku thanthwe la ku Rimoni kukaŵauza kuti nkhondo yatha.
14
Abenjamini adabwera nthaŵi imeneyo. Ndipo Aisraele adaŵapatsa Abenjaminiwo akazi a ku Yabesi-Giliyadi amene sadaŵaphe aja. Koma adapereŵera, osakwanira.
15
Aisraele adaŵamvera chifundo Abenjaminiwo chifukwa chakuti Chauta anali atachotsako anthu ena mu fuko limodzi la Aisraele.
16
Tsono akuluakulu a mpingo adati, “Kodi tikaŵapezera kuti akazi anthu amene atsaliraŵa, popeza kuti akazi a fuko la Benjamini adaphedwa?”
17
Iwowo adati, “Nkofunika kuti anthu otsalira a fuko la Benjamini akhale nazo zidzukulu, kuti fuko lao lisafafanizike pa mtundu wa Israele.
18
Komabe sitingathe kuŵapatsa ana athu aakazi kuti aŵakwatire.” Paja Aisraele anali atalumbira kuti, “Akhale wotembereredwa munthu amene apatse Mbenjamini mkazi.”
19
Choncho adati, “Paja kuli chikondwerero cha chaka ndi chaka cholemekeza Chauta ku mzinda wa Silo.” Silo ali kumpoto kwa Betele, kuvuma kwa Lebona.
20
Ndiye adalamula Abenjamini aja kuti, “Pitani mukabisale m'minda yamphesa,
21
ndipo muzikapenyetsetsa. Ana aakazi a ku Silo akamakabwera kudzavina magule, pomwepo mutuluke m'minda yamphesa ndi kukaŵagwira, aliyense wake, nkupita nawo ku dziko la Benjamini.
22
Tsono pamene azibambo kapena alongo ao adzabwere kuno kudzadandaula, ife tidzaŵauza kuti, ‘Chonde, tiloleni kuti tiŵatenge, popeza kuti anthuŵa sitidaŵapezere akazi pomenya nkhondo, ndipo inunso simudachita kuŵapatsa akaziwo. Mukadatero bwenzi tsopano mutapalamula.’ ”
23
Abenjaminiwo adachitadi zimenezi. Mwa akazi amene ankavina aja adatengapo ao, molingana ndi chiŵerengero chao, napita nawo. Kenaka adanyamuka kubwerera ku dziko lakwao nakamanganso mizinda yatsopano ndi kumakhalamo.
24
Tsono Aisraele adachoka kumeneko nthaŵi yomweyo, napita aliyense ku fuko lake ndiponso ku banja lake, ndipo kuchokera kumeneko aliyense adapita ku dera la choloŵa chake.
25
Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israele. Munthu aliyense ankangochita zimene zinkakomera mwiniwakeyo.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21