bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 6
Judges 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 7 →
1
Aisraele adachitanso zinthu zoipira Chauta, ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Amidiyani zaka zisanu ndi ziŵiri.
2
Amidiyani anali amphamvu ndi oopsa kupambana Aisraele. Nchifukwa chake Aisraele ankakumba malo obisalamo m'mapiri ndiponso m'mapanga, namanganso malinga ao.
3
Aisraele ankati akabzala mbeu, Amidiyani ndi Aamaleke pamodzi ndi anthu akuvuma, ankabwera kudzaŵathira nkhondo.
4
Ankamanga zithando zao moyang'anana ndi Aisraele, ndi kuwononga zokolola zao zonse mpaka ku Gaza, osaŵasiyirako Aisraelewo chakudya chilichonse, nkhosa, ng'ombe kapenanso bulu.
5
Iwo Amidiyani ankabwera ndi ng'ombe zao zomwe pamodzi ndi mahema ao. Ankabwera ambiri ngati dzombe. Kunali kosatheka kuŵaŵerenga anthuwo ndi ngamira zao. Ankaononga dzikolo pamene ankabwera.
6
Motero Amidiyani adalulutsa dziko la Israele kwambiri. Ndipo Aisraele adalira kwa Chauta kuti aŵathandize.
7
Pamene Aisraele adalira kwa Chauta chifukwa cha Amidiyaniwo,
8
Chautayo adaŵatumizira mneneri. Ndipo iye adaŵauza kuti, “Zimene Chauta, Mulungu wa Israele, wanena ndi izi, ‘Ndine amene ndidakutsogolerani kuchokera ku Ejipito, nkukutulutsani m'dziko laukapolo.
9
Ndidakupulumutsani kwa Aejipito ndiponso kwa onse amene ankakuzunzani. Ndidakupirikitsirani adani anu inu mulikufika, ndi kukupatsani dziko lao.
10
Ndidakuuzani kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, musapembedze milungu ya Aamori amene mukukhala m'dziko lao, koma inu simudasamale mau anga.’ ”
11
Tsiku lina mngelo wa Chauta adabwera ku Ofura ndi kukhala pansi patsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yoasi Mwabiyezere. Nthaŵiyo nkuti Gideoni, mwana wake, akupuntha tirigu, atabisala m'nyumba yofinyira mphesa, kuti Amidiyani asamuwone tiriguyo.
12
Apo mngelo wa Chauta uja adamuwonekera namuuza kuti, “Chauta ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.”
13
Gideoni adauza mngeloyo kuti, “Pepani mbuyanga, ngati Chauta ali nafe, chifukwa chiyani tsono zonsezi zatigwera? Nanga zili kuti ntchito zake zonse zodabwitsa zimene makolo athu ankatisimbira zakuti ati Chauta adatitulutsa ku dziko la Ejipito? Koma tsopano watitaya, ndipo watipereka kwa Amidiyani.”
14
Chauta adamlamula kuti, “Pita ndi mphamvu zakozi, ukapulumutse Aisraele kwa Amidiyani. Nanga kodi sindine amene ndikukutuma?”
15
Apo Gideoni adayankha kuti, “Inu Chauta, ndapota nanu, kodi ndingathe bwanji kupulumutsa Aisraele? Onani, mbumba yanga ndiye yofooka kwambiri m'fuko la Manase, ndipo m'banja mwa bambo wanga, wamng'ono koposa ndine.”
16
Chauta adamuuza kuti, “Koma Ine ndidzakhala nawe, ndipo udzaŵagonjetsa Amidiyani onse ngati munthu mmodzi.”
17
Tsono Gideoni adati, “Ngati tsopano mwandikomera mtima, onetseni chizindikiro chosonyeza kuti ndinudi Chauta amene mukulankhula nane.
18
Musachoke pano, ndapota nanu, mpaka nditabwerera kwa inu kudzakutulirani chopereka cha chakudya.” Apo Chauta adati, “Chabwino, ndikudikira mpaka utabwerera.”
19
Tsono Gideoni adakaloŵa m'nyumba mwake, nakakonza mwanawambuzi, naphika makeke osatupitsa a ufa wa makilogramu khumi. Nyamayo adaiika m'dengu ndipo msuzi wake adauthira mu mphika, nabwera nazo zonsezo kudzazipereka kwa mngelo uja patsinde pa mtengo wa thundu paja.
20
Mngelo wa Mulunguyo adamuuza kuti, “Tenga nyamayi pamodzi ndi makekeŵa, uziike pathanthwepo, ndi kuthira msuzi pamwamba pake.” Gideoni adachitadi zimenezo.
21
Tsono mngelo wa Chauta adatenga ndodo m'manja mwake nakhudza nayo nyama ija ndi makeke aja. Pompo padabuka moto pathanthwepo ndi kupsereza nyamayo pamodzi ndi makeke aja. Basi mngelo wa Chauta adazimirira osaonekanso.
22
Apo Gideoni adazindikira kuti analidi mngelo wa Chauta, ndipo adati, “Kalanga ine, Chauta Wamphamvuzonse! Ndaona mngelo wa Chauta ndi maso.”
23
Koma Chauta adamuuza kuti, “Mtendere ukhale nawe. Usaope, suufa,”
24
Tsono Gideoni adamangira Chauta guwa pa malo omwewo ndipo adalitcha dzina loti “Chauta ndiye mtendere.” Guwalo lili ku Ofura, mzinda wa Aabiyezere, mpaka lero lino.
25
Usiku umenewo Chauta adauza Gideoni kuti, “Utenge ng'ombe yamphongo ya bambo wako, ng'ombe ina yachiŵiri, ya zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo ugwetse guwa la Baala limene bambo wako ali nalo, ndi kugwetsanso fano la Asera limene lili pambali pake.
26
Kenaka pamwamba pa linga pano umange ndi miyala yoyala bwino guwa la Chauta, Mulungu wako. Tsono utenge ng'ombe yamphongo yachiŵiri ija ndi kuipereka kuti ikhale nsembe yopsereza, pogwiritsa ntchito mtengo wa fano la Asera limene udule ngati nkhunilo.”
27
Choncho Gideoni adatenga anthu khumi mwa atumiki ake, ndipo adachitadi monga momwe Chauta adaamuuzira. Koma popeza kuti ankaopa kwambiri a m'banja la bambo wake ndiponso anthu am'mudzimo, sadachite zimenezo masana, adachita usiku.
28
Pamene anthu am'mudzimo adadzuka m'mamaŵa, adangoona guwa la Baala litagwetsedwa, fano la Asera limene linali pambali pake litadulidwa, ndipo ng'ombe yamphongo yachiŵiri ija itaperekedwa nsembe pa guwa adaamangalo.
29
Ndiye adayamba kufunsana kuti, “Wachita zimenezi ndani?” Atafufuza ndi kufunsafunsa, adati, “Gideoni, mwana wa Yoasi, ndiye amene wachita zimenezi.”
30
Pomwepo anthu am'mudzimo adauza Yoasi kuti, “Mutulutse mwana wako. Ayenera kufa popeza kuti wagwetsa guwa la Baala, ndipo wadula fano la Asera limene linali pambali pake pa guwalo.”
31
Koma onse amene adamuukirawo, Yoasi adaŵauza kuti, “Kodi inu ndinu amene mukuti mummenyere nkhondo Baala? Kodi ndinu amene mukuti mumtchinjirize? Aliyense amene amenyere Baala nkhondo, aphedwa maŵa m'maŵa. Ngati iye ndi mulungudi, adzimenyere nkhondo yekha, popeza kuti guwa lake lagwetsedwa.”
32
Nchifukwa chake pa tsiku limenelo Gideoni adatchedwa Yerubaala, ndiye kuti, “Baala alimbane naye,” poti adaagwetsa guwa lake.
33
Tsono Amidiyani ndi Aamaleke onse, pamodzi ndi anthu onse akuvuma, adasonkhana, ndipo ataoloka Yordani, adakamanga zithando zankhondo m'chigwa cha Yezireele.
34
Koma Mzimu wa Chauta udaloŵa mwa Gideoni. Choncho Gideoniyo adaimba lipenga, ndipo Aabiyezere aja adaitanidwa kuti amtsate.
35
Adatuma amithenga m'dziko lonse la Manase, nawonso Amanasewo adaitanidwa kuti amtsate. Adatumanso amithenga kwa Aasere, Azebuloni ndiponso Anafutali. Onsewo adapita kukaŵachingamira.
36
Gideoni adalankhula ndi Mulungu nati, “Ngati mukuti mupulumutse Aisraele ndi dzanja langa, monga momwe mwaneneramu,
37
chabwino, tsono ine ndikuyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Mame akangogwa pa ubweya wankhosa pokhapo, koma panthaka nkukhala pouma, apo ndidziŵa kuti Inu mudzapulumutsadi Aisraele kudzera mwa ine, monga momwe mudanenera.”
38
Ndipo zidachitikadi choncho. Pamene adadzuka m'mamaŵa ndi kuufinya ubweya uja, adafinya madzi odzaza mkhate.
39
Tsono Gideoni adalankhulanso ndi Mulungu nati, “Musandipsere mtima, mundilole ndilankhulenso kamodzi kokhaka. Ndapota nanu, mulole kuti paubweya pokhapa pakhale pouma koma panthaka ponsepa pagwe mame.”
40
Mulungu adachitadi momwemo usiku umenewo, mwakuti paubweya pokha panali pouma, koma panthaka ponse padagwa mame.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21